< 申命記 17 >

1 有任何殘缺或瑕疵的牛羊,不可祭獻給上主你的天主,因為這為上主你的天主是可憎惡的事。
Musapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena cholakwika chilichonse, pakuti zimenezi zimamunyansa.
2 在你中間,即在上主你的天主賜給你的一座城內,若發見一個男人或女人,做了上主你的天主眼中視為惡的事,違犯了他的盟約,
Ngati mwamuna kapena mkazi pakati panu, mʼmizinda imene Yehova akukupatsani apezeka akuchita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu pophwanya pangano lake,
3 去事奉敬拜其他的神,或太陽,或月亮,或任何天象,反對我所吩咐的事;
ndipo ngati motsutsana ndi lamulo langa wapembedza milungu ina, kuyigwadira milunguyo, kaya ndi dzuwa kapena mwezi kapena nyenyezi zakumwamba,
4 如果有人告訴了你,你一聽說,就應詳細調查。如果實有其事,真在以色列中做了這種可惡的事,
ndipo inu nʼkuwuzidwa zimenezi, mufufuze bwinobwino. Ngati ndi zoona, ndipo ngati zatsimikizika kuti chonyansa choterechi chachitikadi mu Israeli,
5 就將那做這種惡事的男人或女人,帶到城門外,用石頭砸死他們。
mumutengere mwamuna kapena mkazi amene wachita chonyansa choterechi ku chipata cha mzinda wanu ndi kumupha pomugenda miyala.
6 根據兩個或三個見證的口供,即可將這該死的人處以死刑;根據一個見證的口供,卻不可處以死刑。
Munthu aziphedwa pakakhala mboni ziwiri kapena zitatu koma osati mboni imodzi yokha ayi.
7 見證人應先下手,然後眾人纔下手將他處死:如此由你中間剷除了這邪惡。
Wochitira umboniwo ndiwo aziyamba kumupha munthuyo, ndipo kenaka anthu onse. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
8 若在你城鎮內發生了訴訟案件:或是殺人,或是爭訟,或是毆傷,而又是你難以處決的案件,你應起來上到上主你的天主所選的地方,
Ngati akubweretserani milandu mʼmabwalo anu imene ili yovuta kuweruza kaya ndi yokhetsa magazi, kaya ndi yophwanyirana ufulu, kaya ndi yovulazana, muyitengere kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.
9 去見肋未司祭和那在職的判官,詢問他們,他們要指教你怎樣判斷這案件。
Mudzapite kwa ansembe Alevi ndi kwa woweruza wa pa nthawi imeneyo. Kawafunseni ndipo iwowo adzakuwuzani zoyenera kuchita.
10 你應依照他們在上主所選的地方,有關那案件指教你的話去執行;凡他們教訓你的,應完全遵行。
Kachiteni zimene adzakuwuzenizo kuchokera ku malo amene Yehova adzasankhe. Kaonetsetseni kuti mukutsatira zonse zimene akuwuzanizo.
11 應全依照他們給你的指導,告訴你的判斷去執行;對他們告訴你的定案,不可偏左偏右。
Kachiteni motsatira malamulo ndi malangizo amene adzakuwuzeni; osawanyoza, potembenukira kumanja kapena kumanzere.
12 若有人擅自行事,不聽從那侍立於上主你的天主前供職的司祭,或不聽從判官,應把這人處死。如此你由以色列中剷除了這邪惡;
Munthu aliyense amene adzanyoza woweruza kapena wansembe amene akutumikira kumeneko mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu, aphedwe ndithu. Muzichotsa choyipa pakati pa Israeli.
13 民眾聽見了,必都害怕,再不敢擅自行事。
Anthu onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha, choncho sadzadzikuzanso.
14 當你進入上主你的天主賜給你的土地,佔據了那地,安住在那裏以後,你如說:「我願照我四周的各民族,設立一位君王統治我,」
Mukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge, ndipo mukakakhazikika mʼmenemo nimunena kuti, “Tiyeni tisankhe mfumu yoti izitilamulira monga imachitira mitundu yonse yotizungulirayi,”
15 你應將上主你的天主所揀選的人,立為你的君王。應由你兄弟中立一人,作你的君王,不可讓不屬你兄弟的外方人統治你。
mudzakhazikitse mfumu yoti izikakulamulirani, mfumu imene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati panu. Mudzasankhe mfumuyo kuchokera pakati pa abale anu. Osasankha mlendo, munthu amene sachokera pakati pa abale anu Aisraeli.
16 但是,不可許他養許多馬,免得他叫人民回到埃及去買馬,因為上主曾對你們說過:「你們不可再回到那條路上去;」
Komatu mfumuyo isadzikundikire akavalo, kapena kutuma anthu kupita ku Igupto kukayipezera akavalo ena, pakuti Ambuye akuti, “Simuyenera kubweranso ku Igupto mʼnjira yomweyo.”
17 也不可許他有許多妻妾,免得他的心迷於邪途;也不可許他過於積蓄金銀。
Asadziwunjikire akazi kuopa kuti mtima wake ungamusocheretse. Asadziwunjikirenso golide ndi siliva wambiri.
18 幾時他登上了王位,依照肋未司祭處所存的法律書,給他抄寫一本,
Akakhala pa mpando waufumuwo, ayenera kulemba za iye mwini mʼbuku la malamuloli, kuchokera kwa ansembe Alevi.
19 叫他帶在身邊一生天天閱讀,好使他學習敬畏上主他的天主,謹守遵行這法律上的一切話和這些規則。
Asunge zimene walembazo ndipo ayenera kumaziwerenga masiku onse a moyo wake, kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake posunga mosamalitsa malamulo ndi malangizowa.
20 如此他可避免對自己的同胞心高氣傲,偏離這些誡命,好使他和他的子孫在以色列中間久居王位。
Asadzione kuti iyeyo ndi wopambana kuposa abale ake, nalekeratu kutsatira malamulo. Akasamala zimenezi iye ndi ana ake adzalamulira ufumu wa Israeli kwa nthawi yayitali.

< 申命記 17 >