< 申命記 12 >

1 這是你們在上主你祖先的天主賜給你作產業的地上,當遵守奉行的法令和規則;你們幾時生活在那地,就應日日遵守。
Awa ndi malangizo ndi malamulo amene muyenera kusamalitsanso kuti muwatsatire mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani kuti mutenge pa nthawi yonse imene muti mudzakhale mʼdzikomo.
2 凡你們去征服的民族供奉神祇的地方,無論在高山上,或在丘陵上,或在任何綠樹下,都應加以破壞:
Muwonongeretu kwathunthu malo onse a pamwamba pa mapiri ataliatali ndi pa mapiri angʼonoangʼono ndi pansi pa mtengo uliwonse wotambalala pamene mitundu imene muyilande dzikolo ankapembedzerapo milungu yawo.
3 拆毀他們的祭壇,打碎他們的石碣,燒毀他們的神柱,砍倒他們神祇的雕像,將他們的名字由那地方完全消除。
Mugumule maguwa awo ansembe, ndi kuphwanya miyala yawo yachipembedzo ndipo mutenthe pa moto mafano awo a Asera: mugwetse mafano a milungu yawo ndi kufafaniza mayina awo mʼmalo amenewo.
4 你們不可像他們那樣崇拜上主你們的天主。
Musapembedze Yehova Mulungu wanu monga mmene amachitira iwowa.
5 上主你們的天主,將由你們各支派中選擇一個地方,為立自己的名號,為做自己的住所,你們只可到那裏去尋求他,
Koma inu muzifunafuna kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati pa mafuko anu kuti ayikeko dzina lake ndi kukhalako. Ku malo amenewa muyenera kupitako.
6 在那裏奉獻你們的全燔祭、祭獻、什一之物、獻儀、還願祭、自願祭,以及首生的牛羊;
Kumeneko muzipititsako zopereka zanu ndi nsembe zanu zopsereza, ndi chakhumi chanu ndi mphatso zapadera zimene munalonjeza kupereka ndi zopereka zanu zaufulu ndi ana oyamba a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu.
7 在那裏你們和你們的家屬,應在上主你們的天主面前宴會歡樂,因為上主你們的天主祝福了你們的一切事業。
Kumeneko, pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalalako pa china chilichonse chimene mudzakhudza, chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.
8 你們不要照我們今日在這裏所行的,各行其是,
Musadzachite monga tikuchitira lero lino, aliyense kumachita zimene akuona kuti ndi zoyenera,
9 因為你們至今還沒有到安居之地,還沒有到上主你的天主賜給你為業的地方。
pakuti simunafike ku malo opumulirako ndi ku cholowa chimene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
10 但是,當你們過了約但河,住在上主你們的天主賜給你們為業的地方,脫免了四周的仇敵,安居樂業時,
Koma mudzawoloka Yorodani ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, ndipo Iye adzakupatsani inu mpumulo ku adani anu okuzungulirani kuti mukhale motchinjirizidwa.
11 你們應在上主你們的天主所選定為立自己名號的地方,奉獻我所吩咐的一切:即你們的全燔祭、獻祭、什一之物、獻儀,以及一切向上主許願應獻的禮品;
Tsono kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti azikhalako muzikabweretsako chilichonse chimene ndikulamulirani inu: zopereka ndi nsembe zanu zopsereza, chakhumi chanu ndi mphatso zapadera, ndi chuma chanu chonse chosankhika chimene munalonjeza kwa Yehova.
12 你們和你們的兒女、僕婢,以及在你們城鎮裏的肋未人,都應在上主你們的天主面前一同歡樂,因為肋未人沒有在你們中分得產業。
Ndipo kumeneko inu mukasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamodzi ndi ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi a mʼmidzi yanu, amene alibe gawo kapena cholowa chawochawo.
13 你應小心,不可在你所見的任何地方奉獻你的全燔祭;
Musamalitse kuti musakaphere nsembe zanu zopsereza paliponse pamene mungafune.
14 只可在上主由你一支派中所選定的地方,奉獻你的全燔祭,行我所規定的一切。
Mukaphere pa malo okhawo amene Yehova adzawasankhe mwa limodzi la mafuko anu, ndipo kumeneko mukasunge chilichonse chimene ndikulamulireni.
15 但是你可在各城鎮內,依照上主你的天主所賜與你的祝福,隨意殺牲食肉;不潔和潔淨的,人都可以吃,如吃羚羊和鹿肉一樣;
Koma mukhoza kumapha ziweto zanu mʼmizinda iliyonse ndi kudya nyama yake mmene mungafunire, ngati kuti ndi agwape kapena mbawala, monga mwadalitso limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Woyeretsedwa ndi wosayeretsedwa akhoza kuyidya.
16 只有血,你們不可以吃,你應將血和水一樣潑在地上。
Koma musamadye magazi. Muziwathira pansi ngati madzi.
17 你所收的五穀、酒、油的十分之一,你的頭胎牛羊,你許願獻的供物,或自願獻的供物以及你手中的獻儀,都不可在你的城鎮內吃,
Musamadyere mʼmizinda yanu chakhumi cha tirigu wanu ndi vinyo watsopano ndi mafuta, kapena za ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu, kapena chilichonse chimene mwalonjeza kuchipereka, nsembe zanu zaufulu, kapena mphatso zapadera,
18 只可在上主你的天主面前,在上主你的天主選定的地方,你和你的兒女、僕婢,以及在你城鎮內的肋未人一起吃;在上主你的天主面前,為了你的一切事業而歡樂。
mʼmalo mwake, muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhira inu, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi ochokera mʼmizinda yanu, ndipo mudzasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa chilichonse chimene mudzachikhudza.
19 你要留意,在你的地域內,永不可忘記肋未人。
Muonetsetse kuti musawataye Alevi pa masiku onse amene mukhale mʼdziko lanumo.
20 當上主你的天主,照他對你所許的,擴展了你的疆域時,你若說:「我想吃肉,」你既然想肉吃,你可以任意吃肉。
Yehova Mulungu wanu akadzakulitsa dziko lanu monga anakulonjezerani, ndipo mukapukwa nyama mumanena kuti, “Ndikufuna nyama,” pamenepo mudzadya mmene mungafunire.
21 若上主你的天主選定建立自己名號的地方離你太遠,你可照我吩咐你的,宰殺上主賜給你的牛羊,在你的城鎮內任意吃,
Ngati malo amene Yehova Mulungu wanu awasankha kuti ayike Dzina lake ali kutali kwambiri ndi inu, mukhoza kupha ziweto pakati pa ngʼombe ndi nkhosa zimene Yehova wakupatsani, monga ndinakulamulani, ndipo mʼmizinda yanuyanu mukhoza kuzidya mmene mungafunire.
22 全如吃羚羊和鹿肉一樣;不潔和潔淨的,人都可以一起吃。
Muzidye ngati mukudya gwape kapena mbawala. Onse oyeretsedwa monga mwa mwambo ndi osayeretsedwa omwe akhoza kudya.
23 但應記住:不可吃血,因為血是生命,你不可將生命與肉一起吃。
Koma muonetsetse kuti musadye magazi, chifukwa magazi ndi moyo, ndipo musamadye moyo pamodzi ndi nyama.
24 你不可吃血,應將血和水一樣潑在地上。
Inu musamadye magazi, muziwathira pansi ngati madzi.
25 你不要吃血,好使你和你的後代子孫能享幸福,因為你行了上主眼中視為正直的事。
Musamadye magazi kuti zikuyendereni bwino inu pamodzi ndi ana anu a pambuyo panu, popeza mudzakhala mukuchita zoyenera pamaso pa Mulungu.
26 至於你所獻的聖物和許願的祭品,應帶到上主所揀選的地方去;
Koma mutenge zinthu zanu zoyeretsedwa ndi china chilichonse chimene munalumbira kupereka, ndi kupita kumalo kumene Yehova adzasankhe.
27 將你的全燔祭、肉和血全獻在上主你的天主的祭壇上;至於其他的祭獻,應將血倒在上主你的天主的祭壇上,肉可以吃。
Mupereke nsembe zanu zopsereza pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, nyama pamodzi ndi magazi omwe. Magazi a nsembe zanu athiridwe pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyamayo mukhoza kudya.
28 你應謹慎聽從我吩咐你的這一切事,好使你和你的後代子孫永遠享福,因為你行了上主你的天主眼中視為善良和正直的事。
Onetsetsani kuti muzimvera mawu onsewa amene ndikukupatsani kuti zinthu zizikuyenderani bwino nthawi zonse inu ndi ana anu chifukwa mudzakhala mukuchita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
29 當上主你的天主,將你所要進佔之地的民族,由你面前剷除,而你佔領了他們的地方,住在那裏的時候,
Yehova Mulungu wanu adzachotsa pamaso panu mitundu ya anthu amene mukufuna kuwathira nkhondo ndi kuwalanda dzikolo. Koma mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼdziko lawo,
30 你應小心,不要在他們由你面前消滅以後,你自己反受迷惑,去仿傚他們;也不要探究他們的神說:「這些民族怎樣事奉了他們的神,我也要怎樣去做。」
ndipo pamene iwo awonongeka pamaso panu, samalirani kuti musakodwe mu msampha pa kufufuza za milungu yawo, nʼkumati, “Kodi anthu a mitunduwa amatumikira bwanji milungu yawo? Ifenso tichita momwemo.”
31 對上主你的天主,你不可這樣做,因為凡上主所憎恨的可惡之事,他們對自己的神都做了;甚至為自己的神,用火焚燒了自己的子女。
Musapembedze Yehova Mulungu wanu momwe amachitira iwowo, chifukwa popembedza milungu yawoyo amachita zonyansa zamitundumitundu zimene Yehova amadana nazo. Amatentha ngakhale ana awo aamuna ndi aakazi pa moto ngati nsembe za kwa milungu yawo.
32 凡我吩咐你們的事,你們應謹慎遵行;不可加添,也不可刪除。
Onetsetsani kuti mukuchita zimene ndikukulamulirani. Musawonjezerepo kapena kuchotserapo.

< 申命記 12 >