< 列王纪上 9 >

1 所罗门建造耶和华殿和王宫,并一切所愿意建造的都完毕了,
Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene ankafuna,
2 耶和华就二次向所罗门显现,如先前在基遍向他显现一样,
Yehova anamuonekera kachiwiri, monga momwe anamuonekera ku Gibiyoni.
3 对他说:“你向我所祷告祈求的,我都应允了。我已将你所建的这殿分别为圣,使我的名永远在其中;我的眼、我的心也必常在那里。
Yehova ananena kwa iye kuti: “Ndamva pemphero ndi pembedzero lako pa zimene wapempha pamaso panga. Ndayipatula Nyumba iyi, imene wamanga, poyikamo Dzina langa mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepo nthawi zonse.
4 你若效法你父大卫,存诚实正直的心行在我面前,遵行我一切所吩咐你的,谨守我的律例典章,
“Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika, mwangwiro ndi moona mtima monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga,
5 我就必坚固你的国位在以色列中,直到永远,正如我应许你父大卫说:‘你的子孙必不断人坐以色列的国位。’
Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu pa Israeli mpaka muyaya, monga ndinalonjezera abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu pa mpando waufumu wa Israeli.’
6 倘若你们和你们的子孙转去不跟从我,不守我指示你们的诫命律例,去事奉敬拜别神,
“Koma ngati iwe kapena ana ako mudzapatuka ndi kuleka kusunga malamulo ndi mawu anga amene ndakupatsani ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza,
7 我就必将以色列人从我赐给他们的地上剪除,并且我为己名所分别为圣的殿也必舍弃不顾,使以色列人在万民中作笑谈,被讥诮。
pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko limene ndinawapatsa ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndayipatula chifukwa cha Dzina langa. Pamenepo Aisraeli adzasanduka mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse.
8 这殿虽然甚高,将来经过的人必惊讶、嗤笑,说:‘耶和华为何向这地和这殿如此行呢?’
Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzatsonya ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’
9 人必回答说:‘是因此地的人离弃领他们列祖出埃及地之耶和华—他们的 神,去亲近别神,事奉敬拜他,所以耶和华使这一切灾祸临到他们。’”
Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Igupto, ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’”
10 所罗门建造耶和华殿和王宫,这两所二十年才完毕了。
Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga nyumba ziwirizi: Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu,
11 泰尔王希兰曾照所罗门所要的,资助他香柏木、松木,和金子;所罗门王就把加利利地的二十座城给了希兰。
Mfumu Solomoni anapereka mizinda makumi awiri ya ku Galileya kwa Hiramu mfumu ya ku Turo chifukwa Hiramu nʼkuti atapereka mitengo yonse ya mkungudza ndi ya payini ndiponso golide yense zimene Solomoni ankazifuna.
12 希兰从泰尔出来,察看所罗门给他的城邑,就不喜悦,
Koma Hiramu atabwera kuchokera ku Turo kudzaona mizinda imene Solomoni anamupatsa, sanasangalatsidwe nayo mizindayo.
13 说:“我兄啊,你给我的是什么城邑呢?”他就给这城邑之地起名叫迦步勒,直到今日。
Iye anafunsa kuti, “Mʼbale wanga, kodi iyi nʼkukhala mizinda yondipatsa?” Ndipo iye anayitcha mizindayo Dziko la Kabuli, dzina lomwe amatchedwa mpaka lero lino.
14 希兰给所罗门一百二十他连得金子。
Koma Hiramu anali atatumiza kwa mfumu golide oposa makilogalamu 4,000.
15 所罗门王挑取服苦的人,是为建造耶和华的殿、自己的宫、米罗、耶路撒冷的城墙、夏琐、米吉多,并基 色。
Izi ndi zimene anachita Mfumu Solomoni: Analamula anthu kuti agwire ntchito yathangata pomanga Nyumba ya Yehova, nyumba yake, malo achitetezo a Milo, mpanda wa Yerusalemu, Hazori, Megido ndi Gezeri.
16 先前埃及王法老上来攻取基色,用火焚烧,杀了城内居住的迦南人,将城赐给他女儿所罗门的妻作妆奁。
(Farao mfumu ya ku Igupto inali itathira nkhondo ndi kulanda Gezeri. Iye anatentha mzindawo. Anapha Akanaani amene ankakhala mʼmenemo ndipo kenaka anawupereka ngati mphatso yaukwati kwa mwana wake wamkazi amene anakwatiwa ndi Solomoni.
17 所罗门建造基色、下伯·和 、
Ndipo Solomoni anamanganso Gezeri.) Iye anamanga Beti-Horoni Wakumunsi,
18 巴拉,并国中旷野里的达莫,
Baalati ndi Tadimori ku chipululu, mʼdziko lake lomwelo,
19 又建造所有的积货城,并屯车和马兵的城,与耶路撒冷、黎巴嫩,以及自己治理的全国中所愿建造的。
pamodzinso ndi mizinda yake yosungira chuma ndiponso mizinda yosungiramo magaleta ndi akavalo ake. Anamanganso chilichonse chimene anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.
20 至于国中所剩下不属以色列人的亚摩利人、赫人、比利洗人、希未人、耶布斯人,
Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli).
21 就是以色列人不能灭尽的,所罗门挑取他们的后裔作服苦的奴仆,直到今日。
Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino.
22 惟有以色列人,所罗门不使他们作奴仆,乃是作他的战士、臣仆、统领、军长、车兵长、马兵长。
Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Mwisraeli aliyense; iwo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri a ankhondo, akapitawo ake, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake.
23 所罗门有五百五十督工的,监管工人。
Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za Solomoni. Anthu okwana 550 ndiwo ankayangʼanira anthu amene ankagwira ntchitowo.
24 法老的女儿从大卫城搬到所罗门为她建造的宫里。那时,所罗门才建造米罗。
Mwana wamkazi wa Farao atachoka mu Mzinda wa Davide, kupita ku nyumba ya mfumu imene Solomoni anamumangira, Solomoni anamanga malo achitetezo a Milo.
25 所罗门每年三次在他为耶和华所筑的坛上献燔祭和平安祭,又在耶和华面前的坛上烧香。这样,他建造殿的工程完毕了。
Katatu pa chaka Solomoni ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe limene anamangira Yehova ndiponso ankafukiza lubani pamaso pa Yehova. Potero ankakwaniritsa zoyenera kuchitika mu Nyumba ya Yehova.
26 所罗门王在以东地红海边,靠近以禄的以旬·迦别制造船只。
Mfumu Solomoni anapanganso sitima zapamadzi ku Ezioni Geberi, malo amene ali pafupi ndi Eloti ku Edomu, mʼmbali mwa Nyanja Yofiira.
27 希兰差遣他的仆人,就是熟悉泛海的船家,与所罗门的仆人一同坐船航海。
Ndipo Hiramu anatumiza anthu ake oyendetsa sitima zapamadzi amene ankadziwa za pa nyanja kuti aziyendetsa pamodzi ndi anthu a Solomoni.
28 他们到了俄斐,从那里得了四百二十他连得金子,运到所罗门王那里。
Iwo anapita ku Ofiri ndipo anakatenga golide okwana makilogalamu 14,000, amene anamupereka kwa Mfumu Solomoni.

< 列王纪上 9 >