< 耶利米書 12 >
1 上主,幾時我與你爭論,總是你有理;但我仍願與你討論正義:「為什麼惡人的生活總是順利,一般詭詐極惡的人總享安寧﹖
Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse ndikati nditsutsane nanu. Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?
2 你栽植了他們,他們就生長根滋長,結出果實;他們的口離你近,他們的心卻離你遠。
Inu munawadzala ndipo anamera mizu; amakula ndi kubereka zipatso. Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse, koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.
3 至於你,上主,你是認識我的,你考察了我對你的心意;求你把他們像待宰的羔羊一樣拉出來,留待宰殺的一天。
Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa; mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga. Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa! Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
4 [這地要哀傷,整個田野的草木要枯萎到幾時﹖由於居民的邪惡,野獸和飛鳥都被消滅。] 因為他們說:「天主不管我們的作為。」
Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti? Nyama ndi mbalame kulibiretu chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa. Iwo amati: “Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”
5 「你與人徒步競走,尚覺疲乏,你怎麼能與馬角逐﹖在平安的地區尚覺不安,在約旦河的叢林區,你更將何如﹖
Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo? Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino, udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango za ku Yorodani?
6 連你的兄弟和你的父族對你都無誠意,在你後面厲聲喊叫;即便他們對說好話,你也不要相信。」
Ngakhale abale ako ndi anansi akuwukira, onsewo amvana zokuyimba mlandu. Usawakhulupirire, ngakhale ayankhule zabwino ndi iwe.
7 「 離開了我的家,拋棄了我的產業,將我最心愛的人交在敵人的手中。
“Ine ndawasiya anthu anga; anthu amene ndinawasankha ndawataya. Ndapereka okondedwa anga mʼmanja mwa adani awo.
8 我的產業對我竟好像是森林中的獅子,向我咆哮,為我憎恨他它。
Anthu amene ndinawasankha asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango. Akundibangulira mwaukali; nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.
9 我的產業對我竟成了一隻帶斑點的鷙鳥,以致鷙鳥圍著向它襲擊。你們去田黟的一切野獸,叫它們來吞噬。
Anthu anga amene ndinawasankha asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga imene akabawi ayizinga. Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo. Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.
10 許多牧童毀壞了我的葡萄園,蹂躝了我的產業,使我喜愛的產業變為荒蕪的曠野。
Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa, anapondereza munda wanga; munda wanga wabwino uja anawusandutsa chipululu.
11 他們使它荒涼,荒涼得在我面前哀傷;全地荒涼,因為沒有一人關心。
Unawusandutsadi chipululu. Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine. Dziko lonse lasanduka chipululu chifukwa palibe wolisamalira.
12 破壞者已來到曠野的一切高崗上,因為上主的刀劍正在砍伐,從地極到地極,凡有血肉的,都不得安寧。
Anthu onse owononga abalalikira ku zitunda zonse za mʼchipululu. Yehova watuma ankhondo ake kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko, ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.
13 他們播種了麥子,卻收割了荊棘;雖筋疲力竭,卻沒有利益;由於上主的憤怒,都因自己的收穫而害羞。
Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga; anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse. Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”
14 上主這樣說:關於那些險惡的鄰邦.即侵犯我給予我民以色列佔有的產業的鄰邦,看,我要由他們的地上將他們拔除,也要由他們中拔除猶大家。
“Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo.
15 在我拔除他們以後,我要再憐憫他們,引他們復歸自己的產業,各回自己的故鄉。
Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake.
16 設若他們殷勤學走我人民的道路,奉我名發誓說:「上主永在」,如同他們昔日教我人民奉巴耳發誓一樣,他們就可在我的人民中再度復興。
Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga.
17 倘若他們不聽從,我必拔除這民族,將他們拔除消滅──上主的斷語。
Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.