< 創世記 20 >
1 亞巴郎從那裏遷往乃革布地,定居在卡德士和叔爾之間。當他住在革辣爾時,
Abrahamu anachokako kumeneko napita ku Negevi ndipo anakakhala ku dziko la Gerari, limene lili pakati pa mzinda wa Kadesi ndi mzinda wa Suri. Anakhala ku Gerari kwa kanthawi,
2 亞巴郎一論到他的妻子撒辣就說:「她是我的妹妹。」革辣爾王阿彼肋客於是派人來取了撒辣去。
ndipo Abrahamu ankawawuza za Sara kuti, “Iyeyu ndi mlongo wanga.” Choncho Abimeleki, mfumu wa ku Gerari anamutenga Sara uja.
3 但是夜間,天主在夢中來對阿彼默肋客說:「為了你取來的那個女人你該死,因為她原是有夫之婦。」
Koma usiku, Mulungu anafika kwa Abimeleki kutulo nati, “Ufatu iwe chifukwa cha mkazi amene watengayu popeza ndi wokwatiwa.”
4 阿彼默肋客尚未接近她,於是說:「我主,連正義的人你也殺害嗎﹖
Nthawi imeneyi nʼkuti Abimeleki asanamukhudze mkaziyo, kotero kuti anati, “Ambuye, kodi mudzawonongadi mtundu wolungama?
5 那男人不是對我說過「她是我的妹妹嗎﹖」連她自己也說「他是我的哥哥。」我做了這事,是出於心正手潔呀! 」
Kodi Abrahamu sanandiwuze kuti iyeyu ndi mlongo wake? Ndiponso mkaziyu ankanena kuti Abrahamu ndi mlongo wake. Choncho ine pochita izi, ndinkachita moona mtima ndiponso mopanda chinyengo.”
6 天主在夢中對他說:「我也知道,你是出於心正做了這事,所以我阻止了你犯罪得罪我,也沒有讓你接觸她。
Tsono kumaloto komweko Mulungu anati kwa iye, “Inde ndikudziwa kuti wachita izi moona mtima, ndipo Ine sindinafune kuti undichimwire. Nʼchifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze.
7 現在你應將女人還給那人,因為他是一位先知,他要為你轉求,你才可生存;倘若你不歸還,你該知道:你以及凡屬於你的,必死無疑。」
Tsopano kabwezere mkaziyo kwa mwamuna wake. Iyeyu ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti ukhale ndi moyo. Koma ukapanda kukamupereka, udziwiretu kuti udzafa pamodzi ndi onse a pa banja pako.”
8 阿彼默肋客很早就起來召集了眾臣僕,將全部實情告訴給他們聽;這些人都很害怕。
Mmamawa mwake Abimeleki anayitanitsa akuluakulu ake onse, ndipo atawafotokozera zimene zinachitika, iwo aja anachita mantha kwambiri.
9 然後阿彼默肋客叫了亞巴郎來,對他說:「你對我們作的是什麼事﹖我在什麼事上得罪了你,竟給我和我的王國招來了這樣大的罪過﹖你對我作了不應該作的事。」
Kenaka Abimeleki anayitana Abrahamu ndipo anati, “Kodi wachita chiyani? Ndakulakwira chiyani kuti undibweretsere ine pamodzi ndi anthu anga chilango chachikulu chotere? Wandichitira zinthu zimene sizinayenera kuchitika.”
10 阿彼默肋客繼而對亞巴郎說:「你作這事,究有什麼意思﹖」
Ndipo Abrahamu anafunsa Abimeleki kuti, “Chifukwa chiyani wachita zimenezi?”
11 亞巴郎答說:「我以為在這地方一定沒有人敬畏天主,人會為了我妻子的緣故殺害我。
Abrahamu anayankha nati, “Ndinkaganiza kuti kuno kulibiretu munthu woopa Mulungu. Ndiye ndimati mwina adzandipha chifukwa cha mkazi wanga.
12 何況她實在是我的妹妹,雖不是我母親的女兒,卻是我父親的女兒;後來做了我的妻子。
Komabe kunena zoona, iyeyu ndi mlongo wangadi, mwana wamkazi wa abambo anga ngakhale kuti si ife a mayi mmodzi. Tsono akhoza kukhala mkazi wanga.
13 當天主叫我離開父家,在外飄流的時候,我對她說:我們無論到什麼地方,你要說我是你的哥哥,這就我是你待我的大恩。」
Ndiye pamene Mulungu anati ndichoke ku nyumba ya abambo anga, ndinawuza mkazi wangayu kuti, ‘Kuti uwonetse kuti ndiwe mkazi wokoma mtima, uziwuza anthu kulikonse kumene tingapite kuti ndine mlongo wako.’”
14 阿彼默肋客把些牛羊奴婢,送給了亞巴郎,也將他的妻子撒辣歸還了他;
Tsono Abimeleki anapereka nkhosa, ngʼombe ndi antchito aamuna ndi aakazi kwa Abrahamu. Ndipo anamubwezeranso Abrahamu Sara, mkazi wake.
15 然後對他說:「看,我的土地盡在你面前,你願住在那裏,就住在那裏。」
Tsono Abimeleki anati kwa Abrahamu, “Dziko langa ndi limene ukulionali; ukhale paliponse pamene ufuna.”
16 繼而對撒辣說:「看,我給了你哥哥一千銀子,作為你在闔家人前的遮羞錢;這樣,各方面無可指摘。」
Ndipo kwa Sara, iye anati, “Ndikumupatsa mlongo wakoyu makilogalamu khumi ndi awiri a siliva kutsimikiza kuti iwe ndi wosalakwa pamaso pa onse amene ali ndi iwe; ulibedi mlandu.”
17 亞巴郎懇求了天主,天主就醫好了阿彼默肋客,他的妻子和他的眾婢女,使她們都能生育,
Tsono Abrahamu anapemphera kwa Mulungu ndipo Mulunguyo anachiritsa Abimeleki, mkazi wake pamodzi ndi adzakazi ake kuti athenso kubereka ana.
18 因為上主為了亞巴郎妻子撒辣的事,關閉了阿彼默肋客家中所有婦女的子宮。
Paja Yehova nʼkuti atatseka akazi onse a mʼbanja la Abimeleki kuti asabereke ana chifukwa cha Sara, mkazi wa Abrahamu.