< 士師記 18 >
1 那時在以色列沒有君王,同時丹支派仍在尋找居住的基地,因為直到那一天在以色列支派中,丹支派尚未得到基地。
Masiku amenewo munalibe mfumu mu Israeli. Ndipo anthu a fuko la Dani amafunafuna malo okhalamo ngati cholowa chawo, chifukwa kufikira nthawi imeneyo anali asanalandire cholowa chawo pakati pa mafuko a Israeli.
2 於是丹子孫從祚辣和厄市陶耳,由全家族中,派了五個勇敢的人去窺探偵察那地方,對他們說:「你們去偵察那地方! 」他們到了厄弗辣因山地,來到米加的住宅,就在那裏過夜。
Choncho fuko la Dani linatumiza kuchokera ku mabanja awo onse anthu olimba mtima asanu. Anthuwa anachokera ku Zora ndi ku Esitaoli ndipo anatumidwa kukazonda ndi kuliyendera dzikolo. Anthu amenewa ankayimira fuko lonse la Dani. Anthuwa anawawuza kuti, “Pitani mukazonde dzikolo.” Anthuwa anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ndi kupita ku nyumba ya Mika komwe anakagona.
3 他們在米加家附近,認出那少年肋末的聲音,就過去向他說:「誰領你來這裏﹖你在這裏作甚麼﹖你在這裏有甚麼職務﹖」
Ali ku nyumba ya Mika anazindikira mawu a mnyamata, Mlevi uja. Choncho anapita kwa iye namufunsa kuti, “Unabwera ndi ndani kuno? Nanga ukuchita chiyani ku malo ano? Komanso nʼchifukwa chiyani uli kuno?”
4 他回答說:「米加待我如此如此! 他聘了我作他的司祭。」
Iye anawawuza zimene Mika anamuchitira ndipo anati, “Iye anandilemba ntchito ndipo ndine wansembe wake.”
5 他們對他說:「你求問天主,使我們知道,我們將走的路順利嗎﹖」
Kenaka iwo anati kwa iye, “Chonde tifunsire kwa Mulungu kuti tidziwe ngati ulendo wathuwu tiyende bwino.”
6 司祭回答他們說:「你們平安去罷! 上主必使你們所走的路順遂。」
Wansembeyo anawayankha kuti, “Pitani mu mtendere, Yehova ali ndi inu pa ulendo wanuwu.”
7 於是那五個人就去了,來到拉依士,在那裏看見城中的人民安居樂業,一如漆冬人一樣,平安無慮,地產豐富,一無所缺;並且他們離漆冬又遠,與阿蘭也沒有往來。
Choncho anthu asanuwo ananyamuka ndipo anafika ku Laisi, kumene anaona kuti anthu ankakhala mwabata monga anthu a ku Sidoni. Anali anthu opanda chowavuta ndiponso aphee. Tsono popeza mʼdziko mwawo analibe chosowa, iwo anali a chuma. Anaonanso kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Sidoni ndipo analibe ubale ndi wina aliyense.
8 當他們回到祚辣和厄市陶耳自己弟兄那裏時,弟兄們問他們說:「你們帶來什麼消息﹖」
Ozonda dziko aja atabwerera kwa abale awo ku Zora ndi Esitaoli, abale awowo anawafunsa kuti, “Mwaonako zotani?”
9 他們回答說:「起來,讓我們上到拉依士去,因為我們已察看過,那地真肥美,你們還等什麼﹖不要再遲延,趕快去佔領!
“Tiyeni tikamenyane nawo nkhondo popeza taliona dziko lawolo kuti ndi lachonde kwambiri. Kodi simuchitapo kanthu? Musachite mphwayi kupita mʼdzikomo ndi kukalilanda.
10 到那裏去,是到一個不設防的人民那裏去,地面寬廣遼闊;天主已把那地交在你們手中;那地方物產豐富,一無所缺。」
Mukalowa, mukapeza anthu amene ali osatekeseka ndi dziko lalikulu. Yehova wakupatsani dziko limeneli. Malowo ngosasowa kanthu kalikonse kopezeka pa dziko lapansi.”
11 於是有六百丹支派的人,帶著武器,從酢辣和厄市陶耳出發,
Kenaka anthu 600 a fuko la Dani ananyamuka ku Zora ndi Esitaoli atanyamula zida za nkhondo.
12 經過山路,在猶大克黎雅特耶阿陵安營;因此,那地方直到今日叫作「丹營;」這地是在克黎雅特耶阿陵西面。
Tsono anakamanga msasa ku Kiriati-Yearimu mʼdziko la Yuda. Malowa ali kumadzulo kwa Kiriati-Yearimu. Ichi ndi chifukwa chake malowo akutchedwa Mahane Dani mpaka lero.
13 他們又從那裏經過厄弗辣因山地,來到米加的住處。丹人搶去米加的神像
Kuchokera kumeneko anapita ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anafika ku nyumba ya Mika.
14 當時先去窺探那地的五個人,告訴弟兄們說:「你們知不知道,在此家內有「厄弗得、」「忒辣芬」和一尊神像﹖現在你們要決定當作什麼。」
Anthu asanu amene anakazonda dziko la Laisi anati kwa abale awo, “Kodi mukudziwa kuti imodzi mwa nyumba izi muli efodi, mafano a mʼnyumba otchedwa terafimu, fano losema ndiponso fano lokuta ndi siliva? Ndiye mudziwe chochita.”
15 於是他們轉入米加的住宅,來到少年肋末人的屋裏,向他請安問好。
Choncho anthuwa anapatuka napita ku nyumba ya Mika kumene mnyamata, Mlevi uja ankakhala ndipo anamufunsa za mmene zinthu zilili.
Nthawi imeneyi nʼkuti anthu 600 a fuko la Dani aja atayima pa chipata atanyamula zida za nkhondo.
17 先去探地的那五個人就上去,進到裏面,要拿那尊神像並「厄弗得」和「忑辣芬,」此時司祭和那六百個帶武器的人站在門口。
Anthu asanu amene anakazonda dziko aja analowa ndi kukatenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba lotchedwa terafimu, ndi fano lokutidwa ndi siliva. Nthawiyi nʼkuti wansembe uja ndi anthu 600 okhala ndi zida za nkhondo aja ali chiyimire pa chipata.
18 當那些人進入米加家裏,拿那尊神像、「厄弗得」和「忑辣芬」時,司祭問他們說:「你們做什麼﹖」
Anthuwo atalowa mʼnyumba ya Mika ndi kutenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba, ndi fano lokutidwa ndi siliva, wansembeyo anawafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”
19 他們回答說:「不要作聲,用手掩住你的口,跟我們去,作我們的師傅和司祭;你作一個人家的司祭好呢﹖還是在以色列中間作一個支派,一個家族的司祭好呢﹖」
Iwo anamuyankha kuti, “Khala chete usayankhule. Tsagana nafe ndipo udzakhala mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino kwa iwe kukhala wansembe wa fuko lonse la Israeli mʼmalo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?”
20 司祭滿懷高興,遂帶了「厄弗得、」「忑辣芬」和神像,到了那些人中間。
Wansembeyo anakondwera ndipo anatenga efodi, fano la mʼnyumba ndi fano losema natsagana nawo.
21 他們遂轉身回去,把婦孺、牲口以及輜重放在前方。
Choncho iwo anatembenuka nachoka, atatsogoza ana, zoweta ndi katundu wawo yense.
22 當他們離開米加的住宅相當遠的時候,米加和米加家附近的人,都聚集起來,去追趕丹的子孫。
Atayenda mtunda pangʼono kuchokera pa nyumba ya Mika, anthu amene amakhala pafupi ndi nyumba ya Mika anasonkhana kulondola a fuko la Dani aja, ndipo anawapeza.
23 他們向丹的子孫呼喊,丹的子孫回過臉來對米加說:「你叫喊什麼﹖」
Atawafuwulira, a fuko la Dani aja anachewuka ndipo anafunsa Mika kuti, “Chavuta nʼchiyani kuti usonkhanitse anthu chotere?”
24 米加回答說:「你們把我所製的神像和司祭都帶走,我還有什麼呢﹖」怎麼你們還向我說:你作什麼﹖」
Iye anayankha kuti, “Inu mwanditengera milungu imene ndinapanga pamodzi ndi wansembe nʼkumapita. Tsono ine ndatsala ndi chiyani? Ndiye inu mungafunse kuti chavuta nʼchiyani?”
25 丹的子孫對他說:「不要再讓我們聽見你的聲音,免得我們中間有暴燥的人打擊你們,使你和你全家都喪失性命! 」
Anthu a fuko la Dani aja anayankha kuti, “Usayankhuleponso kanthu chifukwa anthu awa angapse mtima nakumenya ndipo iwe ndi banja lako lonse nʼkutayapo miyoyo yanu.”
26 此後,丹的子孫繼續前行,米加見他們比自己強大,就轉身回了家。丹族佔據拉依士
Choncho anthu a fuko la Dani anapitiriza ulendo wawo. Mika ataona kuti anthuwo anali amphamvu kuposa iye, anangotembenuka kubwerera kwawo.
27 丹的子孫帶著米加所做的神像和他私有的司祭,來到拉依士,到了一個平安無慮的人民那裏,用刀劍殺戮了他們,放火燒了那城,
Anthu a fuko la Dani aja anatenga zinthu zimene Mika anapanga pamodzi ndi wansembe uja. Iwo anakafika ku Laisi kwa anthu a phee, osatekeseka aja ndipo anawathira nkhondo, nawapha ndi kutentha mzindawo ndi moto.
28 沒有人來援救,因為拉依士離漆冬很遠,與阿蘭又沒有往來。這城位於貝特勒曷布山谷中;丹的子孫重建這城,住在那裏,
Panalibe wowapulumutsa chifukwa anali kutali ndi Sidoni ndiponso sanali pa ubale ndi wina aliyense. Mzindawo unali mʼchigwa cha Beti-Rehobu. Anthu a fuko la Adaniwo anawumanganso mzindawo ndi kumakhalamo.
29 按他們的祖宗,以色列所生的兒子丹的名字,給這城起名叫丹;其實這城原先名叫拉依士。
Iwo anawutcha mzindawo Dani, kutengera dzina la kholo lawo Dani, amene anali mwana wa Israeli, ngakhale kuti mzindawo poyamba unali Laisi.
30 丹的子孫把那尊神像立起來,梅瑟的後裔,革爾雄的子孫約納堂和他的子孫作丹支派的司祭,直到該地被擄掠的時日。
Anthu a fuko la Dani anayimiritsa fano losema lija. Yonatani mwana wa Geresomu, mwana wa Mose pamodzi ndi ana ake onse anakhala ansembe a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo.
31 天主的殿在史羅多少時日,米加所作的神像在丹支派中也立了多少時日。
Choncho anthu a fuko la Dani ankapembedza fano limene Mika anapanga nthawi yonse pamene nyumba ya Mulungu inali ku Silo.