< 約伯記 29 >

1 約伯繼續他的言論說:
Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:
2 誰能賜我似以前的歲月,像以往天主護守我的時日呢﹖
“Aa! Ndikanakhala momwe ndinalili miyezi yapitayi, masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,
3 那時他的燈,光照在我頭上,藉他的光明,我走過黑暗。
pamene nyale yake inkandiwunikira ndipo ndi kuwunika kwakeko ine ndinkatha kuyenda mu mdima!
4 惟願我如壯年之時,那時天主護佑我的帳幕;
Ndithu, masiku amene ndinali pabwino kwambiri, pamene ubwenzi wa Mulungu unkabweretsa madalitso pa nyumba yanga,
5 全能者與我相偕,我的子女環繞著我;
nthawi imene Wamphamvuzonse anali nane, ndipo ana anga anali atandizungulira mʼmbalimu,
6 那時我以奶油洗腳,崖石流油成河。
pamene popondapo ine panali patakhathamira mafuta a mkaka, ndipo pa thanthwe pamatuluka mitsinje ya mafuta a olivi.
7 當我走出城門,在市井設我座位之時,
“Pamene ndinkapita pa chipata cha mzinda ndi kukhala pa mpando wanga pabwalo,
8 少年人看見我都迴避,老年人都起身站立;
anyamata amati akandiona ankapatuka ndipo anthu akuluakulu ankayimirira;
9 王侯停止講話,用手堵住自己的口;
atsogoleri ankakhala chete ndipo ankagwira pakamwa pawo;
10 首領不敢出聲,舌頭緊貼上顎。
anthu otchuka ankangoti duu, ndipo malilime awo anali atamatirira ku nkhama zawo.
11 凡有耳聽見我的,必稱我有福;凡有眼看見我的,都必稱讚我。
Aliyense amene anamva za ine anayankhula zabwino zanga, ndipo iwo amene anandiona ankandiyamikira,
12 因為我援助了呼救的窮人,和無依無靠的孤兒。
chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo, ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.
13 那受喪亡之痛的人稱謝我,我使寡婦的心歡樂。
Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa; ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye.
14 我披上正義,正義就如我衣;我的公正,猶如我的長袍和冠冕。
Chilungamo chinali ngati chovala changa; chiweruzo cholungama ndiye chinali mkanjo ndi nduwira yanga.
15 我作了盲人的眼,跛者的腳。
Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya; ndinali ngati mapazi kwa anthu olumala.
16 我成了窮人之父,我調查過素不相識者的案件。
Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi; ndinkayimira mlendo pa mlandu wake.
17 我打碎惡人的燎牙,由他牙齒中奪出了獵物。
Ndinkawononga mphamvu za anthu oyipa ndi kulanditsa amene anali atagwidwa.
18 我心想:我必壽終正寢,我的壽數必如塵沙。
“Ndinkaganiza kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga, masiku a moyo wanga ali ochuluka ngati mchenga.
19 我的根蔓延到水邊,夜間甘露落在我的枝葉上。
Mizu yanga idzatambalalira ku madzi, ndipo mame adzakhala pa nthambi zanga usiku wonse.
20 我的榮耀不斷更新,我手中的弓日新月異。
Ulemerero wanga udzakhala wosaguga mwa ine, ndipo uta wanga udzakhala watsopano nthawi zonse mʼdzanja langa.’
21 聽我講話的人,屏息等待,靜聽我的指教。
“Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena mwachidwi, ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga.
22 我講話之後,無人再敢講話,我的話像水珠滴在他們身上。
Ndikayankhula, iwo sankayankhulanso; mawu anga ankawagwira mtima.
23 他們期待我如望甘霖,張著大口如渴盼春雨。
Ankayembekezera ine monga momwe amayembekezera mvula ndipo ankalandira mawu anga ngati mvula ya mʼmalimwe.
24 我向他們微笑,他們不敢相信;我和善的面容,他們必不放過。
Ndikawasekerera, iwo sankatha kukhulupirira; kuwala kwa nkhope yanga chinali chinthu chamtengowapatali kwa iwowo.
25 我為他們選擇了道路,身居前導,一如立在軍中的君王;我引他們到那裏,他們就去。
Ndinkawasankhira njira yawo ndipo ndinkawatsogolera ngati mfumu; ndinkakhala ngati mfumu pakati pa gulu lake lankhondo; ndinali ngati msangalatsi pakati pa anthu olira.”

< 約伯記 29 >