< 哥林多前书 1 >
1 奉 神旨意,蒙召作耶稣基督使徒的保罗,同兄弟所提尼,
Paulo, woyitanidwa mwachifuniro cha Mulungu kuti akhale mtumwi wa Khristu Yesu ndi mʼbale wathu Sositene.
2 写信给在哥林多 神的教会,就是在基督耶稣里成圣、蒙召作圣徒的,以及所有在各处求告我主耶稣基督之名的人。基督是他们的主,也是我们的主。
Kupita ku mpingo wa Mulungu ku Korinto, kwa oyeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi oyitanidwa kukhala opatulika ndiponso kwa onse amene amapemphera mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu mʼdziko lonse lapansi, amene ndi Ambuye wawo ndi wathunso.
3 愿恩惠、平安从 神我们的父并主耶稣基督归与你们。
Landirani chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu.
4 我常为你们感谢我的 神,因 神在基督耶稣里所赐给你们的恩惠;
Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu chifukwa cha chisomo chake chopatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu.
Pakuti mwa Iye mwalemekezedwa mʼnjira iliyonse, mʼkuyankhula kwanu konse ndi mʼkudziwa kwanu konse,
chifukwa umboni wathu pa za Khristu unatsimikizidwa mwa inu.
7 以致你们在恩赐上没有一样不及人的,等候我们的主耶稣基督显现。
Choncho inu simusowa mphatso yauzimu iliyonse pamene mukudikira mofunitsitsa kuti Ambuye athu Yesu Khristu avumbulutsidwe.
8 他也必坚固你们到底,叫你们在我们主耶稣基督的日子无可责备。
Adzakulimbikitsani mpaka kumapeto kuti mudzakhale wopanda mlandu pa tsiku lobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
9 神是信实的,你们原是被他所召,好与他儿子—我们的主耶稣基督一同得分。
Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika.
10 弟兄们,我借我们主耶稣基督的名劝你们都说一样的话。你们中间也不可分党,只要一心一意,彼此相合。
Ndidandaulira inu, abale, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu kuti nonsenu muvomerezane wina ndi mnzake kuti pasakhale kugawikana pakati panu ndi kuti mukhale amodzi kwenikweni mu nzeru ndi mʼmaganizo.
11 因为革来氏家里的人曾对我提起弟兄们来,说你们中间有纷争。
Abale anga, ena a ku nyumba ya Kloe andidziwitsa kuti pali mkangano pakati panu.
12 我的意思就是你们各人说:“我是属保罗的”;“我是属亚波罗的”;“我是属矶法的”;“我是属基督的”。
Chimene ndikutanthauza ndi ichi: wina amati, “Ndimatsatira Paulo,” wina, “Ndimatsatira Apolo,” wina, “Ndimatsatira Kefa,” winanso, “Ndimatsatira Khristu.”
13 基督是分开的吗?保罗为你们钉了十字架吗?你们是奉保罗的名受了洗吗?
Kodi Khristu wagawikana? Kodi Paulo anapachikidwa pa mtanda chifukwa cha inu? Kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo?
14 我感谢 神,除了基利司布并该犹以外,我没有给你们一个人施洗,
Ine ndikuyamika kuti sindinabatizepo mmodzi mwa inu kupatula Krispo ndi Gayo,
mwakuti palibe amene anganene kuti anabatizidwa mʼdzina langa.
16 我也给司提反家施过洗,此外给别人施洗没有,我却记不清。
(Inde, ine ndinabatizanso a mʼbanja la Stefano, koma sindikumbukira ngati ndinabatizanso wina aliyense).
17 基督差遣我,原不是为施洗,乃是为传福音,并不用智慧的言语,免得基督的十字架落了空。
Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu.
18 因为十字架的道理,在那灭亡的人为愚拙;在我们得救的人,却为 神的大能。
Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu.
19 就如经上所记: 我要灭绝智慧人的智慧, 废弃聪明人的聪明。
Pakuti kwalembedwa kuti, “Ine ndidzawononga nzeru za anthu anzeru; luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
20 智慧人在哪里?文士在哪里?这世上的辩士在哪里? 神岂不是叫这世上的智慧变成愚拙吗? (aiōn )
Munthu wanzeru ali kuti? Munthu wozama ndi maphunziro ali kuti? Munthu wodziwa zakuya zamakono ali kuti? Kodi Mulungu sanazipusitse nzeru za dziko lapansi? (aiōn )
21 世人凭自己的智慧,既不认识 神, 神就乐意用人所当作愚拙的道理拯救那些信的人;这就是 神的智慧了。
Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira.
Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru,
23 我们却是传钉在十字架的基督,在犹太人为绊脚石,在外邦人为愚拙;
koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina.
24 但在那蒙召的,无论是犹太人、希腊人,基督总为 神的能力, 神的智慧。
Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu.
25 因 神的愚拙总比人智慧, 神的软弱总比人强壮。
Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.
26 弟兄们哪,可见你们蒙召的,按着肉体有智慧的不多,有能力的不多,有尊贵的也不多。
Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero.
27 神却拣选了世上愚拙的,叫有智慧的羞愧;又拣选了世上软弱的,叫那强壮的羞愧。
Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu.
28 神也拣选了世上卑贱的,被人厌恶的,以及那无有的,为要废掉那有的,
Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo,
kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu.
30 但你们得在基督耶稣里是本乎 神, 神又使他成为我们的智慧、公义、圣洁、救赎。
Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.
Choncho poti zinalembedwa kuti, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”