< 历代志上 6 >

1 利未的儿子是革顺、哥辖、米拉利。
Ana a Levi anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
2 哥辖的儿子是暗兰、以斯哈、希伯伦、乌薛。
Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
3 暗兰的儿子是亚伦、摩西,还有女儿米利暗。亚伦的儿子是拿答、亚比户、以利亚撒、以他玛。
Ana a Amramu anali awa: Aaroni, Mose ndi Miriamu. Ana a Aaroni anali awa: Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara
4 以利亚撒生非尼哈;非尼哈生亚比书;
Eliezara anabereka Finehasi, Finehasi anabereka Abisuwa,
5 亚比书生布基;布基生乌西;
Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi.
6 乌西生西拉希雅;西拉希雅生米拉约;
Uzi anabereka Zerahiya, Zerahiya anabereka Merayoti,
7 米拉约生亚玛利雅;亚玛利雅生亚希突;
Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi.
8 亚希突生撒督;撒督生亚希玛斯;
Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Ahimaazi.
9 亚希玛斯生亚撒利雅;亚撒利雅生约哈难;
Ahimaazi anabereka Azariya, Azariya anabereka Yohanani,
10 约哈难生亚撒利雅(这亚撒利雅在所罗门于耶路撒冷所建造的殿中,供祭司的职分);
Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),
11 亚撒利雅生亚玛利雅;亚玛利雅生亚希突;
Azariya anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi,
12 亚希突生撒督;撒督生沙龙;
Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Salumu,
13 沙龙生希勒家;希勒家生亚撒利雅;
Salumu anabereka Hilikiya, Hilikiya anabereka Azariya,
14 亚撒利雅生西莱雅;西莱雅生约萨答。
Azariya anabereka Seraya, ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.
15 当耶和华借尼布甲尼撒的手掳掠犹大和耶路撒冷人的时候,这约萨答也被掳去。
Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.
16 利未的儿子是革顺、哥辖、米拉利。
Ana a Levi anali awa: Geresomu, Kohati ndi Merari.
17 革顺的儿子名叫立尼、示每。
Mayina a ana a Geresomu ndi awa: Libini ndi Simei.
18 哥辖的儿子是暗兰、以斯哈、希伯伦、乌薛。
Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
19 米拉利的儿子是抹利、母示。这是按着利未人宗族分的各家。
Ana a Merari anali awa: Mahili ndi Musi. Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:
20 革顺的儿子是立尼;立尼的儿子是雅哈;雅哈的儿子是薪玛;
Ana a Geresomu ndi awa: Libini, Yehati, Zima,
21 薪玛的儿子是约亚;约亚的儿子是易多;易多的儿子是谢拉;谢拉的儿子是耶特赖。
Yowa, Ido, Zera ndi Yeaterai.
22 哥辖的儿子是亚米拿达;亚米拿达的儿子是可拉;可拉的儿子是亚惜;
Zidzukulu za Kohati ndi izi: Aminadabu, Kora, Asiri,
23 亚惜的儿子是以利加拿;以利加拿的儿子是以比雅撒;以比雅撒的儿子是亚惜;
Elikana, Ebiyasafu, Asiri,
24 亚惜的儿子是他哈;他哈的儿子是乌列;乌列的儿子是乌西雅;乌西雅的儿子是少罗。
Tahati, Urieli, Uziya ndi Sauli.
25 以利加拿的儿子是亚玛赛和亚希摩。
Zidzukulu za Elikana ndi izi: Amasai, Ahimoti,
26 亚希摩的儿子是以利加拿;以利加拿的儿子是琐菲;琐菲的儿子是拿哈;
Elikana, Zofai, Nahati,
27 拿哈的儿子是以利押;以利押的儿子是耶罗罕;耶罗罕的儿子是以利加拿;以利加拿的儿子是撒母耳。
Eliabu, Yerohamu, Elikana ndi Samueli.
28 撒母耳的长子是约珥,次子是亚比亚。
Ana a Samueli ndi awa: Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya.
29 米拉利的儿子是抹利;抹利的儿子是立尼;立尼的儿子是示每;示每的儿子是乌撒;
Zidzukulu za Merari ndi izi: Mahili, Libini, Simei, Uza,
30 乌撒的儿子是示米亚;示米亚的儿子是哈基雅;哈基雅的儿子是亚帅雅。
Simea, Hagiya ndi Asaya.
31 约柜安设之后,大卫派人在耶和华殿中管理歌唱的事。
Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo.
32 他们就在会幕前当歌唱的差,及至所罗门在耶路撒冷建造了耶和华的殿,他们便按着班次供职。
Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.
33 供职的人和他们的子孙记在下面: 哥辖的子孙中有歌唱的希幔。希幔是约珥的儿子;约珥是撒母耳的儿子;
Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa: Ochokera ku banja la Kohati: Hemani, katswiri woyimba, anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,
34 撒母耳是以利加拿的儿子;以利加拿是耶罗罕的儿子;耶罗罕是以列的儿子;以列是陀亚的儿子;
mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Elieli, mwana wa Towa,
35 陀亚是苏弗的儿子;苏弗是以利加拿的儿子;以利加拿是玛哈的儿子;玛哈是亚玛赛的儿子;
mwana wa Zufi, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,
36 亚玛赛是以利加拿的儿子;以利加拿是约珥的儿子;约珥是亚撒利雅的儿子;亚撒利雅是西番雅的儿子;
mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,
37 西番雅是他哈的儿子;他哈是亚惜的儿子;亚惜是以比雅撒的儿子;以比雅撒是可拉的儿子;
mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,
38 可拉是以斯哈的儿子;以斯哈是哥辖的儿子;哥辖是利未的儿子;利未是以色列的儿子。
mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israeli;
39 希幔的族兄亚萨是比利家的儿子,亚萨在希幔右边供职。比利家是示米亚的儿子;
ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja: Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,
40 示米亚是米迦勒的儿子;米迦勒是巴西雅的儿子;巴西雅是玛基雅的儿子;
mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya, mwana wa Malikiya,
41 玛基雅是伊特尼的儿子;伊特尼是谢拉的儿子;谢拉是亚大雅的儿子;
mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya,
42 亚大雅是以探的儿子;以探是薪玛的儿子;薪玛是示每的儿子;
mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana Simei,
43 示每是雅哈的儿子;雅哈是革顺的儿子。革顺是利未的儿子。
mwana wa Yahati, mwana wa Geresomu, mwana wa Levi;
44 他们的族弟兄米拉利的子孙,在他们左边供职的有以探。以探是基示的儿子;基示是亚伯底的儿子;亚伯底是玛鹿的儿子;
ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere: Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki,
45 玛鹿是哈沙比雅的儿子;哈沙比雅是亚玛谢的儿子;亚玛谢是希勒家的儿子;
mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
46 希勒家是暗西的儿子;暗西是巴尼的儿子;巴尼是沙麦的儿子;
mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri,
47 沙麦是末力的儿子;末力是母示的儿子;母示是米拉利的儿子;米拉利是利未的儿子。
mwana wa Mahili, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.
48 他们的族弟兄利未人也被派办 神殿中的一切事。
Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu.
49 亚伦和他的子孙在燔祭坛和香坛上献祭烧香,又在至圣所办理一切的事,为以色列人赎罪,是照 神仆人摩西所吩咐的。
Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.
50 亚伦的儿子是以利亚撒;以利亚撒的儿子是非尼哈;非尼哈的儿子是亚比书;
Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa: Eliezara, Finehasi, Abisuwa,
51 亚比书的儿子是布基;布基的儿子是乌西;乌西的儿子是西拉希雅;
Buki, Uzi, Zerahiya,
52 西拉希雅的儿子是米拉约;米拉约的儿子是亚玛利雅;亚玛利雅的儿子是亚希突;
Merayoti, Amariya, Ahitubi,
53 亚希突的儿子是撒督;撒督的儿子是亚希玛斯。
Zadoki ndi Ahimaazi.
54 他们的住处按着境内的营寨,记在下面:哥辖族亚伦的子孙先拈阄得地,
Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo).
55 在犹大地中得了希伯 和四围的郊野;
Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
56 只是属城的田地和村庄都为耶孚尼的儿子迦勒所得。
Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune.
57 亚伦的子孙得了逃城希伯 ,又得了立拿与其郊野,雅提珥、以实提莫与其郊野;
Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa,
58 希 与其郊野,底璧与其郊野,
Hileni, Debri,
59 亚珊与其郊野,伯·示麦与其郊野。
Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.
60 在便雅悯支派的地中,得了迦巴与其郊野,阿勒篾与其郊野,亚拿突与其郊野。他们诸家所得的城共十三座。
Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13.
61 哥辖族其余的人又拈阄,在玛拿西半支派的地中得了十座城。
Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase.
62 革顺族按着宗族,在以萨迦支派的地中,亚设支派的地中,拿弗他利支派的地中,巴珊内玛拿西支派的地中,得了十三座城。
Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani.
63 米拉利族按着宗族拈阄,在吕便支派的地中,迦得支派的地中,西布伦支派的地中,得了十二座城。
Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
64 以色列人将这些城与其郊野给了利未人。
Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa.
65 这以上录名的城,在犹大、西缅、便雅悯三支派的地中,以色列人拈阄给了他们。
Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina.
66 哥辖族中有几家在以法莲支派的地中也得了城邑,
Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu.
67 在以法莲山地得了逃城示剑与其郊野,又得了基色与其郊野,
Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri,
68 约缅与其郊野,伯·和 与其郊野,
Yokineamu, Beti-Horoni,
69 亚雅 与其郊野,迦特·临门与其郊野。
Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira.
70 哥辖族其余的人在玛拿西半支派的地中得了亚乃与其郊野,比连与其郊野。
Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati.
71 革顺族在玛拿西半支派的地中得了巴珊的哥兰与其郊野,亚斯他录与其郊野;
Ageresomu analandira malo awa: Kuchokera ku theka la fuko la Manase, analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;
72 又在以萨迦支派的地中得了基低斯与其郊野,大比拉与其郊野,
Kuchokera ku fuko la Isakara analandira Kedesi, Daberati,
73 拉末与其郊野,亚年与其郊野;
Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
74 在亚设支派的地中得了玛沙与其郊野,押顿与其郊野,
kuchokera ku fuko la Aseri analandira Masala, Abidoni,
75 户割与其郊野,利合与其郊野;
Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
76 在拿弗他利支派的地中得了加利利的基低斯与其郊野,哈们与其郊野,基列亭与其郊野。
ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.
77 还有米拉利族的人在西布伦支派的地中得了临摩挪与其郊野,他泊与其郊野;
Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa: kuchokera ku fuko la Zebuloni, iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
78 又在耶利哥的约旦河东,在吕便支派的地中得了旷野的比悉与其郊野,雅哈撒与其郊野,
Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko, analandira Bezeri ku chipululu, Yaza,
79 基底莫与其郊野,米法押与其郊野;
Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;
80 又在迦得支派的地中得了基列的拉末与其郊野,玛哈念与其郊野,
ndipo kuchokera ku fuko la Gadi analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu,
81 希实本与其郊野,雅谢与其郊野。
Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.

< 历代志上 6 >