< 以賽亞書 7 >
1 當烏齊雅的孫子,約堂的兒子阿哈次為猶大王時,阿蘭王勒斤和以色列王勒瑪里雅的兒子培卡黑,上來攻打耶路撒冷,但是不能攻陷。
Pamene Ahazi mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya anali mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, koma sanathe kuwugonjetsa.
2 有人報告達味家說:「阿蘭已經駐紮在厄弗辣因!」君王與人民都膽戰心驚,有如風中搖動的樹木。
Tsono nyumba ya Davide inawuzidwa kuti, “Dziko la Siriya lagwirizana ndi Efereimu.” Choncho mfumu Ahazi ndi anthu ake ananjenjemera, monga momwe mitengo ya mʼnkhalango imagwedezekera ndi mphepo.
3 上主對依撒意亞說:「你和你的兒子舍阿爾雅叔布出去,到上池的水溝盡頭,即漂工田間的大道上,去會見阿哈次;
Pamenepo Yehova anawuza Yesaya kuti, “Tuluka, iwe ndi mwana wako Seariyasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu wopita ku Munda wa mmisiri wochapa nsalu.
4 對他說:你必須審慎,保持鎮定,不必畏懼,不要因那兩個冒煙的火把頭-即勒斤、阿蘭和勒瑪里雅之子-的怒火而膽怯。
Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya.
5 雖然阿蘭、厄弗辣因和勒瑪里雅的兒子同謀,迫害你說:
Mfumu ya Siriya, Efereimu ndi mwana wa Remaliya apangana kuti akuchitire choyipa. Akunena kuti,
6 我們上猶大去,擾亂她,把她佔領過來歸於我們,並在那裏立塔貝耳的兒子為王;
‘Tiyeni tikalimbane ndi Yuda. Tiyeni tiliwononge ndi kuligawa; tiligawane pakati pathu, ndipo tilonge ufumu mwana wa Tabeeli kumeneko.’
7 但是吾主上主卻這樣說:這事決不能成立,亦不能發生!
Komabe zimene akunena Ambuye Yehova ndi izi: “‘Zimenezo sizidzatheka, sizidzachitika konse,
8 因為阿蘭的首都是大馬士革,大馬士革的首領是勒斤;
pakuti Siriya amadalira Damasiko, ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi. Zisanathe zaka 65 Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.
9 厄弗辣因的首都是撒瑪黎雅,撒瑪黎雅的首領是勒瑪里雅的兒子。【六年或五年以後,阿蘭將被消滅,厄弗辣因將要衰敗。】假使你們不肯相信,你們必然不能存立。」
Dziko la Efereimu limadalira Samariya ndipo Samariya amadalira mwana wa Remaliya basi. Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu, ndithu simudzalimba konse.’”
Yehova anayankhulanso ndi Ahazi,
11 你向上主你的天主要求一個徵兆罷 !或求諸陰府深處,或求諸上天高處。」 (Sheol )
“Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.” (Sheol )
12 阿哈次回答說:「我不要求,我不願試探上主。」
Koma Ahazi anati, “Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova.”
13 依撒意亞說:「達味的家族,你們聽著罷 !你們使人厭惡還不夠,還要使我的天主厭惡嗎﹖
Apo Yesaya anati, “Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga?
14 因此,吾主要親自給你們一個徵兆:看,有位貞女要懷孕生子,給他起名叫厄瑪奴耳。
Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli.
Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino.
16 因為在這孩子尚未知道棄惡擇善以前,你在那兩個君王面前所擔心的國土,必將荒廢。
Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja.
17 上主必使患難的日子臨於你、你的百姓和你的父家身上;這是從厄弗辣因叛離猶大那一天所未有過的,【即亞述王加禍的日子。】
Yehova adzabweretsa pa inu, pa anthu anu ndiponso pa nyumba ya bambo wanu masiku a mavuto woti sanakhalepo kuyambira tsiku limene Efereimu anapatukana ndi Yuda. Yehova adzabweretsa mfumu ya ku Asiriya.”
18 那一日,上主要喚來埃及大河盡頭的蠅和亞述境內的蜂,
Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya.
19 牠們將要前來,一起落在荒谷、巖穴,以及一切荊棘叢中和一切水溝上。
Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika mu zigwa zozama, mʼmingʼalu ya matanthwe ndi mʼzitsamba zonse zaminga ndiponso ponse pamene pali malo omwetsera ziweto.
20 那一日,吾主要用由大河那邊借來的剃刀【即亞述王】剃去你的頭髮和恥毛,連鬍鬚也要刮掉。
Tsiku limenelo Ambuye adzalemba ganyu ometa ochokera kutsidya kwa Mtsinje, ndiye mfumu ya ku Asiriya, kudzameta tsitsi lanu la ku mutu ndi la mʼmiyendo ndi ndevu zomwe.
Tsiku limenelo adzangosunga ngʼombe yayikazi yayingʼono ndi mbuzi ziwiri.
22 因為出奶很多,人將以乳酪為食,因而境內所有的遺民,都將以乳酪和蜂蜜為食。
Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene ziwetozi zidzapereka, munthuyo azidzadya chambiko. Aliyense amene adzatsalire mʼdzikomo azidzadya chambiko ndi uchi.
23 到那一日,先前所有種植一千棵葡萄,值一千塊銀子的地方,必將叢生荊棘和蒺藜。
Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga.
24 人往那裏去,必須攜帶弓箭,因為遍地都是荊棘和蒺藜。
Anthu adzapita kumeneko kukachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti mʼdziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga.
25 先前用鋤頭開墾的山地,沒有人敢到那裏,因為害怕荊棘蒺藜。那裏將成為放牛和羊群踐踏的地區。
Ndipo mʼmapiri monse mʼmene kale munkalimidwa ndi khasu, simudzapitamo kuopa mkandankhuku ndi minga; malowo adzasanduka odyetserako ngʼombe ndi nkhosa.