< 申命記 8 >

1 我今日吩咐你的一切誡命,你們應謹守遵行,好使你們生存,人數增多,能去佔領上主向你們的祖先所誓許的地方。
Samalani potsata lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mukhale ndi moyo ndi kuchulukana kuti mulande ndi kulowa mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu.
2 你當記念上主你的天主使你這四十年在曠野中所走的路程,是為磨難你,試探你,願知道你的心懷,是否願遵守他的誡命。
Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi.
3 他磨難了你,使你感到饑餓,卻以你和你祖先所不認識的「瑪納,」養育了你,叫你知道人生活不但靠食物,而且也靠上主口中所發的一切言語生活。
Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.
4 這四十年來,你身上的衣服沒有穿破,你的腳也沒有腫。
Mʼzaka makumi anayi zimenezi, zovala zanu sizinangʼambike ndipo mapazi anu sanatupe.
5 為此,你要明瞭:上主你的天主管教你,如人管教自己的兒子一樣;
Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.
6 所以你當謹守上主你天主的誡命,遵行他的道路,敬畏他。
Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye.
7 因為上主你的天主快要領你進入肥美的土地,那裏有溪流,有泉水,有深淵之水由谷中和山中流出;
Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino, dziko lokhala ndi mitsinje ndi mathawale a madzi, akasupe oyenderera mu zigwa ndi mʼmapiri,
8 那地出產小麥、大麥、葡萄、無花果和石榴;那地出產橄欖、油和蜂蜜;
dziko lokhala ndi tirigu ndi barele, mpesa ndi mitengo ya mkuyu, makangadza, mafuta a olivi ndi uchi;
9 在那地你決不缺糧吃,在那裏你將一無所缺;那地方的石頭是鐵,由山中可以採銅。
dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa.
10 幾時你吃飽了,應感謝上主你的天主,因為是他賜給你這樣肥美的土地。
Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.
11 你應小心,別忘記上主你的天主,而不遵守我今天吩咐你的誡命、規則和法令。
Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero,
12 當你吃飽了,建造了華美房屋居住,
kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo,
13 牛群羊群加多,金銀增加,你所有的一切都增加了,
ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka,
14 你要小心,不要心高氣傲,以致忘記了由埃及地,由為奴之家,領你出來的上主你的天主,
mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo.
15 是他領你經過了遼闊可怖,有火蛇蝎子的曠野,經過了乾旱無水之地;是他使水由堅硬的磐石中為你流出,
Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma.
16 是他在曠野內,以你祖先不認識的「瑪納」養育了你;他這樣磨難你,試探你,終究是為使你獲得幸福。
Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino.
17 你心裏不要想:「這是我的力量,我手臂的能力,給我造就了這樣的財富。」
Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.”
18 你應記得上主你的天主,因為是他賜給你得財富的能力,為實踐他對你祖先起誓訂立的盟約,就如今日一樣。
Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.
19 如果你真忘記了上主你的天主,而隨從別的神,奉事敬拜他們,我今日對你們作證:你們必要滅亡,
Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu.
20 上主怎樣由你們面前毀滅了那些民族,你們也要怎樣遭受毀滅,因為你們沒有聽從上主你們天主的聲音。
Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.

< 申命記 8 >