< 傳道書 6 >

1 我看見在太陽下,另有一種不幸,重壓在人身上:
Ine ndinaona choyipa china pansi pano, ndipo chimasautsa anthu kwambiri:
2 有一人,天主賜他富裕、錢財、光榮;凡他心中所願意的,一件也不缺;但天主沒有讓他享用這一切,卻讓外人享用了:這也是空虛,是一件很悲慘的事。
Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.
3 有一人生有百子,活了很大歲數,他年紀雖高,卻沒有隨心享受福樂,且未得安葬,照我看來,他還不如流產的胎兒。
Ngakhale munthu atabereka ana 100 ndi kukhala ndi moyo zaka zambiri; komatu ngakhale atakhala zaka zambiri chotani, ngati iye sangadyerere chuma chake ndi kuyikidwa mʼmanda mwaulemu, ine ndikuti mtayo umamuposa iyeyo.
4 流產的胎兒徒然而來,悄然而去,他的名字也湮沒無聞;
Mtayo umangopita pachabe ndipo umapita mu mdima, ndipo mu mdimamo dzina lake limayiwalika.
5 他沒有見過天日,也沒有任何知覺,但他總比那人更享安寧。
Ngakhale kuti mtayowo sunaone dzuwa kapena kudziwa kanthu kalikonse, koma umapumula kuposa munthu uja,
6 那人即便活了兩千歲,如未享受福樂,他們二人豈不是同歸一處﹖
ngakhale munthuyo atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma ndi kulephera kudyerera chuma chake. Kodi onsewa sapita malo amodzi?
7 人的一切勞碌都是為了口腹,但他的慾望卻總不知滿足。
Ntchito yonse ya munthu imathera pakamwa pake, komatu iye sakhutitsidwa ndi pangʼono pomwe.
8 智者較愚者究有什麼利益﹖知道如何與人往來的窮人,能得什麼好處﹖
Kodi munthu wanzeru amaposa motani chitsiru? Kodi munthu wosauka amapindula chiyani podziwa kukhala bwino pamaso pa anthu ena?
9 眼看見過的總勝過心所想望的:這也是空虛,也是追風。
Kuli bwino kumangoona zinthu ndi maso kusiyana ndi kumangozilakalaka mu mtima. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
10 已往所有的,都已有名可稱;人為何物,都已知道;人決不能與強於自己的抗辯。
Chilichonse chimene chilipo anachitchula kale dzina, za mmene munthu alili nʼzodziwika; sangathe kutsutsana ndi munthu amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.
11 說話多,必多空談:這對人能有什麼益處﹖
Mawu akachuluka zopandapake zimachulukanso, nanga munthu zimamupindulira chiyani?
12 在空虛,消逝如影的人生少數歲月內,有誰知道什麼事對人有益﹖又有誰能指給人指示,他身後在太陽下要發生什麼事﹖
Pakuti ndani amene amadziwa chomwe ndi chabwino pa moyo wa munthu, pakuti moyo wake ndi wa masiku ochepa ndi opandapake, umangopitira ngati mthunzi. Ndani amene angamufotokozere zimene zidzachitika pansi pano iye atapita?

< 傳道書 6 >