< 民數記 7 >

1 梅瑟豎立起會幕那天,就傅油祝聖了帳幕和其中的一切器具、祭壇和附屬的用具。他傅油祝聖以後,
Mose atamaliza kuyimika chihema chija, anachidzoza mafuta ndi kuchipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse.
2 以色列的領袖,各家族首領,即協助登記的各支派的領袖,前來奉獻,
Kenaka atsogoleri a Aisraeli, akuluakulu a mabanja omwe ankayangʼanira mafuko a anthu omwe anawawerenga aja, anachita chopereka.
3 將他們的供物獻於上主面前:篷車六輛,公牛十二頭:每兩位領袖一輛車,每位領袖一頭牛。他們把這些送到會幕前時,
Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova: ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ngʼombe zothena khumi ndi ziwiri. Mtsogoleri mmodzi ngʼombe yothena imodzi ndipo atsogoleri awiri ngolo imodzi. Izi anazipereka ku chihema.
4 上主訓示梅瑟說:「
Yehova anawuza Mose kuti,
5 你把這些收下,為會幕的事務使用,按照肋未人的職務,分給他們。」
“Ulandire zimenezi kwa iwo kuti zigwire ntchito ku tenti ya msonkhano. Uzipereke kwa Alevi, aliyense monga mwa ntchito yake.”
6 梅瑟就收下車輛和牛,交給了肋未人。
Choncho Mose anatenga ngolo ndi ngʼombe zothenazo nazipereka kwa Alevi.
7 按革爾雄子孫的職務,分給了他們兩輛車及四頭牛;
Anapereka ngolo ziwiri ndi ngʼombe zothena zinayi kwa Ageresoni monga mwantchito yawo
8 按默辣黎子孫的職務,分給了他們四輛車及八頭牛,他們都在司祭亞郎的兒子依塔瑪爾指揮下服務。
ndiponso anapereka ngolo zinayi ndi ngʼombe zothena zisanu ndi zitatu kwa Amerari molingananso ndi ntchito yawo. Onsewa ankawayangʼanira anali Itamara mwana wa Aaroni wansembe.
9 但沒有分給刻哈特子孫,因為他們應用肩抬所照管的聖物。
Koma Mose sanapereke zimenezi kwa Akohati chifukwa zinthu zawo zopatulika zomwe ankayangʼanira zinali zoti azinyamula pa mapewa awo.
10 在傅油祝聖祭壇時,眾領袖也為祝聖祭壇奉獻了供物。當眾領袖把他們的供物送到祭壇面前時,
Guwa la nsembe litadzozedwa, atsogoleri anabweretsa zopereka zawo zopatulira guwa nazipereka paguwapo.
11 上主對梅瑟說:「每天應有一位領袖,奉獻自己的供物,為祝聖祭壇。」
Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, “Tsiku lililonse mtsogoleri mmodzi azibweretsa chopereka chake chopatulira guwa lansembe.”
12 第一日奉獻自己供物的,是猶大支派阿米納達布的兒子納赫雄。
Amene anabweretsa chopereka chake tsiku loyamba anali Naasoni mwana wa Aminadabu wa fuko la Yuda.
13 他的供物是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, ndi beseni lasiliva limodzi lowazira, lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo wopatulika ndipo zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka chachakudya;
14 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
15 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza;
16 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi yayimuna imodzi, nsembe ya machimo;
17 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是阿米納達布的兒子納赫雄的供物。
ndi ngʼombe zothena ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Naasoni mwana wa Aminadabu.
18 第二日奉獻供物的,是依撒加爾的領袖,族阿爾的兒子乃塔乃耳。
Pa tsiku lachiwiri, Natanieli mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa Isakara, anabweretsa chopereka chake.
19 他奉獻的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chomwe anabwera nacho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, molingana ndi muyeso wa ku malo opatulika. Mbale zonse zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha chakudya.
20 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110 yodzaza ndi lubani;
21 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza:
22 公山羊一隻,為作贖罪祭:
mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yotetezera machimo;
23 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是族阿爾的兒子乃塔乃耳的供物。
ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi, nsembe ya chiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Netanieli mwana wa Zuwara.
24 第三日是則步隆子孫的領袖,赫隆的兒子厄里雅布。
Pa tsiku lachitatu, Eliabu mwana wa Heloni, mtsogoleri wa Azebuloni, anabweretsa chopereka chake.
25 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, mbale zonse zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka cha chakudya;
26 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
27 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza;
28 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
29 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是赫隆的兒子厄里雅布的供物。
ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliabu mwana wa Heloni.
30 第四日是勒烏本子孫的領袖,舍德烏爾的兒子厄里族爾。
Tsiku lachinayi linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa fuko la Rubeni, anabweretsa chopereka chake.
31 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka chachakudya.
32 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
33 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza;
34 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
35 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是舍德烏爾的兒子厄里族爾的供物。
ndi ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri.
36 第五日是西默盎子孫的領袖,族黎沙待的兒子舍路米耳。
Pa tsiku lachisanu Selumieli mwana wa Zurisadai, mtsogoleri wa fuko la Simeoni, anabweretsa chopereka chake.
37 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chake chinali mbale yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
38 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale yagolide imodzi yolemera 110, yodzaza ndi lubani;
39 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wamwamuna wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza;
40 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
41 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是族黎沙待的兒子協路米耳的供物。
ngʼombe ziwiri, nkhosa zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Selumieli mwana wa Zurisadai.
42 第六日是加得子孫的領袖勒烏耳的兒子厄里雅撒夫。
Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, Eliyasafu mwana wa Deuweli, mtsogoleri wa fuko la Gadi, anabweretsa chopereka chake.
43 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
44 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
45 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, chopereka cha nsembe yopsereza:
46 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
47 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,作和平祭:以上是勒烏耳兒子厄里雅撒夫的供物。
ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuweli.
48 第七日是厄弗辣因子孫的領袖阿米胡得的兒子厄里沙瑪。
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa fuko la Efereimu, anabweretsa chopereka chake.
49 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonsezi monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
50 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
51 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza;
52 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
53 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是阿米胡得的兒子厄里沙瑪的供物。
ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elisama mwana wa Amihudi.
54 第八日是默納協子孫的領袖,培達族爾的兒子加默里耳。
Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Gamalieli mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa fuko Manase, anabweretsa chopereka chake.
55 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
56 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani,
57 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza;
58 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
59 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是培達族爾的兒子加默里耳的供物。
ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Gamalieli mwana wa Pedazuri.
60 第九日是本雅明子孫的領袖,基德敖尼的兒子阿彼丹。
Pa tsiku lachisanu ndi chinayi Abidani mwana wa Gideoni mtsogoleri wa fuko la Benjamini, anabweretsa chopereka chake.
61 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha zakudya;
62 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
63 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza;
64 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
65 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是基德敖尼的兒子阿彼丹的供物。
ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni.
66 第十日是丹子孫的領袖,阿米沙待的兒子阿希厄則爾。
Pa tsiku lakhumi Ahiyezeri mwana wa Amisadai, mtsogoleri wa fuko la Dani anabweretsa chopereka chake.
67 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
68 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂:
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
69 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza;
70 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
71 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是阿米沙待的兒子阿希厄則爾的供物。
ndi ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
72 第十一日是阿協爾子孫的領袖,敖革蘭的兒子帕革厄耳。
Pa tsiku la khumi ndi chimodzi, Pagieli mwana wa Okirani, mtsogoleri wa fuko la Aseri, anabweretsa chopereka chake.
73 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
74 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂;
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
75 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza;
76 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo;
77 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻,一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是敖革蘭的兒子帕革厄耳的供物。
ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Pagieli mwana wa Okirani.
78 第十二日是納斐塔里子孫的領袖,厄南的兒子阿希辣。
Pa tsiku la khumi ndi chimodzi Ahira mwana wa Enani, mtsogoleri wa fuko la Nafutali, anabweretsa chopereka chake.
79 他的供物,是一個重一百三十「協刻耳」的銀盤,一個依聖所的衡量,重七十「協刻耳」的銀盆,兩件內都盛滿油調的細麵,為作素祭;
Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
80 一個重十「協刻耳」盛滿香料的金盂,
mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani;
81 公牛犢一頭,公綿羊一隻,一歲的公羔羊一隻,為作全燔祭;
mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza;
82 公山羊一隻,為作贖罪祭;
mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo;
83 又公牛二頭,公綿羊五隻,公山羊五隻一歲的公羔羊五隻,為作和平祭:以上是厄南的兒子阿希辣的供物。
ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahira mwana wa Enani.
84 以上是傅油祝聖祭壇時,以色列領袖們為祝聖祭壇所奉獻的供物,計有銀盤十二個,銀盆十二個,金盂十二個;
Zopereka za atsogoleri a Israeli zopatulira guwa lansembe pamene linadzozedwa zinali izi: mbale khumi ndi ziwiri zasiliva, mabeseni owazira asiliva khumi ndi awiri ndi mbale zagolide khumi ndi ziwiri.
85 銀盤每個重一百三十「協刻耳」,銀盆每個重七十,器皿的銀子依聖所的衡量,共重二千四百「協刻耳」;
Mbale iliyonse yasiliva inkalemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndipo beseni lililonse lowazira linkalemera magalamu 800. Pamodzi, mbale zonse zasiliva zinkalemera makilogalamu 27 monga mwa muyeso wa ku malo opatulika.
86 盛滿香料的金盂十二個,依聖所衡量,每個盂重十「協刻耳」,這些盂的金子,共重一百二十「協刻耳」;
Mbale khumi ndi ziwiri zagolide zodzaza ndi lubanizo zinkalemera magalamu 110 iliyonse, monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Pamodzi, mbale zagolide zinkalemera kilogalamu imodzi ndi theka.
87 為作全燔祭的一切牲畜,計有公牛犢十二頭,公綿羊十二隻,一歲的公羔羊十二隻,還有同獻的素祭;此外尚有公山羊十二隻,為作贖罪祭;
Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yopsereza chinali motere: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, nkhosa zazimuna khumi ndi ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi awiri a chaka chimodzi pamodzi ndi chopereka chachakudya. Mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri zinali za nsembe yopepesera machimo.
88 為作和平祭的一切牲畜,計有公牛犢二十四頭,公綿羊六十隻,公山羊六十隻,一歲的公羔羊六十隻:以上是在傅油祝聖祭壇後,為祝聖祭壇所獻的供物。
Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa.
89 當梅瑟進入會幕為同上主說話時,他聽見從約櫃的贖罪蓋上,兩革魯賓間,有與他說話的聲音:是上主在與他說話。
Mose atalowa mu tenti ya msonkhano kukayankhula ndi Yehova, anamva mawu kuchokera pakati pa Akerubi awiri amene anali pamwamba pa chivundikiro cha bokosi la umboni. Ndipo anayankhula naye.

< 民數記 7 >