< 撒母耳記上 18 >

1 達味同撒烏耳說完了話,約納堂的心和達味的心很相契;約納堂愛他如愛自己一樣。
Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha.
2 那天,撒烏耳把達味留下,不讓他回父家去。
Choncho Sauli anamusunga Davideyo kuyambira tsiku limenelo ndipo sanamulole kuti abwerere ku nyumba ya abambo ake.
3 約納堂同達味結為盟友,愛他如愛自己一樣。
Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera.
4 約納堂脫下自己穿的外氅,連軍裝,帶刀劍,甚至弓和腰帶,都給了達味。
Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba.
5 撒烏耳派達味出去無論作什麼事,沒有不成功的;故此撒烏耳派他作軍隊的將領;軍民和撒烏耳的臣僕都非常喜愛他。
Davide ankapita kulikonse kumene Sauli ankamutuma kuti apite kukamenya nkhondo, ndipo ankapambana. Choncho Sauli anamupatsa udindo woyangʼanira gulu lankhondo. Ichi chinakondweretsa anthu onse ngakhalenso atsogoleri a nkhondo a Sauli.
6 當達味殺死那培肋舍特人後,班師回來時,婦女們從城中出來,唱歌跳舞,打鼓彈琴,興高采烈地前來歡迎撒烏耳君王。
Anthu akubwerera kwawo Davide atapha Mfilisiti uja, amayi anatuluka mʼmizinda yonse ya Israeli, akuyimba ndi kuvina kukachingamira mfumu Sauli. Ankayimba ndi kuvina mokondwa, kwinaku ngʼoma ndi zitoliro zikulira.
7 婦女們邊唱邊跳說:「撒烏耳殺了一千,達味殺了一萬」。
Amayiwo ankalandizana nyimbo mokondwera namati: “Sauli wapha 1,000, Koma Davide wapha miyandamiyanda.”
8 撒烏耳因此很是憤怒,這話使他很不高興,遂說:「給了根一萬,只給我一千;他所少的只有王位了!」
Koma Sauli anapsa mtima kwambiri ndipo mawu amenewa anamuyipira. Iye anati, “Iwo amuwerengera Davide miyandamiyanda, koma ine 1,000 okha. Nanga chatsalanso nʼchiyani kuti atenge? Si ufumu basi?”
9 從那一天起,撒烏耳常嫉視達味。
Ndipo kuyambira tsiku limeneli Sauli ankamuchitira nsanje Davide.
10 第二天,惡神由天主那裏降到撒烏耳身上;使他在屋中發狂。達味一如往日手中彈著琴,撒烏耳手中卻拿著一根長槍,
Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake.
11 撒烏耳舉起槍來,想把達味釘在牆上;達味已由他面前逃脫了兩次。
Tsono anawuponya mkondowo, namati mu mtima mwake, “Ndimubaya Davide ndi kumukhomera ku khoma.” Koma Davide anawulewa kawiri konse.
12 撒烏耳害怕達味,因為上主與達味同在,而離開了撒烏耳。
Pambuyo pake Sauli amamuopa Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo, nʼkumusiya Sauli.
13 因此,撒烏耳叫他離開自己,派他作千夫長,達味便在軍民前往來出入。
Kotero Sauli anamuchotsa Davide pamaso pake ndi kumuyika kukhala mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Choncho Davide ankapita ndi kubwera akutsogolera ankhondowa.
14 達味在所行的一切事上,無不順利,因為天主與他同在。
Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye.
15 撒烏耳見他辦事順利,就更疑懼他。
Sauli ataona momwe Davide ankapambanira, iye anamuopa kwambiri.
16 但全以色列和猶大人卻愛達味,因為他在他們前往來出入。
Koma Aisraeli onse ndi anthu a Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera pa nkhondo zawo.
17 撒烏耳對達味說:「看;我要把我的長女默辣布嫁給你為妻,只要你為我勇敢服務,為上主作戰」。──撒烏耳心中想:我不親手害他,讓培肋舍特人加害他。
Tsiku lina Sauli anawuza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkazi wamkulu. Ine ndakupatsa kuti umukwatire. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Yehova.” Poteropo Sauli ankanena kuti, “Ndisamuphe ndi manja angawa koma aphedwe ndi Afilisti!”
18 達味回答撒烏耳說:「我是誰,我父在以色列又算得什麼,我怎配作君王的女婿﹖」
Ndipo Davide anati kwa Sauli, “Ine ndine yani, ndipo abale anga kapena banja la abambo anga ndife yani mʼdziko la Israeli kuti ndikhale mpongozi wa mfumu?”
19 但是撒烏耳的女兒默辣布正要嫁給達味的時候,卻嫁給了默曷拉人阿德黎耳為妻。
Koma pa nthawi yoti Merabi mwana wa Sauli akwatiwe ndi Davide, Sauli anamupereka kwa Adrieli wa ku Mehola kuti amukwatire.
20 當時撒烏耳的女兒米加耳很愛達味;有人告訴了撒烏耳,他看這事好,
Koma Mikala mwana wamkazi wa Sauli anamukonda Davide ndipo Sauli atamva za zimenezi, anakondwera.
21 心想:「我把她嫁給達味,叫她成為他的羅網,藉培肋舍特人害他」。所以撒烏耳再次對達味說:「今天你要作我的女婿了! 」
Sauli ankaganiza kuti, “Ndimupatse amukwatire kuti akhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo adzaphedwe ndi Afilisti.” Choncho Sauli anawuza Davide kachiwiri, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.”
22 撒烏耳吩咐他的臣僕說:「你們暗暗地告訴達味說:看,君王多麼喜愛你,如今你要作君王的女婿了! 」
Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’”
23 撒烏耳的臣僕將這些話告訴了達味;達味反答說:「你們以為作君王的女婿軟碟件小事嗎﹖我不過是個貧窮賤卑賤的人」。
Iwo anakamuwuza Davide mawu amenewa, koma Davide anati, “Kodi inu mukuganiza kuti ndi chinthu chapafupi kukhala mpongozi wa mfumu? Ine ndine wosauka ndiponso wosatchuka.”
24 撒烏耳的臣僕回報王說:「達味如此如此說了」。
Nduna za Sauli zinamuwuza zonse zimene anayankha Davide.
25 撒烏耳答說:「你們要這樣對達味說:君王不要什麼聘禮,只要一百培培肋舍特人的包皮,為報復君王的仇敵」。撒烏耳有意使達味落在培肋舍特人手中。
Sauli anayankha kuti, “Kamuwuzeni Davide kuti, ‘Mfumu sikufuna malowolo a mtundu wina uliwonse koma timakungu ta msonga za mavalo a Afilisti 100 kuti ilipsire adani ake.’” Maganizo a Sauli anali akuti Davide aphedwe ndi Afilisti.
26 他的臣僕將這些話轉告給達味,達味看這事為作君王的女婿也對,所限的日期尚未過去,
Nduna za Saulizo zitamuwuza Davide zimenezi, anakondwera kuti akhale mpongozi wa mfumu. Koma nthawi imene anapatsidwa isanathe,
27 達味就和他的人起身去殺死了一百培肋舍特人,將他們的包皮帶回,足數交給君王,為作君王的女婿;撒烏耳就將女兒米加耳嫁給他為妻。
Davide ndi anyamata ake anapita ndi kukapha Afilisti 200. Iye anabwera ndi timakungu tija natipereka tonse kwa mfumu kuti akhale mpongozi wa mfumu. Kotero Sauli anapereka mwana wake wamkazi, Mikala, kwa Davide kuti amukwatire.
28 撒烏耳看出了上主與達味同在,全以色列也都愛他,
Sauli atazindikira kuti Yehova anali ndi Davide ndiponso kuti mwana wake Mikala amamukonda Davide,
29 從此更疑懼達味,終身與他為敵。
iye anapitirirabe kumuopa Davide ndi kumadana naye moyo wake wonse.
30 培肋舍特人的首領仍不斷出征;但每遇他們出征,達味所行的常比撒烏耳所有的臣僕成就更大,為此他更受人景仰。
Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri.

< 撒母耳記上 18 >