< 历代志上 26 >

1 守门的班次记在下面:可拉族亚萨的子孙中,有可利的儿子米施利米雅。
Magulu a alonda a pa zipata: Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.
2 米施利米雅的长子是撒迦利亚,次子是耶叠,三子是西巴第雅,四子是耶提聂,
Meselemiya anali ndi ana awa: woyamba Zekariya, wachiwiri Yediaeli, wachitatu Zebadiya, wachinayi Yatinieli,
3 五子是以拦,六子是约哈难,七子是以利约乃。
wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani, ndipo wachisanu ndi chiwiri Elihunai.
4 俄别·以东的长子是示玛雅,次子是约萨拔,三子是约亚,四子是沙甲,五子是拿坦业,
Obedi-Edomu analinso ndi ana awa: woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinayi Sakara, wachisanu Netaneli,
5 六子是亚米利,七子是以萨迦,八子是毗乌利太,因为 神赐福与俄别·以东。
wachisanu ndi chimodzi Amieli, wachisanu ndi chiwiri Isakara ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletayi. (Pakuti Mulungu anadalitsa Obedi-Edomu).
6 他的儿子示玛雅有几个儿子,都是大能的壮士,掌管父亲的家。
Mwana wake Semaya analinso ndi ana amene anali atsogoleri mʼbanja la abambo awo chifukwa anali anthu amphamvu.
7 示玛雅的儿子是俄得尼、利法益、俄备得、以利萨巴。以利萨巴的弟兄是壮士,还有以利户和西玛迦。
Ana a Semaya anali: Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi; abale ake, Elihu ndi Semakiya, analinso anthu amphamvu.
8 这都是俄别·以东的子孙,他们和他们的儿子并弟兄,都是善于办事的壮士。俄别·以东的子孙共六十二人。
Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62.
9 米施利米雅的儿子和弟兄都是壮士,共十八人。
Meselemiya anali ndi ana ndi abale ake amene anali aluso ndipo onse analipo 18.
10 米拉利子孙何萨有几个儿子:长子是申利,他原不是长子,是他父亲立他作长子。
Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri),
11 次子是希勒家,三子是底巴利雅,四子是撒迦利亚。何萨的儿子并弟兄共十三人。
wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wachinayi Zekariya. Ana ndi abale onse a Hosa analipo 13.
12 这些人都是守门的班长,与他们的弟兄一同在耶和华殿里按班供职。
Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo.
13 他们无论大小,都按着宗族掣签分守各门。
Iwo anachita maere mwa mabanja awo aangʼono ndi aakulu omwe kuti apeze mlonda pa chipata chilichonse.
14 掣签守东门的是示利米雅;他的儿子撒迦利亚是精明的谋士,掣签守北门。
Maere a chipata chakummwa anagwera Selemiya. Maere anachitikanso chifukwa cha mwana wake Zekariya, phungu wanzeru ndipo maere a chipata chakumpoto anagwera iye.
15 俄别·以东守南门,他的儿子守库房。
Maere a chipata chakummwera anagwera Obedi-Edomu, ndipo maere a nyumba yosungiramo katundu anagwera ana ake.
16 书聘与何萨守西门,在靠近沙利基门、通着往上去的街道上,班与班相对。
Maere a chipata chakumadzulo ndi chipata cha Saleketi ku msewu wa ku mtunda anagwera Supimu ndi Hosa. Mlonda ankayangʼanana ndi mlonda mnzake:
17 每日东门有六个利未人,北门有四个,南门有四个,库房有两个,又有两个轮班替换。
Mbali ya kummawa kunkakhala Alevi 6 pa tsiku, kumpoto anayi pa tsiku, kummwera anayi pa tsiku ndipo awiri ankakhala pa nyumba yosungiramo katundu.
18 在西面街道上有四个,在游廊上有两个。
Ndipo ku bwalo cha kumadzulo, anayi amakhala mu msewu ndi awiri pabwalo penipeni.
19 以上是可拉子孙和米拉利子孙守门的班次。
Awa anali magulu a alonda a pa zipata amene anali zidzukulu za Kora ndi Merari.
20 利未子孙中有亚希雅掌管 神殿的府库和圣物的府库。
Abale awo Alevi, motsogozedwa ndi Ahiya, anali oyangʼanira chuma cha nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Mulungu.
21 革顺族、拉但子孙里,作族长的是革顺族拉但的子孙耶希伊利。
Adzukulu a Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, amene anali atsogoleri a mabanja a Ageresoni, anali awa: Yehieli,
22 耶希伊利的儿子西坦和他兄弟约珥掌管耶和华殿里的府库。
ana a Yehieli, Zetamu ndi mʼbale wake Yoweli. Iwo amayangʼanira chuma cha ku Nyumba ya Mulungu wa Yehova.
23 暗兰族、以斯哈族、希伯伦族、乌泄族也有职分。
Kuchokera ku banja la Amramu, banja la Aizihara, banja la Ahebroni ndi banja la Auzieli:
24 摩西的孙子、革舜的儿子细布业掌管府库。
Subaeli, chidzukulu cha Geresomu, mwana wa Mose, anali mkulu woyangʼanira chuma.
25 还有他的弟兄以利以谢。以利以谢的儿子是利哈比雅;利哈比雅的儿子是耶筛亚;耶筛亚的儿子是约兰;约兰的儿子是细基利;细基利的儿子是示罗密。
Abale ake obadwa mwa Eliezara, anali Rekabiya mwana wake, Yesaya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake ndi Selomiti mwana wake.
26 这示罗密和他的弟兄掌管府库的圣物,就是大卫王和众族长、千夫长、百夫长,并军长所分别为圣的物。
Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena.
27 他们将争战时所夺的财物分别为圣,以备修造耶和华的殿。
Zina zofunkha ku nkhondo anazipereka kuti zikhale zokonzera Nyumba ya Yehova.
28 先见撒母耳、基士的儿子扫罗、尼珥的儿子押尼珥、洗鲁雅的儿子约押所分别为圣的物都归示罗密和他的弟兄掌管。
Ndipo zonse zimene zinaperekedwa ndi Mlosi Samueli, Sauli mwana wa Kisi, Abineri mwana wa Neri ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya ndi zinthu zonse zimene zinkaperekedwa zimasungidwa ndi Selomiti ndi abale ake.
29 以斯哈族有基拿尼雅和他众子作官长和士师,管理以色列的外事。
Kuchokera ku banja la Izihari: Kenaniya ndi ana ake anapatsidwa ntchito kutali ndi Nyumba ya Mulungu ngati akuluakulu ndi oweruza Israeli.
30 希伯伦族有哈沙比雅和他弟兄一千七百人,都是壮士,在约旦河西、以色列地办理耶和华与王的事。
Kuchokera ku banja la Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake, anthu anzeru 1,700. Iwo ankayangʼanira ntchito zonse za Yehova ndi ntchito yonse ya mfumu cha kumadzulo kwa Yorodani.
31 希伯伦族中有耶利雅作族长。大卫作王第四十年,在基列的雅谢,从这族中寻得大能的勇士。
Pa banja la Ahebroni, Yeriya anali mtsogoleri monga mwa mbiri ya mibado ya mabanja awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide, panachitika kafukufuku ndipo ena mwa anthu aluso a banja la Hebroni anapezeka kuti anali ku Yazeri ku Giliyadi.
32 耶利雅的弟兄有二千七百人,都是壮士,且作族长;大卫王派他们在吕便支派、迦得支派、玛拿西半支派中办理 神和王的事。
Yeriya anali ndi abale 2,700 amene anali aluso ndiponso atsogoleri a mabanja. Mfumu Davide anawayika iwowa kuti aziyangʼanira fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase pa zinthu zonse za Mulungu ndi za mfumu.

< 历代志上 26 >