< 撒母耳記下 4 >

1 撒烏耳的兒子依市巴耳,一聽見阿貝乃爾死在赫貝龍,就慌了手腳,全以色列大驚。
Isiboseti mwana wa Sauli atamva kuti Abineri waphedwa ku Hebroni, anataya mtima ndipo Aisraeli onse anachita mantha kwambiri.
2 撒烏耳的兒子依市巴耳有兩個土匪頭目:一個名叫巴阿納,一個名叫勒加布,是本雅明子孫貝洛特人黎孟的兒子,──貝洛特被認為是本雅明族,
Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini,
3 因為貝洛特人逃到了基塔殷,僑居在那裏,直到今日。
chifukwa anthu a ku Beeroti anathawira ku Gitaimu ndipo akhala ali kumeneko ngati alendo mpaka lero lino.
4 撒烏耳的兒子約納堂有個兒子雙足跛了,當撒烏耳與約納堂的凶信由依次勒耳傳來時,他只有五歲,他的乳母帶他逃跑,在慌張逃跑中,他跌瘸了腿;他名叫默黎巴耳。
(Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti).
5 貝洛特人黎孟的兒子勒加布和巴阿納出去,正當中午炎熱的時候,到了依市巴耳家裏,他正在床上睡午覺。
Choncho Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti ananyamuka kupita ku nyumba ya Isi-Boseti, ndipo anafika nthawi ya masana kukutentha pamene iye amapumula.
6 看門的女僕在篩麥子,也打盹睡著了。此時勒加布和他兄弟巴阿納溜進去,
Iwo analowa mʼchipinda chamʼkati ngati kuti amakatenga tirigu, ndipo anamulasa mʼmimba. Kenaka Rekabu ndi mʼbale wake Baana anathawa.
7 到了屋內,見依市巴耳正睡在臥室的床上,便將他打死,砍下他的頭,帶著頭,在阿辣巴的大路上走了一夜。
Iwo analowa mʼnyumbamo iye akugona pa bedi mʼchipinda chake. Atamulasa ndi kumupha, anadula mutu wake nʼkuwutenga, nayenda usiku wonse mʼnjira yopita ku Araba.
8 他們帶著依市巴耳的頭,到了赫貝龍見達味王說:「大王的仇人撒烏耳常謀害你的性命;看,他兒子依市巴耳的頭;上主今天為我主向撒烏耳和他的後代報了仇。」
Iwo anabweretsa mutu wa Isi-Boseti kwa Davide ku Hebroni ndipo anati kwa mfumu, “Nawu mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu, amene anafuna kukuphani. Lero lino Yehova wabwezera mbuye wanga mfumu adani anu, Sauli ndi ana ake.”
9 但是,達味答覆貝洛特人黎孟的兒子勒加布和他兄弟巴阿納說:「我指著那救我脫離了一切患難的永生上主起誓:
Davide anayankha Rekabu ndi mʼbale wake Baana, ana a Rimoni wa ku Beeroti kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene wandipulumutsa ku mavuto anga onse,
10 那告訴我說:撒烏耳死了的,自以為是報喜信,我卻拿住他,在漆刻拉格殺了,作為他報信的賞報;
pamene munthu wina anandiwuza kuti, ‘Sauli wafa’ ndipo ankaganiza kuti wabweretsa nkhani yabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha ku Zikilagi. Iyi inali mphotho imene ndinapereka kwa iyeyo chifukwa cha uthenga wake!
11 那麼,現在這些匪徒,偷進人屋,殺了睡在床上的義人,我豈不更該從你們手中追討他的血債,將你們由地上剷除﹖」
Nanji pamene anthu oyipa apha munthu wosalakwa ali mʼnyumba mwake ndiponso pa bedi lake! Kodi ine ndingaleke kukulangani ndi kukuchotsani pa dziko lapansi pano?”
12 達味遂命自己的僮僕,殺了他們,砍去他們的手足,掛在赫貝龍的池旁;至於依市巴耳的頭,叫人拿去葬在赫貝龍,阿貝乃爾的墳墓內。
Kotero Davide analamulira ankhondo ake, ndipo anawapha. Iwo anawadula manja ndi mapazi ndi kupachika matupi awo pa dziwe la ku Hebroni. Koma anatenga mutu wa Isi-Boseti nawuyika mʼmanda a Abineri ku Hebroni.

< 撒母耳記下 4 >