< 以賽亞書 22 >
1 有關「神視谷」的神諭:你究竟為了什麼上了屋頂﹖
Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya: Kodi chachitika nʼchiyani, kuti nonsenu mukwere pa madenga?
2 你這座充滿喧嘩嘈雜的城市,享樂的都會!你的被殺者並不是被殺於刀劍,也不是死於戰場。
Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya, iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera? Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga, kapena kufera pa nkhondo.
3 你所有的官長都結伴逃遁,竄逃遠方;你所有的將士也都集體被俘,棄弓就縛。
Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi; koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe. Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo, ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
4 為此我說:「你們不要管我,讓我痛哭一場罷!也不要為了我民族的女兒的零落,有勞你們來安慰我!」
Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga; ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa. Musayesere kunditonthoza chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
5 因為這是一個混亂、蹂躪、惶惑的日子,是屬於吾主萬軍的上主的日子;在「神視谷」內,城牆倒塌,喊聲震撼山岳。
Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo mʼChigwa cha Masomphenya. Malinga agumuka, komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
6 厄藍取了箭囊,阿蘭騎上了戰馬,克爾亮出了盾牌。
Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja. Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
7 你最富麗的山谷充滿了戰車,騎兵已在門前佈好陣勢。
Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta, ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
8 猶大的屏障已被揭開。那天你們只仰望林宮內的武器,
zonse zoteteza Yuda zachotsedwa. Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
9 只看見了達味城上的許多裂縫,聚集了下池塘的蓄水,
inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide anali ndi malo ambiri ogumuka; munasunga madzi mu chidziwe chakumunsi.
10 計算了耶路撒冷的房屋,拆毀了民房來鞏固城牆,
Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
11 在兩城牆之間,又鑿了個蓄水池,來貯藏池塘的水;卻沒有仰望這事的主事者,也沒有回顧那老早計劃了這事。
Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale, koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi, kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
12 那天,吾主萬軍的上主本來叫人哭泣、哀號、削髮、腰束苦衣;
Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi; kumeta mutu wanu mpala ndi kuvala ziguduli.
13 但是,看,仍是歡躍喜樂,宰牛殺羊,飲酒食肉:「吃喝罷!明天我們就要死啦!」
Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala; munapha ngʼombe ndi nkhosa; munadya nyama ndi kumwa vinyo. Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa pakuti mawa tifa!”
14 萬軍的上主親自附耳傳示給我說:「決不赦免你們這罪惡,除非你們死去。」吾主萬軍的上主這樣說。
Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
15 有關宮殿總管舍布納的神諭:吾主萬軍的上主這樣說:去!到那個在高處給自己鑿墳墓,
Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo, amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16 在巖石間給自己闢寢室的家宰那裏去,對他說:「你在這裏有什麼東西﹖你在這裏有什麼人,竟在這裏為你鑿墳墓﹖
Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo kuti udzikumbire manda kuno, kudzikumbira manda pa phiri ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
17 看哪!上主要大力一擲,把你擲得遠遠的;他要抓緊你,
“Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
18 將你捲了又捲,捲成一團,如一圓球,拋擲到廣闊之地。你要死在那裏,連你的彩車也要毀滅,你這個王宮的恥辱!
Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu. Kumeneko ndiko ukafere ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako. Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
20 到那天,我要召希耳克雅的兒子厄里雅金作我的僕人。
“Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya.
21 我要把你的朝衣給他穿上,把你的玉帶給他束上,將你的治權交在他手中;他將作耶路撒冷居民和猶大家室的慈父。
Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda.
22 我要將達味家室的鑰匙放在他肩上;他開了,沒有人能關;他關了,沒有人能開。
Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula.
23 我要堅定他,有如釘在穩固地方的木橛;他將成為他父家榮譽的寶座。
Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye.
24 他父家全部的榮耀、細枝、嫩芽、各種細小的物品,自碗具以至各種壺瓶都懸掛在它上面。
Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
25 到那一天--萬軍上主的斷語--釘在穩固地方的木橛必將脫落,破裂,掉下來,上面所掛的重載也要摔得粉碎。因為上主說了。
“Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’” Yehova wayankhula chomwechi.