< 箴言 21 >

1 君王的心在上主手裏,有如水流,可隨意轉移。
Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova; Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.
2 人對自己的行為,都自覺正直;但審察人心的,卻是上主。
Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo, koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.
3 秉公行義,比獻祭獻更悅上主。
Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.
4 傲慢的眼睛,驕傲的心靈,惡人的炫耀,無非是罪惡。
Maso odzikuza ndi mtima wonyada, zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.
5 熟思的人,必足以致富;草率的人,必貧困纏身。
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake; koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.
6 以謊言偽語騙得的財寶,是浮雲輕煙,死亡的羅網。
Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
7 惡人的暴戾,必殃及自身,因他們不肯去履行正義。
Chiwawa cha anthu oyipa chidzawawononga, pakuti iwo amakana kuchita zolungama.
8 惡人的道路,歪曲邪僻;正人的行為,正直適中。
Njira ya munthu wolakwa ndi yokhotakhota, koma makhalidwe a munthu wosalakwa ndi olungama.
9 寧願住在屋頂的一角,不願與吵婦同居一室。
Nʼkwabwino kukhala wekha pa ngodya ya denga la nyumba, kuposa kukhala mʼnyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
10 惡人的心靈,只求邪惡;對自己友伴,毫不關懷。
Munthu woyipa amalakalaka zoyipa; sachitira chifundo mnansi wake wovutika.
11 輕狂人遭受處罰,幼稚者將得明智;智慧人接受教訓,更增加自己知識。
Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru; koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.
12 正義的上主監視惡人的家,且使惡人們都陷於災禍中。
Zolingalira za munthu woyipa nʼzosabisika pamaso pa Yehova, ndipo Iye adzawononga woyipayo.
13 誰對窮人的哀求,充耳不聞,他呼求時,也不會得到應允。
Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.
14 暗中相送的饋贈,可平息忿怒;投入懷中的禮物,可平息狂怒。
Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo, ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa.
15 秉公行義,能叫義人喜樂;但為作惡的人,卻是恐懼。
Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala, koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.
16 凡遠離明智道路的人,必居於幽靈的集會中。
Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.
17 貪愛享樂的人,必遭受窮困;喜愛酒油的人,必不會致富。
Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18 惡人必將為義人作贖金,敗類也將替君子作代價。
Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima.
19 與好爭易怒的女人同居,倒不如獨自住在曠野裏。
Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.
20 珍貴的寶藏和油,積藏在智者家裏;但糊塗愚昧的人,卻將之消耗淨盡。
Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma wopusa amachiwononga.
21 追求正義和仁慈的人,必將獲得生命與尊榮。
Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika, amapeza moyo ndi ulemerero.
22 智者必登上勇士的城邑,攻破城邑所憑倚的保壘。
Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.
23 誰謹守自己的口舌,心靈必能免受煩惱。
Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake sapeza mavuto.
24 高傲的人名叫「狂人」,他行事必極端蠻橫。
Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,” iye amachita zinthu modzitama kwambiri.
25 怠惰人的手不肯操作,必為他的願望所扼殺。
Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito.
26 貪婪的人,終日貪婪;正義的人,廣施不吝。
Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri, koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.
27 惡人的祭獻,已是可憎;若懷惡而獻,更將如何﹖
Nsembe ya anthu oyipa imamunyansa Yehova, nanji akayipereka ndi cholinga choyipa!
28 作假見證的人,必要滅亡;但善於聽的人,纔可常言。
Mboni yonama idzawonongeka, koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.
29 邪惡的人,常裝腔作勢;正直的人,卻舉止檢點。
Munthu woyipa amafuna kudzionetsa ngati wolimba mtima, koma munthu wowongoka amaganizira njira zake.
30 任何智慧、才略或計謀,都不能與上主相對抗。
Palibe nzeru, palibe kumvetsa bwino, palibenso uphungu, zimene zingapambane Yehova.
31 招兵買馬,是為作作戰之日;但是勝利,卻由上主指使。
Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Yehova amene amapambanitsa.

< 箴言 21 >