< 詩篇 95 >
1 請大家前來向上主歡呼,齊向救助我們的磐石歌舞。
Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe, tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu
2 一齊到祂面前感恩讚頌,向祂歌唱聖詩,歡呼吟詠。
Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu, mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.
Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi, ndipo msonga za mapiri ndi zake.
5 海洋屬於祂,因為是祂所創造;陸地屬於祂,因為是祂所形成。
Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye, ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.
Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
7 因為祂是我們的真神,我們是祂牧養的人民,是祂親手引導的羊群。您們今天該聽從祂的聲音:
pakuti Iye ndiye Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za mʼdzanja lake. Lero ngati inu mumva mawu ake,
8 不要再像在默黎巴那樣心頑,也不要像在曠野中瑪撒那天!
musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba, monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.
9 您們的祖先雖然見過我的工作,在那裏他們還是試探我,考驗我。
Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa, ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.
10 四十年之久,我厭惡了那一世代,曾說:這百姓心中迷惑,不肯承認我的真道,
Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo; ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera ndipo sanadziwe njira zanga.”
11 因此我懷著憤怒而起說:他們決不得進入我的的安所。
Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti, “Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”