< 列王紀下 6 >
1 眾先知的弟子對厄里叟說:「看,我們同你住的地方太窄小了,
Ana a aneneri anati kwa Elisa, “Taonani malo amene timakhala ndi inu atichepera kwambiri.
2 請你讓我們到約旦河去,每人取一根樑木,在那裏建造我們的住所。」他答說:「你們去罷! 」
Tiloleni tipite ku Yorodani kumene aliyense wa ife akadule mtengo umodzi, kuti timange malo woti tizikhalamo.” Ndipo Elisa anati, “Pitani.”
3 其中一個人說:「請你也同你的僕人一起去! 」厄里叟答說:「我去。」
Mmodzi wa iwo anati, “Chonde mulole kutsagana nawo atumiki anu.” Elisa anayankha kuti, “Ndipita nanu.”
4 先知便同他們一起去了。他們到了約旦河,就砍伐樹木。
Ndipo anapita nawo. Anapita ku Yorodani nayamba kudula mitengo.
5 其中一個,砍木樑時,斧頭掉在水裏了,就大聲叫喊說:哎唷! 我主,這把斧子是借來的啊! 」
Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, “Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!”
6 天主的人問他說:「斧頭掉在那裏﹖」那人將那地方指給先知看。先知即砍下一塊木頭,丟在那裏,使斧頭浮了上來。
Ndipo munthu wa Mulungu uja anafunsa, “Yagwera pati?” Pamene anamuonetsa malowo, Elisa anadula kamtengo nakaponya pamenepo, ndipo nkhwangwayo inayandama.
7 先知對他說:「你拿上來罷! 」他就伸手拿了上來。
Elisa anati, “Itenge.” Ndipo munthuyo anatambalitsa dzanja lake nayitenga.
8 阿蘭王同以色列交戰時,與自己的臣商議說:要在某某地方埋伏。
Tsono mfumu ya ku Aramu inali pa nkhondo ndi Israeli. Itakambirana ndi atsogoleri ake ankhondo inati, “Ndidzamanga misasa yanga pamalo akutiakuti.”
9 但天主的人打發人去見以色列王說:「你要小心提防,不要經過某某地方,因為阿蘭人已在那裏設下埋伏。」
Munthu wa Mulungu anatumiza mawu kwa mfumu ya ku Israeli kuti “Musamale podutsa malo akuti, chifukwa Aaramu akupita kumeneko.”
10 以色列王就派人去偵察天主的人警告他的地方;他就小心防備,不只一兩次。
Choncho mfumu ya ku Israeli inatuma anthu kumalo kumene munthu wa Mulunguyo ananena. Nthawi ndi nthawi Elisa ankachenjeza mfumu, kotero kuti ankakhala tcheru ku malo amenewo.
11 阿蘭王為此事心中頗為煩惱,遂將臣僕召來,對他說:「難道你們不能告訴我:我們中誰支持以色列王嗎﹖」
Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri mfumu ya ku Aramu. Mfumuyo inayitanitsa atsogoleri ake ankhondo ndipo inawafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze munthu amene pakati pathu pano ali mbali ya mfumu ya ku Israeli?”
12 一個臣僕答說:「我主,大王! 沒有誰支持,只有以色列的先知厄里叟,將君王在密室裏所談的事,都告訴了以色列王。」
Mmodzi mwa atsogoleri a ankhondowo anati, “Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu, inu mbuye wanga, koma Elisa mneneri amene ali ku Israeli amawuza mfumu ya ku Israeli mawu enieni amene inu mumayankhula ku chipinda kwanu.”
13 阿蘭王說:「你們去看看他在那裏,我好派人去捉拿。」有人告訴君王說:「他在多堂。」
Choncho mfumu inalamula kuti, “Pitani, kafufuzeni kumene akukhala kuti ine nditume anthu kukamugwira.” Anthuwo anabweretsa mawu oti, “Taonani, Elisa ali ku Dotani.”
14 阿蘭王就打發馬隊戰車和強大的部隊前去,夜間到了那裏,將城圍住。
Ndipo mfumu inatumizako magaleta ndi akavalo ndiponso gulu lankhondo lamphamvu. Anapita usiku nakawuzungulira mzindawo.
15 天主的人的僕人清早起來出門時,看見軍隊車馬將城包圍了,就對先知說:「哎! 我主,我們怎麼辦﹖」
Mtumiki wa munthu wa Mulungu atadzuka mmamawa ndi kutuluka panja, gulu la ankhondo pamodzi ndi akavalo ndi magaleta anali atazungulira mzindawo. Mtumikiyo anafunsa kuti, “Kalanga mbuye wanga, tidzachita chiyani?”
16 先知答說:「不必害怕,因為偕同我們的,比他們的還多。」
Mneneri anamuyankha kuti, “Usachite mantha. Amene ali mbali yathu ndi ambiri kupambana amene ali mbali yawo.”
17 厄里叟就祈禱說:「上主,求你開啟他的眼,叫他看見。」上主就開了僕人的眼,他看見遍山都是火馬車,圍繞著厄里叟。
Ndipo Elisa anapemphera kuti, “Inu Yehova tsekulani maso ake kuti aone.” Pamenepo Yehova anatsekula maso a mtumikiyo, ndipo anayangʼana naona kuti phiri lonse linali lodzaza ndi akavalo ndi magaleta a moto atazungulira Elisa.
18 敵人下到先知那裏的時候,厄里叟懇求上主說:「求你打擊這個民族,使他們眼目失明。」上主果然照厄里叟的話打擊了他們,使他們眼目失明。
Pamene adaniwo ankabwera kudzalimbana naye, Elisa anapemphera kwa Yehova kuti, “Achititseni khungu anthu awa.” Kotero Yehova anawachititsa khungu monga anapemphera Elisa.
19 厄里叟對他們說:「不是這條路,也不是這座城;你們跟我來,我要領你們到你們尋找的人那裏去。」於是先知領他們到了撒瑪黎雅。
Elisa anawawuza ankhondowo kuti, “Njira si imeneyi ndipo mzinda sumenewunso. Tsateni, ndipo ndidzakutengerani kwa munthu amene mukumufunayo.” Ndipo anawatengera ku Samariya.
20 他們一進了撒瑪黎雅,厄里叟就祈禱說:「上主,開啟這些人的眼睛,叫他們看見。」上主果然開了他們的眼睛;他們一看,自己竟在撒瑪黎雅城內。
Atalowa mu mzinda wa Samariya, Elisa anati, “Yehova tsekulani maso a anthu awa kuti aone.” Choncho Yehova anatsekula maso awo ndipo anangoona kuti ali mʼkati mwenimweni mwa Samariya.
21 以色列王看見他們,就對厄里叟說:「我父,要殺死他們嗎﹖」
Mfumu ya ku Israeli itawaona, inafunsa Elisa kuti, “Abambo anga, kodi ndiwaphe? Kodi ndiwaphe?”
22 厄里叟答說:「不要殺他們;你自己用弓劍擄來的人,你豈可殺死﹖你要為這些人預備飯和水,叫他們吃喝,然後讓他們回到自己的主上那裏去。」
Elisa anayankha kuti, “Musawaphe. Kodi mungaphe anthu amene munawagwira pogwiritsa ntchito lupanga ndi uta? Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa kenaka apite kwa mbuye wawo.”
23 君王就給他們預備了盛宴,叫他們吃了喝了,打發他們回到自己的主上那裏去。從此,阿蘭隊伍再沒有侵犯以色列地方。
Choncho anawakonzera mphwando lalikulu, ndipo atatsiriza kudya ndi kumwa, anawatumiza kwawo ndipo anabwerera kwa mbuye wawo. Kotero magulu a ankhondo a ku Aramu analeka kuthira nkhondo dziko la Israeli.
24 這事以後,阿蘭王本哈達得集合了他所有的軍隊,上來圍困撒瑪黎雅。
Patapita nthawi, Beni-Hadadi mfumu ya Aramu anasonkhanitsa gulu lake lonse la ankhondo, napita kukazungulira mzinda wa Samariya.
25 撒瑪黎雅被圍困後,陷於嚴重的飢荒,甚至一個驢頭,值八十「協刻耳」銀子,四分之一「卡步」豆莢,值五「協刻耳」銀子。
Mu mzinda wa Samariya munali njala yoopsa. Ndipo taonani, Aaramu anazungulira mzindawu kwa nthawi yayitali kotero kuti mutu wa bulu ankawugulitsa ndalama za siliva 80, ndipo magalamu 200 a zitosi za nkhunda ankawagulitsa pa mtengo wa masekeli asanu.
26 當以色列王從城牆上經過時,有一個婦人呼求他說:「我主大王,救救我罷! 」
Pamene mfumu inkayenda pa khoma la mzindawo, mayi wina anafuwulira mfumuyo kuti, “Thandizeni mbuye wanga mfumu!”
27 君王答說:「如果上主不救你,我怎能救你﹖靠禾場﹖靠酒池﹖」
Mfumu inayankha kuti, “Ngati Yehova sakuthandiza iwe, ine thandizo lako ndingalipeze kuti? Kuchokera ku malo opunthira tirigu kodi? Kuchokera kumalo opsinyira mphesa kodi?”
28 君王問那婦人說:「你有什麼事﹖」婦人答說:「這個女人曾對我說:把你的兒子交出來,我們今天吃;留下我的兒子,我們明天吃。
Pamenepo mfumuyo inafunsa mayiyo kuti, “Kodi chakuvuta nʼchiyani?” Iye anayankha kuti, “Mayi uyu anandiwuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye lero, ndipo mawa tidzadya mwana wangayu.’
29 於是我們就把我的兒子煮著吃了。第二天我對那女人說:把你的兒子交出來給我們吃,她卻把自己的兒子藏了起來。」
Choncho tinaphika mwana wanga ndi kumudya. Tsiku lotsatira lakelo ine ndinati, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye,’ koma iye anabisa mwana wakeyo.”
30 君王聽了這婦人的話,就撕裂了自己的衣服,─當他正在城牆上經過,民眾都看見了他貼身穿著苦衣,─
Mfumu itamva mawu a mayiyo, inangʼamba mkanjo wake. Pamene inkayenda pa khoma, anthu anayangʼana, ndipo anaona zovala zamʼkati, pakuti anavala chiguduli.
31 說「如果沙法特的兒子厄里叟的頭,今天還留在他身上,願天主嚴厲,且加倍嚴厲地懲罰我! 」
Mfumuyo inati, “Mulungu andilange, andilange kwambiri ndikapanda kudula mutu wa Elisa mwana wa Safati lero!”
32 那時厄里叟正坐在屋裏,長老們同他坐在一起,君王派一個人在他以前去,但是這人還未來到,厄里叟就對長老們說:「你們看,這個兇手之子,竟派人來要斬我的頭。你們注意,使者來到時,你們要把門關上,把他關在門外;在他後面不就是他主上的腳步聲嗎﹖」
Tsono Elisa nʼkuti atakhala mʼnyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Mfumu inatuma munthu wina kuti imutsogolere, koma asanafike, Elisa anawuza akuluakuluwo kuti, “Kodi simukuona momwe wopha munthu uja watumizira munthu wina kuti adzadule mutu wanga? Taonani mthengayo akafika, mutseke chitseko ndipo muchigwiritsitse kuti asalowe. Kodi ndikumvawo pambuyo pake si mgugu wa mbuye wake?”
33 先知還同他們說話的時候,君王就下到他那裏說:「這災難是由上主來的,我對上主還有什麼指望﹖」
Elisa akuyankhulabe ndi anthuwo, taonani, wamthengayo anafika kwa iye. Ndipo mfumu inati, “Mavuto amenewa ndi ochokera kwa Yehova. Kodi nʼchifukwa chiyani ine ndiyenera kudikira thandizo lochokera kwa Yehova?”