< 出埃及記 39 >

1 以後用紫色、紅色、朱紅色的毛線,做了聖所內行禮穿的祭服,也做了為亞郎穿的聖衣,全照上主向梅瑟所吩咐的。厄弗得
Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose.
2 用金線,紫色、紅色、朱紅色的毛線和捻的細麻,做了厄弗得,
Popanga efodi, iwo anagwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yosalala yofewa.
3 就是將金子鎚成了薄片,切成細線,以織工編織在紫色、紅色、朱紅色毛線和細麻之中。
Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso.
4 為厄弗得做了肩帶,結在厄弗得的兩端,連結在一起。
Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga.
5 那將厄弗得束在身上的帶子,像厄弗得一樣做成,與厄弗得連在一起,是用金線,紫色、紅色、朱紅色的毛線和捻成的細麻做成的,全按上主向梅瑟所吩咐的。
Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose.
6 將兩塊紅瑪瑙石修好崁在金框內,以刻印之法雕刻了以色列的兒子們的名字。
Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo.
7 將金框安在厄弗得的肩帶上,作為以色列子民的記念石,全照上主向梅瑟所吩咐的。胸牌
Kenaka anayimangirira pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli monga momwe Yehova analamulira Mose.
8 又以繡工用金線,紫色、紅色、朱紅色的毛線和捻的細麻做了胸牌,像做厄弗得一樣。
Iwo anapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri. Anachipanga ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino.
9 做的胸牌是方形的,雙層,一柞長,一柞寬。
Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri.
10 上面安裝了四行寶石:第一行:赤玉、青玉、翡翠;
Kenaka anayikapo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba anayika miyala ya rubi, topazi ndi berili;
11 第二行:紫寶石、藍玉、金鋼石;
mzere wachiwiri anayikapo miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi;
12 第三行:黃瑪瑙、白瑪瑙、紫晶;
mzere wachitatu anayikapo miyala ya opera, agate ndi ametisiti;
13 第四行:黃玉、紅瑪瑙、水蒼玉:這些寶石都鑲在金框內。
mzere wachinayi anayikapo miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi anayiyika mu zoyikamo zagolide.
14 寶石上有以色列的兒子們的名字,按他們的名字共十二塊;按刻印的方法,每塊刻上一個名字,代表十二支派。
Miyalayo inalipo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse unazokotedwa ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.
15 在胸牌上做了金的鏈子,像繩子一樣擰成。
Anapanga timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe.
16 又做了兩個金框和兩個金環;將兩個金環安在胸牌的兩端。
Anapanganso zoyikamo zake zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anamangirira mphetezo pa ngodya ziwiri za chovala chapachifuwa.
17 將兩條金鏈結在胸牌兩端的環子上。
Anamangirira timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho.
18 把兩條鏈子的另兩端結在兩框子上;把兩框子結在厄弗得肩帶的前面。
Ndipo mbali ina ya timaunyoloto anamangirira pa zoyikapo zake ziwiri zija, ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi.
19 又做了兩個金環,安在胸排下兩端,靠近厄弗得的內邊緣上。
Anapanganso mphete ziwiri zagolide ndipo analumikiza ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija.
20 還做了兩個金環,安在厄弗得的前面肩帶的下邊,靠近厄弗得帶子的上邊與肩帶相結連的地方。
Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi.
21 用一根紫繩,把胸牌的環子繫在厄弗得的環子上,使胸牌結在厄弗得的帶上子上,免得胸牌在厄弗得上移動:全照上主向梅瑟所吩咐的。無袖長袍
Anamangirira mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi ija monga Yehova analamulira Mose.
22 以後又為厄弗得做了一件無袖長袍,是織成的,全為紫色。
Anayipangira efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo, wolukidwa ndi mmisiri waluso.
23 長袍中間有一領口,像戰袍的領口;領口周圍鑲上邊,免得破裂。
Mkanjowo unali ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo panali chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike.
24 又在長袍底邊上,用捻的紫色、紅色、珠紅色的毛線做了石榴;
Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo.
25 又用純金做了鈴鐺,將鈴鐺繫在長袍底邊周圍的石榴中間,
Ndipo anapanga maberu agolide wabwino kwambiri ndipo analumikiza mozungulira mpendero pakati pa makangadzawo.
26 如此在長袍底邊周圍,一個鈴鐺,一個石榴;一個鈴鐺,一個石榴,為行敬禮穿:全照上主向梅瑟所吩附的。司祭的禮服
Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose.
27 以後為亞郎和他的兒子們做了細麻長衣,是織成的。
Kwa Aaroni ndi ana ake anawapangira minjiro ya nsalu yofewa yosalala, yolukidwa bwino ndi munthu waluso,
28 也做了細麻的禮冠,細麻的華麗頭巾,捻的細麻布褲子;
nduwira ya nsalu yofewa yosalala, lamba wa nsalu yofewa yosalala, womanga mʼmutu, ndi makabudula amʼkati a nsalu yofewa yosalala olukidwa bwino.
29 又用捻的細麻及紫色、紅色、朱紅色的毛線編織了腰帶:全按上主向梅瑟所吩咐的。
Anapanga lamba wolukidwa bwino wa nsalu yofewa ndi yosalala ya mtundu wa mtambo yapepo ndi yofiira. Ili linaliluso la munthu wopanga zokometsera monga Yehova analamulira Mose.
30 又用純金做了聖冠上的牌子,在上面像雕刻印章,刻上了「祝聖於上。」
Iwo anapanga duwa lagolide wabwino kwambiri ngati chidindo ndipo anazokotapo mawu akuti, Wopatulikira Yehova.
31 又用紫色繩子將這牌子繫在理冠上:全按上主向梅瑟所吩咐的。向梅瑟交代完成的工作
Kenaka analimangira ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira, monga momwe Yehova analamulira Mose.
32 帳棚、會幕的一切工程都完成了;凡上主向梅瑟所吩咐的,以色列子民都照做了。
Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.
33 他們遂把帳棚運到梅瑟前,即帳幕和帳幕的一切用具:鉤子、木板、橫木、柱子、卯座,
Kenaka anabweretsa chihema kwa Mose. Tenti ndi zipangizo zake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake;
34 染紅的公山羊皮的頂罩,海豚皮的頂罩,作屏障的帳幔,
chophimba cha chikopa cha nkhosa yayimuna chonyikidwa mu utoto ofiira, chophimba cha chikopa cha akatumbu ndi nsalu zophimba;
35 約櫃和杠桿,贖罪蓋,
bokosi la umboni pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake;
36 供桌和桌上的一切用具,共餅,
tebulo pamodzi ndi zipangizo zake ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova;
37 純金的燈台與燈盞,即擺在燈台上的燈盞及其一切用具,燈油,
choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo;
38 金祭壇,傅禮的油,馨香的香料,帳棚的門簾,
guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani onunkhira ndi nsalu yotchinga pa khomo lolowera mu tenti;
39 銅祭壇、祭壇的銅格子、杠桿和一切用具,盆和盆座,
guwa lamkuwa ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse; beseni ndi miyendo yake;
40 庭院的帷幔、柱子和卯座,庭院的門簾、繩子和橛子,以及一切為會幕聖所內使用的器皿;
nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano;
41 聖所內行禮的祭服,司祭亞郎的聖衣,和他兒子們盡司祭職的衣服:
ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.
42 以色列子民所作的一切工程,全是照上主向梅瑟所吩咐的。
Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose.
43 梅瑟查看了一切工程,見他們所行的,完全是照上主所吩咐的,遂祝福了他們。
Mose anayendera ntchitoyo ndipo anaona kuti anayichita monga momwe Yehova analamulira. Kotero Mose anawadalitsa.

< 出埃及記 39 >