< 列王紀下 21 >
1 默納舍登極時才十二歲,在耶咯撒冷做王五十五年,他的母親名叫赫斐漆巴。
Manase anakhala mfumu ali ndi zaka khumi ndi ziwiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 55. Amayi ake anali Hefiziba.
2 他行了上主視為惡的事,仿效上主從以色列子民前所驅逐的異民所行的可恥之事,
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira mchitidwe wonyansa wa mitundu imene Yehova anayipirikitsa pofika Aisraeli.
3 重建了他父親希則克雅所拆毀的高丘,為巴耳建立了祭壇,製造了木偶,像以色列王阿哈布所作的一樣,且崇拜敬奉天上的萬象,
Iyetu anamanganso malo opembedzera mafano amene Hezekiya abambo ake anawawononga. Anamangira Baala maguwa a nsembe ndi mtengo wa fano la Asera monga anachitira Ahabu mfumu ya Israeli ndipo ankapembedza zolengedwa zonse zamlengalenga.
4 雖然上主曾指著聖殿說過:「我要將我的名建立在耶路撒冷。」但他仍在上主的殿內建立了一些祭壇,
Anamanga maguwa ansembewa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Mu Yerusalemu ndidzayikamo Dzina langa.”
5 又在上主殿宇的兩庭院內,為天上萬像建立了祭壇;
Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova, Manase anamangamo maguwa opembedzerapo zinthu zamlengalenga.
6 使自己的兒子經火獻神,行占卜邪術,立招魂師和術士,不斷行上主視為惡的事,惹上主發怒。
Iye anapsereza mwana wake pa moto ngati nsembe, ankachita za matsenga, ankawombeza mawula, ankapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndiponso ankapembedza mizimu. Iyeyo anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova ndipo anakwiyitsa Yehovayo.
7 他又將自己製造的阿舍辣雕像,安放在上主的殿內,雖然上主論及這殿曾對達味的兒子撒羅滿說:「我要在這殿內,和我在以色列各支派所選出的耶路撒冷立我的名,直到永遠;
Iye anatenga fano losema la Asera limene analipanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Yehova, Nyumba imene Yehova ananena kwa Davide ndi mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba iyi ndi mu Yerusalemu ndiwo malo amene ndasankha pakati pa mafuko onse a Aisraeli kuyikamo Dzina langa kwamuyaya.
8 只要以色列謹守遵行我所吩咐他們的一切,及我僕人梅瑟所吩咐他們的一切法律,我決不再使以色列人的腳,離開我賜與他們祖先的土地。」
Sindidzalola kuti Aisraeli achotsedwe mʼdziko lawo limene ndinapatsa makolo awo ngati iwowo adzasamala kuchita zinthu zonse zimene ndinawalamula ndi kusunga malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anawapatsa.”
9 但是,他們卻不聽從,甚至默納舍誘惑他們行惡,甚於上主由以色列子民前所消滅的那些民族。
Koma anthu sanamvere. Manase anawasocheretsa, kotero kuti anachita zoyipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Yehova anawawononga pamene Aisraeli ankafika.
Yehova anayankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri kuti,
11 因為猶太王默納舍行了這些可恥的事,甚於他以前的阿摩黎人所行的,以自己的神像引猶太犯罪。
“Manase mfumu ya Yuda wachita machimo onyansawa ndipo wachita zoyipa kupambana Aamori amene analipo kale iye asanabadwe ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda ndi mafano ake.
12 所以上主以色列的天主這樣說:看,我要使這樣的災禍降在耶路撒冷和猶太,使聽見的人兩耳都要齊鳴。
Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru.
13 我要用測量撒瑪黎雅的繩索,和測量阿哈布家的鉛錘,來測量耶路撒冷,要擦淨耶路撒冷如同人擦淨盤子一樣,擦淨之後,就翻過來;
Ndidzalanga Yerusalemu ndi Yuda pogwiritsa ntchito muyeso umene ndinalangira Samariya ndi Ahabu pamodzi ndi nyumba yake. Ndidzayeretsa Yerusalemu monga mmene munthu amachitira popukuta mbale ndipo atayipukuta amayivundikira pansi.
14 我要拋棄作我產業的遺民,將他們交於敵人手中,使他們成為一切敵人的掠物與勝利品。
Ndidzawataya anthu otsala amene ndi cholowa changa ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Adzachotsedwa ndipo adaniwo adzawalanda zinthu zonse
15 因為他們自從他們的祖先出離埃及那一天,直到今日,行了我視為惡的事,使我發怒。」
chifukwa anachita zoyipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuchokera tsiku limene makolo awo anatuluka mu Igupto mpaka lero lino.’”
16 默納舍除了使猶大陷於罪惡,行了上主視為惡的事以外,還流了許多無辜者的血,使耶路撒冷流成河,從這邊流到那邊。
Kuwonjezera apo, Manase anakhetsa kwambiri magazi a anthu osalakwa mpaka magaziwo kuyenderera mu Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina, kuphatikiza pa kuchimwitsa Yuda, kotero kuti anthu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
17 默納舍其餘的事蹟,他行的一切,所犯的罪惡,都記載在猶大列王實錄上。
Ntchito zina za Manase ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
18 默納舍與他的列祖同眠,埋葬在王宮花園,即烏匝花園裏;他的兒子阿孟繼位為王。
Manase anagona ndi makolo ake ndipo anayikidwa mʼmanda mʼmunda wa Uza, ku nyumba yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
19 阿孟登極時,年二十二歲,在耶路撒冷作王兩年;他的母親名叫默叔肋默,是約特巴人哈魯茲的女兒。
Amoni anakhala mfumu ali ndi zaka 22 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka ziwiri. Amayi ake anali Mesulemeti mwana wa Haruzi, wochokera ku Yotiba.
20 他行了上主認為視為惡的事。全像他父親所行的一樣;
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Manase abambo ake.
21 走了他父親所走的的路,事奉敬拜了他父親所事奉的偶像,
Anatsatira makhalidwe onse a abambo ake. Ankapembedza mafano amene abambo akewo ankawapembedza ndipo ankawagwadira.
Iyeyo anasiya Yehova Mulungu wa makolo ake ndipo sanayende mʼnjira ya Yehova.
Nduna za Amoni zinamuchita chiwembu ndipo zinamupha mʼnyumba yake.
24 但地方的人民起來,殺了所有反叛阿孟王的人,立了他的兒子約史雅繼位為王。
Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anachitira chiwembu Mfumu Amoni, nayika Yosiya mwana wake kukhala mfumu mʼmalo mwake.
25 阿孟所作的其它事蹟,都記載在猶大列王實錄上。
Ntchito zina za Amoni ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
26 他也葬在烏匝花園內自己的墳墓裏;他的兒子約史雅繼位為王。
Iye anayikidwa mʼmanda ake mʼmunda wa Uza. Ndipo Yosiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.