< 約拿書 2 >

1 約納在魚腹裏,祈求上主,他的天主。
Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake.
2 他說:「我在患難中,呼求上主,衪便應允了我,我從陰府的深處呼求,你便俯聽了我的呼聲。 (Sheol h7585)
Iye anati: “Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova, ndipo Iye anandiyankha. Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo, ndipo Inu munamva kulira kwanga. (Sheol h7585)
3 你將我拋入海心深處,大水包圍了我;你的波濤和巨浪漫過了我。
Munandiponya mʼnyanja yozama, mʼkati mwenimweni mwa nyanja, ndipo madzi oyenda anandizungulira; mafunde anu onse ndi mkokomo wake zinandimiza.
4 我曾說:我雖從你面前被拋棄,但我仍要瞻仰你的聖殿。
Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa pamaso panu; komabe ndidzayangʼananso ku Nyumba yanu yopatulika.’
5 大水圍困我,危及卜性命;深淵包圍我,海草纏住我的頭。
Madzi wondimiza anandichititsa mantha, nyanja yozama inandizungulira; udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.
6 我下深直到礁底,大地的門閂永為我關閉。上主,卜天主! 你卻從坑裏救出了我的性命。
Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri; mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha. Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo, Inu Yehova Mulungu wanga.
7 當我奄奄一息時,我記起了上主;我的祈禱達於你前,達於你的聖殿中。
“Pamene moyo wanga umachoka mwa ine, ine ndinakumbukira Inu Yehova, ndipo pemphero langa linafika kwa inu, ku Nyumba yanu yopatulika.
8 敬奉虛無偶像的人,實在是捨棄了慈愛的根源。
“Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe amataya chisomo chawo.
9 至於我,我要在頌謝的歌聲中,向你獻祭,償還我許的誓願。救恩屬於上主! 」
Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe ndikuyimba nyimbo yamayamiko. Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa. Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”
10 當時,上主命令那魚,那魚便將約納吐在陸地上。
Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.

< 約拿書 2 >