< 約伯記 32 >

1 因為約伯自以為義,那三個友人就不再回答他。
Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.
2 那時,有個布次蘭族的人,他是巴辣革耳的兒子厄里烏,為了約伯在天主前自以為義人,便大為憤怒;
Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.
3 同時也對約伯的三個友人大為震怒,因為他們找不到適當的答覆,又以天主為不公。
Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.
4 厄里烏先等他們同約伯講完話,因為他們都比他年老。
Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.
5 他一見他們三人無話可說:遂大為憤怒。
Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.
6 於是布次人巴辣革耳的兒子厄里烏發言說:我年齡小,你們年紀大,故此我退縮畏懼,不敢在你們前表示我的見解。
Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati: “Ine ndine wamngʼono, inuyo ndinu akuluakulu, nʼchifukwa chake ndimaopa, ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
7 我心想:「老人應先發言,年高者應教人智慧。」
Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula; anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’
8 但人本來都具有靈性,全能者的氣息賦與人聰明;
Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu, mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.
9 並不是年高者就有智慧,老年人就通曉正義。
Si okalamba amene ali ndi nzeru, si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.
10 故此我請你們且聽我說,我也要表示我的見解。
“Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni; inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’
11 直到如今,我等待你們講話,靜聽你們的理論,等待你們尋出適當的言詞;
Ndadikira nthawi yonseyi, ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula, pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,
12 但現今我已明白看出了,你們中沒一個能駁倒約伯,能回答他的話的。
ineyo ndinakumvetseranidi. Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu; palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
13 你們不要說:「我們尋到了智慧! 只有天主可說服他,人卻不能。」
Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru; Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’
14 我決不那樣辯論,也決不以你們說的話答覆他。
Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine, ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.
15 他們已心亂,不能再回答,且已窮於辭令。
“Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso; mawu awathera.
16 他們已不再講話了,他們已停止,不再答話了,我還等什麼﹖
Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano, pakuti angoyima phee wopanda yankho?
17 現在我要開始講我的一段話,表示出我的見解。
Inenso ndiyankhulapo tsopano; nanenso ndinena zimene ndikudziwa.
18 因為我覺著充滿了要說的話,內心催迫著我。
Pakuti ndili nawo mawu ambiri, ndipo mtima wanga ukundikakamiza;
19 看啊! 我內心像尋覓出口的新酒,要將新酒囊爆裂。
mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo, ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.
20 我一說出,必覺輕鬆,我定要開口發言。
Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike; ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.
21 我決不顧情面,也決不奉承人。
Sindidzakondera munthu wina aliyense, kapena kuyankhula zoshashalika,
22 因為我不會奉承,不然,造我者必立即將我消滅。
pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika, Mlengi wanga akanandilanga msanga.”

< 約伯記 32 >