< 申命記 13 >
1 若你們中出現了一位先知或作夢的人,給你提供一種神蹟或奇事,
Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa,
2 而他所說的神蹟和奇事實現了,以致向你說:「讓我們去隨從事奉其他的神罷! 」而那神是你素不相識的;
chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe),
3 你不要聽從這先知或作夢者的話,因為上主你們的天主有意試探你們,願意知道你們是否全心全靈真愛上主你們的天主。
musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
4 你們只應跟隨上主你們的天主,只應敬畏他,遵守他的誡命,聽從他的話,事奉他。依靠他。
Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo.
5 至於這先知或作夢的人,應處死刑,因為他出言背叛了領你出埃及地,由奴隸之家贖出你來的上主你們的天主,要你離棄上主你的天主命你當行的道路:如此你由你中間剷除了邪惡。
Mneneri kapena wolotayo ayenera kuphedwa, popeza analalikira zopandukira Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo. Wolalikirayo anafuna kukupatutsani pa njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani kuti muyitsatire. Muzichotsa choyipa pakati panu.
6 如果你的兄弟,你父親或母親的兒子,或你的兒女,或你的愛妻,或你視如性命的朋友,暗中引誘你說:「讓我們去事奉其他的神罷! 」而那神是你和你的祖先素不相識的,
Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe,
7 是你四周,離你或近或遠,由地極這邊到地極那邊的各民族所敬拜的神;
milungu ya anthu okuzungulirani, kaya ndi apafupi kapena akutali, kuchokera kumapeto mpaka kumapeto kwina kwa dziko lapansi),
8 你不可對他表示同意,不可聽從他,也不可憐視他,顧惜他,袒護他;
musamugonjere kapena kumumvera. Musamumvere chisoni. Musamuleke kapena kumutchinjiriza.
9 務要將他殺死,並且你應先動手,然後全體人民動手打死他。
Mumuphe ndithu. Dzanja lanu likhale loyambirira kumupha, kenaka manja a anthu ena onse.
10 你應用石頭砸死他,因為他圖謀使你離棄領你出埃及地,出奴隸之家的上主你的天主。
Mumuponye miyala mpaka kumupha, chifukwa anafuna kukupatutsani pa njira ya Yehova Mulungu amene anakutulutsani ku Igupto, dziko la ukapolo.
11 這樣全以色列人聽了必然害怕,在你中間不致做出這樣邪惡的事。
Tsono Aisraeli onse adzamva nachita mantha, ndipo palibe mmodzi pakati panu amene adzachitenso choyipa chotere.
12 如果你聽說,在上主你的天主賜給你居住的一座城內,
Ngati mumvetsedwa kuti ku umodzi mwa mizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mukhalemo,
13 由你中間出來了一些壞人,勾引本城的居民說:「讓我們去事奉其他的神罷! 」而那神是你們素不相識的;
kwapezeka anthu ena oyipa pakati panu ndipo asocheretsa anthu ambiri mʼmizinda yanu, pomanena kuti, “Tiyeni tikapembedze milungu ina” (milungu imene simunayidziwe),
14 你就該調查、探尋、仔細訪問;如果真有其事,在你中間真發生了這樣可惡的事,
mukuyenera kufunsa, kulondola ndi kufufuza bwino nkhaniyo. Ndipo ngati zitatsimikizikadi kuti ndi zoona kuti chinthu chonyansa chotere chachitikadi pakati panu,
15 你該用利劍殺盡這城的居民,完全破壞此城和城中所有的一切,連城中的牲畜也用劍殺盡,
muyenera kuwapha onse okhala mu mzinda umenewo. Muwonongeretu kwathunthu mzindawo, anthu ake ndi ziweto zake zomwe.
16 並把由城中掠奪的一切財物堆積在廣場上,將城和所掠奪的一切財物放火焚燒,全獻給上主你的天主,使那城永遠成為廢墟,再不得重建。
Katundu yense wa anthu mu mzindawo mumuwunjike pamodzi pakatikati pa bwalo losonkhanako ndipo mutenthe mzindawo pamodzi ndi katundu wake yense monga nsembe yathunthu yopsereza ya kwa Yehova Mulungu wanu. Mzinda umenewo ukhale bwinja mpaka muyaya, usadzamangidwenso.
17 凡應毀滅之物,一件也不可留在你手中,好使上主撤回他的盛怒,對你施恩,憐恤你,照他對你祖先所誓許的,使你繁昌,
Musapezeke ndi kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa kuti Yehova abweze mkwiyo wake wochititsa manthawu. Adzakuchitirani chifundo ndi kukumverani chisoni, ndipo adzakuchulukitsani monga analonjeza mwa lumbiro kwa makolo anu,
18 只要你聽從上主你的天主的話,遵守我今天所吩咐你的一切誡命,實行上主你的天主眼中視為正直的事。
chifukwa mumamvera Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino ndi kuchita zoyenera pamaso pake.