< 撒母耳记上 25 >
1 撒母耳死了,以色列众人聚集,为他哀哭,将他葬在拉玛—他自己的坟墓里。 大卫起身,下到巴兰的旷野。
Samueli anamwalira, ndipo Aisraeli onse anasonkhana kudzalira maliro ake ndipo anamuyika mʼmanda ku mudzi kwawo ku Rama. Ndipo Davide anapita ku chipululu cha Parani.
2 在玛云有一个人,他的产业在迦密,是一个大富户,有三千绵羊,一千山羊;他正在迦密剪羊毛。
Kunali munthu wina wolemera kwambiri ku Maoni amene malo ake a ntchito anali ku Karimeli. Iyeyu anali ndi mbuzi 1,000 ndi nkhosa 3,000.
3 那人名叫拿八,是迦勒族的人;他的妻名叫亚比该,是聪明俊美的妇人。拿八为人刚愎凶恶。
Dzina lake linali Nabala ndipo anali wa fuko la Kalebe. Dzina la mkazi wake linali Abigayeli. Anali mkazi wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wake, wa banja la Kalebe, anali wowuma mtima ndi wamwano pa zochita zake.
Davide anamva akanali ku chipululu kuti Nabala akumeta nkhosa.
5 大卫就打发十个仆人,吩咐他们说:“你们上迦密去见拿八,提我的名问他安。
Choncho anatuma anyamata khumi nawawuza kuti, “Pitani kwa Nabala ku Karimeli ndipo mukamulonjere mʼdzina langa.
6 要对那富户如此说:‘愿你平安,愿你家平安,愿你一切所有的都平安。
Mukamuwuze kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu, banja lanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo.
7 现在我听说有人为你剪羊毛,你的牧人在迦密的时候和我们在一处,我们没有欺负他们,他们也未曾失落什么。
“‘Tsono ndamva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitinawachite china chilichonse choyipa, ndipo sanasowe kanthu pa nthawi yonse imene anali ku Karimeli.
8 可以问你的仆人,他们必告诉你。所以愿我的仆人在你眼前蒙恩,因为是在好日子来的。求你随手取点赐与仆人和你儿子大卫。’”
Muwafunse antchito anu ndipo akuwuzani. Kotero akomereni mtima anyamata anga, pakuti tabwera pa nthawi yachikondwerero. Chonde apatseniko antchito anuwo ndi mwana wanu Davide chilichonse chimene mungakhale nacho.’”
9 大卫的仆人到了,将这话提大卫的名都告诉了拿八,就住了口。
Anyamata a Davide aja atafika, anamuwuza Nabala zonse zimene Davide anayankhula. Ndipo anadikira yankho.
10 拿八回答大卫的仆人说:“大卫是谁?耶西的儿子是谁?近来悖逆主人奔逃的仆人甚多,
Nabala anayankha anyamata a Davide kuti, “Kodi Davide ndi ndani? Mwana wa Yese ndi ndani? Masiku ano pali antchito ambiri amene akuthawa kwa mabwana awo.
11 我岂可将饮食和为我剪羊毛人所宰的肉给我不知道从哪里来的人呢?”
Nditengerenji buledi, madzi ndi nyama zimene ndaphera anthu anga ometa nkhosa ndi kuzipereka kwa anthu amene sindikudziwa kumene achokera?”
12 大卫的仆人就转身从原路回去,照这话告诉大卫。
Choncho anyamata a Davide aja anatembenuka nabwerera. Atafika anafotokozera Davide mawu onse a Nabala.
13 大卫向跟随他的人说:“你们各人都要带上刀!”众人就都带上刀,大卫也带上刀。跟随大卫上去的约有四百人,留下二百人看守器具。
Davide anawuza anthu ake kuti, “Aliyense amangirire lupanga lake!” Choncho aliyense anamangirira lupanga lake. Davidenso anamangirira lupanga lake. Anthu pafupifupi 400 ndiwo anapita ndi Davide, pamene anthu 200 anatsala ndi katundu.
14 有拿八的一个仆人告诉拿八的妻亚比该说:“大卫从旷野打发使者来问我主人的安,主人却辱骂他们。
Tsono mmodzi mwa antchito anawuza Abigayeli mkazi wa Nabala kuti, “Davide anatumiza amithenga kuchokera ku chipululu kudzalonjera mbuye wathu, koma iye anawalalatira.
15 但是那些人待我们甚好;我们在田野与他们来往的时候,没有受他们的欺负,也未曾失落什么。
Komatu anthuwa anatichitira zabwino kwambiri. Sanatizunze, ndipo nthawi yonse imene tinali nawo ku busa sitinasowe kanthu.
16 我们在他们那里牧羊的时候,他们昼夜作我们的保障。
Ankatitchinjiriza ngati mpanda usiku ndi usana nthawi yonse tinkaweta nkhosa.
17 所以你当筹划,看怎样行才好;不然,祸患定要临到我主人和他全家。他性情凶暴,无人敢与他说话。”
Tsono onani chimene mungachite, chifukwa zimenezi zingadzetse tsoka pa mbuye wathu pamodzi ndi nyumba yake. Paja mbuye athu aja ndi munthu wa khalidwe loyipa moti palibe amene angathe kuyankhula naye.”
18 亚比该急忙将二百饼,两皮袋酒,五只收拾好了的羊,五细亚烘好了的穗子,一百葡萄饼,二百无花果饼,都驮在驴上,
Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu.
19 对仆人说:“你们前头走,我随着你们去。”这事她却没有告诉丈夫拿八。
Kenaka anawuza antchito ake kuti, “Tsogolani, ine ndikutsatirani.” Koma sanawuze mwamuna wake Nabala.
20 亚比该骑着驴,正下山坡,见大卫和跟随他的人从对面下来,亚比该就迎接他们。
Mayi uja atakwera pa bulu wake ndi kufika pa tsinde la phiri, anangoona Davide ndi ankhondo ake akubwera kunali iye. Choncho anakumana nawo.
21 大卫曾说:“我在旷野为那人看守所有的,以致他一样不失落,实在是徒然了!他向我以恶报善。
Nthawiyi nʼkuti Davide atanena kuti, “Kani ndinalondera pachabe katundu wa munthu uyu mʼchipululu muja! Ndipotu palibe kanthu nʼkamodzi komwe kake kamene kanasowa. Tsono wandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino.
22 凡属拿八的男丁,我若留一个到明日早晨,愿 神重重降罚与我!”
Mulungu andilange kwambiri ngati pofika mmawa nditakhale nditasiyako ngakhale munthu mmodzi mwa onse amene ali nawo.”
23 亚比该见大卫,便急忙下驴,在大卫面前脸伏于地叩拜,
Abigayeli ataona Davide, anatsika pa bulu wake mofulumira ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pa Davide.
24 俯伏在大卫的脚前,说:“我主啊,愿这罪归我!求你容婢女向你进言,更求你听婢女的话。
Ali chigonere choncho pa mapazi a Davide anati, “Mbuye wanga, kulakwa kukhale pa ine ndekha. Chonde lolani kuti mdzakazi wanune ndiyankhule nanu, ndipo mumve mawu a ine mdzakazi wanu.
25 我主不要理这坏人拿八,他的性情与他的名相称;他名叫拿八,他为人果然愚顽。但我主所打发的仆人,婢女并没有看见。
Mbuye wanga musasamale za mwamuna wanga Nabala, munthu wa khalidwe loyipa. Iyeyu ali monga dzina lake liliri. Monga dzina lake litanthauza kuti chitsiru, ndiye kuti zake zonse ndi zauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindinawaone anthu amene mbuye wanga munawatuma.
26 我主啊,耶和华既然阻止你亲手报仇,取流血的罪,所以我指着永生的耶和华、又敢在你面前起誓说:‘愿你的仇敌和谋害你的人都像拿八一样。’
Tsono mbuye wanga muli apa, ndikulumbira pali Yehova wamoyo amene wakuletsani kuti musakhetse magazi a munthu ndi kulipsira nokha, kuti adani anu amene afuna kukuchitani zoyipa adzakhale ngati Nabala.
Choncho, nazi mphatso zimene mdzakazi wanu ndabwera nazo kwa mbuye wanga kuti zipatsidwe kwa anyamata amene muli nawo.
28 求你饶恕婢女的罪过。耶和华必为我主建立坚固的家,因我主为耶和华争战;并且在你平生的日子查不出有什么过来。
Chonde khululukani zolakwa za ine mdzakazi wanu. Ndithu Yehova adzakhazikitsa banja la mbuye wanga mu ufumu, popeza mukumenya nkhondo ya Yehova. Choncho choyipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu.
29 虽有人起来追逼你,寻索你的性命,你的性命却在耶和华—你的 神那里蒙保护,如包裹宝器一样;你仇敌的性命,耶和华必抛去,如用机弦甩石一样。
Ngati munthu wina akuwukirani ndi kukulondani, Yehova Mulungu wanu adzateteza moyo wa mbuye wanga monga mmene munthu asungira chuma mʼphukusi, koma moyo wa adani anu adzawutaya kutali monga momwe munthu amaponyera mwala ndi legeni.
30 我主现在若不亲手报仇流无辜人的血,到了耶和华照所应许你的话赐福与你,立你作以色列的王,那时我主必不至心里不安,觉得良心有亏。耶和华赐福与我主的时候,求你记念婢女。”
Yehova adzakuchitirani mbuye wanga zabwino zonse zimene anakulonjezani. Adzakuyikani kukhala wolamulira Aisraeli.
Zikadzatero, inu mbuye wanga simudzakhala ndi chikumbumtima choti munakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Koma Yehova akadzakuchitirani zabwino zonsezi musadzandiyiwale ine mdzakazi wanu.”
32 大卫对亚比该说:“耶和华—以色列的 神是应当称颂的,因为他今日使你来迎接我。
Tsono Davide anawuza Abigayeli kuti, “Alemekezeke Yehova Mulungu wa Israeli, amene wakutuma iwe lero kuti ukumane nane.
33 你和你的见识也当称赞;因为你今日拦阻我亲手报仇、流人的血。
Yehova akudalitseni chifukwa cha nzeru zanu pondiletsa lero kuti ndisakhetse magazi ndi kubwezera adani anga ndi manja anga.
34 我指着阻止我加害于你的耶和华—以色列永生的 神起誓,你若不速速地来迎接我,到明日早晨,凡属拿八的男丁必定不留一个。”
Kunena zoona, pali Yehova Wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene wandiletsa kuti ndisakupwetekeni, mukanapanda kubwera msanga kudzakumana nane, palibe munthu aliyense wamwamuna wa Nabala akanasiyidwa wamoyo pakucha mmawa.”
35 大卫受了亚比该送来的礼物,就对她说:“我听了你的话,准了你的情面,你可以平平安安地回家吧!”
Ndipo Davide analandira kwa mayiyo zimene anamutengera ndipo anati, “Pitani kwanu mu mtendere. Ine ndamva mawu anu ndipo ndavomera zimene mwapempha.”
36 亚比该到拿八那里,见他在家里设摆筵席,如同王的筵席;拿八快乐大醉。亚比该无论大小事都没有告诉他,就等到次日早晨。
Abigayeli atabwerera kwa Nabala anamupeza ali mʼnyumba akuchita mphwando ngati la mfumu. Iye anali atakondwa kwambiri popeza anali ataledzera kwambiri. Choncho mkazi wakeyo sanamuwuze kalikonse mpaka mmawa kutacha.
37 到了早晨,拿八醒了酒,他的妻将这些事都告诉他,他就魂不附体,身僵如石头一般。
Tsono mmawa, mowa utamuchoka Nabala, mkazi wake anamuwuza zonse. Pomwepo mtima wake unaleka kugunda ndipo unawuma gwaa ngati mwala.
Patapita masiku khumi, Yehova anakantha Nabala ndipo anafa.
39 大卫听见拿八死了,就说:“应当称颂耶和华,因他伸了拿八羞辱我的冤,又阻止仆人行恶;也使拿八的恶归到拿八的头上。”于是大卫打发人去,与亚比该说,要娶她为妻。
Pamene Davide anamva kuti Nabala wamwalira, iye anati, “Alemekezeke Yehova, walipsira Nabala chipongwe chimene anandichita ndipo anandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choyipa. Yehova wabwezera pamutu pa Nabala choyipa chimene iye anachita.” Kenaka Davide anatumiza mawu kwa Abigayeli, kumupempha kuti akhale mkazi wake.
40 大卫的仆人到了迦密见亚比该,对她说:“大卫打发我们来见你,想要娶你为妻。”
Anyamata a Davide atafika ku Karimeli anawuza Abigayeli kuti, “Davide watituma kwa iwe kuti tikutenge ukhale mkazi wake.”
41 亚比该就起来,俯伏在地,说:“我情愿作婢女,洗我主仆人的脚。”
Abigayeli anagwada nagunditsa nkhope yake pansi ndipo anati, “Ine mdzakazi wa mbuye wanga ndakonzeka kutumikira ngakhale kusambitsa mapazi a anyamata ake.”
42 亚比该立刻起身,骑上驴,带着五个使女,跟从大卫的使者去了,就作了大卫的妻。
Motero Abigayeli ananyamuka mofulumira nakwera bulu wake. Tsono iye pamodzi ndi anamwali ake asanu amene ankamutumikira, anatsagana ndi amithenga a Davide aja ndipo anakakhala mkazi wake wa Davide.
43 大卫先娶了耶斯列人亚希暖,她们二人都作了他的妻。
Davide nʼkuti atakwatiranso Ahinoamu wa ku Yezireeli ndipo onse awiri anali akazi ake.
44 扫罗已将他的女儿米甲,就是大卫的妻,给了迦琳人拉亿的儿子帕提为妻。
Koma Sauli anali atakwatitsa Mikala, mkazi wa Davide kwa Paliti mwana wa Laisi wa ku Galimu.