< 以賽亞書 13 >

1 阿摩茲的兒子依撒意亞所見有關巴比倫的神諭:
Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:
2 你們在禿山上樹起旗幟,向他們高呼揮手,叫他們走進王侯的御門!
Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see, muwafuwulire ankhondo; muwakodole kuti adzalowe pa zipata za anthu olemekezeka.
3 我已向我聖潔的人下令,並為了我的憤怒,召集了我的戰士,我那驕矜自喜的常勝軍。
Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga; ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira amene amadzikuza ndi chipambano changa.
4 聽!山上有喧囂聲,好像有無數的人群。聽!列國的嘈雜聲,萬民正在聚集;萬軍的上主正在檢閱赴敵的部隊:
Tamvani phokoso ku mapiri, likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu! Tamvani phokoso pakati pa maufumu, ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi! Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera kuchita nkhondo.
5 他們都來自遠方,來自天邊。上主和他盛怒的工具,要來毀滅整個大地。
Iwo akuchokera ku mayiko akutali, kuchokera kumalekezero a dziko Yehova ali ndi zida zake za nkhondo kuti adzawononge dziko la Babuloni.
6 號啕罷!因為上主的日子近了,它來有如全能者實行毀滅;
Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
7 為此,人手將要鬆懈,人心將要消融,
Zimenezi zinafowoketsa manja onse, mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
8 人人都驚慌失措,劇疼和痛苦侵襲他們,痙攣得有如臨產的婦女;他們彼此驚愕相視,面容有如火燄。
Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu, zowawa ndi masautso zidzawagwera; adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka. Adzayangʼanana mwamantha, nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.
9 看哪!上主的日子來到,必有殘忍、雷霆和烈怒,為使大地變為荒涼,為殲滅地上的罪人。
Taonani, tsiku la Yehova likubwera, tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo; kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.
10 那時,天上的眾星與群宿不再發光,太陽一升起即變為昏黑,月亮也不再放光明。
Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga sizidzaonetsa kuwala kwawo. Dzuwa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzawala konse.
11 我要懲罰世界,是為了它的罪惡;懲罰惡人,是為了他們的惡行;要抑制自負者的驕橫,要屈服暴虐者的傲慢;
Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake, anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza, ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
12 我要使人比提煉的黃金更少見,使人比敖非爾純金更希罕。
Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino. Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.
13 為此,由於萬軍上主的憤怒,在他暴發怒火之日,天要震撼,地要震動,離其本位。
Tsono ndidzagwedeza miyamba ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.
14 那時,人們將如被追逐的羚羊,又如無人率領的羊群,各自轉向自己的民族,各自逃回自己的故鄉。
Ngati mbawala zosakidwa, ngati nkhosa zopanda wozikusa, munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo, aliyense adzathawira ku dziko lake.
15 凡被捕獲的,都要被刺殺;凡被擒住的,都要喪身刀下。
Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa adzaphedwa momubaya ndi lupanga.
16 他們的嬰兒將在他們眼前被人摔死,他們的房屋將被洗劫,他們的婦女要受姦污。
Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona; nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.
17 我要鼓勵瑪待人來攻擊他們,這些人既不重視白銀,也必貪愛黃金。
Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva ndipo sasangalatsidwa ndi golide, kuti amenyane ndi Ababuloni.
18 他們的弓箭要刺死青年,對腹中的胎兒毫不憐恤,對於嬰兒,他們的眼睛也毫不憐視。
Adzapha anyamata ndi mauta awo; sadzachitira chifundo ana ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.
19 巴比倫--萬國的光輝,加色丁的驕矜榮耀,必要被上主傾覆,如同索多瑪和哈摩辣一樣,
Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse. Anthu ake amawunyadira. Koma Yehova adzawuwononga ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
20 永遠再沒有居民,世世代代無人居住;阿剌伯人不在那裏設帳,牧人也不在那裏立欄;
Anthu sadzakhalamonso kapena kukhazikikamo pa mibado yonse; palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake, palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.
21 臥在那裏的只有野獸,他們的房屋滿了鴟鴞;駝鳥在那裏棲息,魍魎在那裏舞蹈;
Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko, nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe; mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi, ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.
22 豺狼在宮殿裏嗥叫,野狗在御苑內呼應;她的時期已來近了,她的日子不會久延。
Mu nsanja zake muzidzalira afisi, mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe. Nthawi yake yayandikira ndipo masiku ake ali pafupi kutha.

< 以賽亞書 13 >