< 詩篇 78 >

1 阿撒夫的訓誨歌。 我的百姓,請傾聽我的指教。請您們側耳,聽我口的訓導。
Ndakatulo ya Asafu. Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa; mvetserani mawu a pakamwa panga.
2 我要開口講述譬喻,我要說出古代謎語。
Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo, ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
3 凡我們所聽見所知道的,我們祖先傳報給我們的,
zimene tinazimva ndi kuzidziwa, zimene makolo athu anatiwuza.
4 我們不願隱瞞他們的子孫;要將上主的光榮和威能,他所施展的奇蹟和異行,都要 傳報給後代的眾生。
Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
5 他曾在雅各伯頒佈了誡命,也曾在以色列立定了法令;凡他吩咐我們祖先的事情,都要一一告知自己的子孫,
Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli, zimene analamulira makolo athu kuphunzitsa ana awo,
6 叫那未來的一代也要明悉,他們生長後,也要告知後裔,
kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa, ngakhale ana amene sanabadwe, ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
7 叫他們仰望天主,不忘記他的工行,反而常要遵守天主的誡命,
Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu ndipo sadzayiwala ntchito zake koma adzasunga malamulo ake.
8 免得他們像他們的祖先,成為頑固背命的世代,成為意志薄弱不堅,而心神不忠於天主的世代。
Iwo asadzakhale monga makolo awo, mʼbado wosamvera ndi wowukira, umene mitima yake inali yosamvera Mulungu, umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.
9 厄弗辣因的子孫,雖知挽弓射箭,但是在作戰的時日,卻轉背逃竄。
Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta, anathawabe pa nthawi ya nkhondo;
10 他們沒有遵守同天主所立的盟約,他們更拒絕依照天主的法律生活。
iwo sanasunge pangano la Mulungu ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.
11 又忘卻了天主的作為,和他顯給他們的奇事:
Anayiwala zimene Iye anachita, zozizwitsa zimene anawaonetsa.
12 就是他昔日在埃及國和左罕地,當著他們祖先的面所行的奇蹟;
Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona, mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 他分開了大海,領他們出險,他使海水壁立,像一道堤岸;
Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo, Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 白天以雲柱領導他們,黑夜以火柱光照他們;
Anawatsogolera ndi mtambo masana ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 在曠野中,把岩石打破,水流如注,讓他們喝飽,
Iye anangʼamba miyala mʼchipululu ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 由岩石中湧出小河,引水流出相似江河。
Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.
17 但是,他們依舊作惡而得罪上主,在沙漠地區仍然冒犯至高之主。
Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye, kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
18 他們在自己心內試探天主,要求滿足自己貪欲的食物;
Ananyoza Mulungu mwadala pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
19 並且出言反抗天主說:天主豈能設宴於沙漠?
Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti, “Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
20 他雖能擊石,使水湧出好似湍流;但豈能給人民備辦鮮肉與食物?
Iye atamenya thanthwe madzi anatuluka, ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi. Koma iye angatipatsenso ife chakudya? Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”
21 天主聽到後,遂即大發憤怒,烈火燃起,要將雅各伯焚去,怒燄生出,要將以色列剷除;
Yehova atawamva anakwiya kwambiri; moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo, ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli,
22 因為他們不相信天主,也不肯依靠他的救助。
pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu kapena kudalira chipulumutso chake.
23 上主卻仍命令雲彩降下,開啟了天上的門閘,
Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;
24 給他們降下瑪納使他們有飯吃,此外給他們賞賜了天上的糧食。
anagwetsa mana kuti anthu adye, anawapatsa tirigu wakumwamba.
25 天使的食糧,世人可以享受,他又賜下食物,使他們飽足。
Anthu anadya buledi wa angelo, Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
26 他由高天激起了東風,以他的能力引出南風,
Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba, ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.
27 他們降下鮮肉多似微塵灰土,給他們降下飛禽,多似海岸沙數。
Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi, mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
28 降落在他們軍營的中央,在他們帳幕的左右四方,
Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo, kuzungulira matenti awo onse.
29 他們吃了,而且吃得十分飽飫,天主使他們的慾望得以滿足;
Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka pakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka.
30 但他們的食慾還沒有完全滿足,當他們口中還銜著他們的食物,
Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho, chakudya chili mʼkamwa mwawobe,
31 天主便對他們大發怒憤,殺死了他們肥壯的勇兵,擊倒了以色列的青年人。
mkwiyo wa Mulungu unawayakira; Iye anapha amphamvu onse pakati pawo, kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli.
32 雖然如此,他們仍然犯罪,還是不信他的奇妙作為。
Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa; ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe.
33 他使他們的時日,迅速消逝,又使他們的歲月,猝然過去。
Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya. Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso.
34 上主擊殺他們,他們即來尋覓上主,他們回心轉意,也熱切地尋求天主,
Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo; iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu.
35 也想起天主是自己的磐石,至高者天主是自己的救主。
Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo, kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo.
36 但是他們卻滿口欺騙,以舌頭向他說出謊言。
Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo, kumunamiza ndi malilime awo;
37 他們的心對他毫無誠意,不忠於與他所立的約誓。
Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye, iwo sanakhulupirike ku pangano lake.
38 但是他卻慈悲為懷,赦免罪污,沒有消滅他們,且常抑止憤怒;也未曾把自己全部怒火洩露。
Komabe Iye anali wachifundo; anakhululukira mphulupulu zawo ndipo sanawawononge. Nthawi ndi nthawi Iye anabweza mkwiyo wake ndipo sanawutse ukali wake wonse.
39 他又想起他們不過是血肉,是一陣去而不復返的唏噓。
Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe, mphepo yopita imene sibwereranso.
40 他們多少次在曠野裏觸犯了他,在沙漠中激怒了他,
Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululu ndi kumumvetsa chisoni mʼdziko lopanda kanthu!
41 三番五次試探了天主,侮辱了以色列的聖主。
Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu; ankamuputa Woyera wa Israeli.
42 不再想念他那有力的手臂,拯救他們脫離敵手的時日:
Sanakumbukire mphamvu zake, tsiku limene Iye anawawombola kwa ozunza,
43 那日,他曾在埃及國顯了奇蹟,在左罕地行了異事。
tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto, zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.
44 血染了他們的江河與流溪,致使他們沒有了可飲的清水。
Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi; Iwo sanathe kumwa madzi ochokera mʼmitsinje yawo.
45 他使蠅蚋傷害他們,又使蛤蟆侵害他們。
Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga, ndiponso achule amene anawasakaza.
46 把他們的產物交給蚱蜢,將他們的收穫餵給蝗虫。
Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala, zokolola zawo kwa dzombe.
47 下冰雹把他們的葡萄打碎,降寒霜把他們的桑樹打毀,
Iye anawononga mphesa zawo ndi matalala ndiponso mitengo yawo yankhuyu ndi chisanu.
48 將他們的牲畜交給瘟疫,將他們的羊群交給毒疾。
Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala, zoweta zawo ku zingʼaningʼani.
49 向他們燃起憤怒之火,赫赫的震怒,以及災禍,好像侵害人們的群魔。
Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo, anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.
50 他為自己的憤怒開了路,未保存他們脫免於死途,瘟死了他們所有的牲畜,
Analolera kukwiya, sanawapulumutse ku imfa koma anawapereka ku mliri.
51 擊殺了埃及所有的長子,將含帳幕內的頭胎殺死。
Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu
52 他如領羊一般地領出了自己的百姓,他在曠野中引領他們有如引領羊群。
Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto; anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.
53 領他們平安走過,使他們一無所畏。而海洋卻把他們的仇人完全淹斃。
Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha koma nyanja inamiza adani awo.
54 引領他們進入自己的聖地,到自己右手所佔領的山區。
Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.
55 親自在他們的面前把異民逐散,將那地方以抽籤方式分為家產,讓以色列各族住進他們的帳幔。
Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo; Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.
56 但他們仍然試探和觸犯上主,沒有遵守至高者的法律,
Koma iwo anayesa Mulungu ndi kuwukira Wammwambamwamba; sanasunge malamulo ake.
57 叛逆失信,如同他們的祖先,徘徊歧途,好像邪曲的弓箭。
Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo, anapotoka monga uta wosakhulupirika.
58 因他們的丘壇,招惹了上主的義憤,因他們的雕像,激起了上主的怒. 恨。
Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano; anawutsa nsanje yake ndi mafano awo.
59 天主一聽到,即發憤怒,想將以色列完全擯除;
Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri; Iye anakana Israeli kwathunthu.
60 甚至他離棄了史羅的居處,就是他在人間所住的帳幕。
Anasiya nyumba ya ku Silo, tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu.
61 讓自己的力量為人俘擄,將自己的光榮交於敵手;
Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo, ulemerero wake mʼmanja mwa adani.
62 將自己的百姓交於刀劍,對自己的產業燃起怒燄。
Anapereka anthu ake ku lupanga; anakwiya kwambiri ndi cholowa chake.
63 烈火併吞了他們的青年,處女見不到婚嫁的喜宴;
Moto unanyeketsa anyamata awo, ndipo anamwali awo analibe nyimbo za ukwati;
64 他們的司祭喪身刀劍,他們的寡婦不能弔唁。
ansembe awo anaphedwa ndi lupanga, ndipo amayi awo amasiye sanathe kulira.
65 上主好似由睡夢中醒起,又好像酒後歡樂的勇士。
Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuwula chifukwa cha vinyo.
66 他由後方打擊自己的仇讎,使他們永永遠遠蒙羞受辱。
Iye anathamangitsa adani ake; anawachititsa manyazi ku nthawi zonse.
67 他並且棄捨了若瑟的帳幕,不再揀選厄弗辣因的家族。
Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe, sanasankhe fuko la Efereimu;
68 但他卻把猶大的家族揀選;以及自己喜愛的熙雍聖山。
Koma anasankha fuko la Yuda, phiri la Ziyoni limene analikonda.
69 他建築了聖殿如天之高遠,永遠奠定了它如地之牢堅。
Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda, dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya.
70 揀選了自己的僕人達味,且自羊圈裏選拔了達味。
Anasankha Davide mtumiki wake ndi kumuchotsa pakati pa makola ankhosa;
71 上主召叫放羊時的達味,為牧放自己的百姓雅各伯,為牧放自己的人民以色列,
kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa kuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo, wa Israeli cholowa chake.
72 他以純潔的心牧養他們,他以明智的手領導了他們。
Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama; ndi manja aluso anawatsogolera.

< 詩篇 78 >