< 箴言 27 >

1 不要為明日自誇,因為你不知今天能發生什麼。
Usamanyadire za mawa, pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.
2 只應讓人讚美你,你不應開口自誇;讚你的該是他人,不該是你的唇舌。
Munthu wina akutamande, koma osati wekha; mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.
3 石頭重,沙礫沉,愚人的忿怒,比二者都重。
Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri, koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.
4 憤怒固然殘酷,暴怒更是猛烈;可是面對妒恨,有誰能夠抵受﹖
Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa. Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.
5 公開的責斥,勝於暗中的溺愛。
Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino kuposa chikondi chobisika.
6 友人的抨擊是忠誠,仇人的擁吻是欺騙。
Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino, koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.
7 人若吃飽了,蜂蜜也厭惡;若肚子饑餓,苦物也甘甜。
Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi, koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.
8 離家飄泊的遊子,有如無巢可歸的雀鳥。
Munthu amene wasochera ku nyumba kwake, ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.
9 香油和香料,能暢快人心;朋友的勸勉,能撫慰人靈。
Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
10 你的知心朋友,你父親的至交,你切不可離棄;在你憂患的時日,不要進兄弟的家。靠近的鄰舍,勝於遠地的兄弟。
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako, ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto; mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.
11 我兒,作個智慧人,使我心高興,好叫我回答笑罵我的人。
Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga; pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.
12 精明人遇見災禍,即行隱避;無知者反向前走,自招損害。
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.
13 誰為外方人作保,拿出他的衣服;誰為異族人作保,以他本人作質。
Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.
14 清晨向人高聲祝福,就等於向他人咀咒。
Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri, anthu adzamuyesa kuti akutemberera.
15 豪雨的時日,滴漏不已:好吵的女人,也是如此;
Mkazi wolongolola ali ngati mvula yamvumbi.
16 誰願意攔阻她,無異攔阻狂風,又好似右手抓油。
Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.
17 朋友互相砥礪,有如以鐵銼鐵。
Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake, chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.
18 看守無花果樹的,必食其果;護守自己主人的,必受器重。
Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake, ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.
19 人心不同,猶如其面。
Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi, chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.
20 陰府和冥域,總填不滿;世人的眼睛,從不滿足。 (Sheol h7585)
Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta. (Sheol h7585)
21 鍋煉銀,爐煉金,諂媚煉人心。
Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo, chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.
22 你盡可在臼中將愚人舂碎,但他的昏愚卻永不能剷除。
Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo ndi musi ngati chimanga, uchitsiru wakewo sudzachoka.
23 對你羊群的情況,應加注意;對你的家畜,應常留心照料;
Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili. Kodi usamalire bwino ziweto zako?
24 因為錢財並不能永存,寶藏也不能永留萬代。
Paja chuma sichikhala mpaka muyaya, ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.
25 割去了乾草,青草又叢生;山間的野草,也收集起來;
Pamene udzu watha, msipu nʼkumera; ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,
26 那時羔羊供你衣料,山羊供你地價,
ana ankhosa adzakupatsani chovala ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.
27 羊奶足以養你,維持你的家庭,養活你的婢女。
Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri kuti muzidya inuyo ndi banja lanu ndi kudyetsa antchito anu aakazi.

< 箴言 27 >