< Zefaniya 1 >

1 Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda.
Verbum Domini quod factum est ad Sophoniam, filium Chusi, filii Godoliæ, filii Amariæ, filii Ezeciæ, in diebus Josiæ, filii Amon, regis Judæ.
2 “Ndidzawononga kotheratu zinthu zonse pa dziko lapansi,” akutero Yehova.
Congregans congregabo omnia a facie terræ, dicit Dominus:
3 “Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe; ndidzawononga mbalame zamlengalenga ndi nsomba za mʼnyanja. Ndidzawononga anthu oyipa, ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,” akutero Yehova.
congregans hominem et pecus, congregans volatilia cæli et pisces maris: et ruinæ impiorum erunt, et disperdam homines a facie terræ, dicit Dominus.
4 Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda ndi onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala, mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano:
Et extendam manum meam super Judam et super omnes habitantes Jerusalem: et disperdam de loco hoc reliquias Baal, et nomina ædituorum cum sacerdotibus;
5 amene amagwada pa madenga a nyumba zawo kupembedza zolengedwa zamumlengalenga, amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova, komanso mʼdzina la Moleki,
et eos qui adorant super tecta militiam cæli, et adorant et jurant in Domino, et jurant in Melchom;
6 amene abwerera mʼmbuyo osatsata Yehova, osafunafuna kapena kupempha nzeru kwa Yehova.
et qui avertuntur de post tergum Domini, et qui non quæsierunt Dominum, nec investigaverunt eum.
7 Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova, chifukwa tsiku la Yehova layandikira. Yehova wakonzekera kupereka nsembe; wapatula iwo amene wawayitana.
Silete a facie Domini Dei, quia juxta est dies Domini: quia præparavit Dominus hostiam; sanctificavit vocatos suos.
8 Pa tsiku la nsembe ya Yehova ndidzalanga akalonga ndi ana aamuna a mfumu ndi onse amene amavala zovala zachilendo.
Et erit: in die hostiæ Domini, visitabo super principes, et super filios regis, et super omnes qui induti sunt veste peregrina;
9 Pa tsiku limenelo ndidzalanga onse amene safuna kuponda pa chiwundo, amene amadzaza nyumba ya ambuye awo ndi chiwawa ndi chinyengo.
et visitabo super omnem qui arroganter ingreditur super limen in die illa, qui complent domum Domini Dei sui iniquitate et dolo.
10 “Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova, “Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba, kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano, ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri.
Et erit in die illa, dicit Dominus, vox clamoris a porta piscium, et ululatus a Secunda, et contritio magna a collibus.
11 Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika; a malonda anu onse adzapululidwa, ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa.
Ululate, habitatores Pilæ: conticuit omnis populus Chanaan, disperierunt omnes involuti argento.
12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale ndi kulanga onse amene sakulabadira, amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa, amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse, chabwino kaya choyipa.’
Et erit in tempore illo: scrutabor Jerusalem in lucernis, et visitabo super viros defixos in fæcibus suis, qui dicunt in cordibus suis: Non faciet bene Dominus, et non faciet male.
13 Chuma chawo chidzafunkhidwa, nyumba zawo zidzagwetsedwa. Adzamanga nyumba, koma osakhalamo; adzadzala minda ya mpesa koma sadzamwako vinyo wake.”
Et erit fortitudo eorum in direptionem, et domus eorum in desertum: et ædificabunt domos, et non habitabunt; et plantabunt vineas, et non bibent vinum earum.
14 Tsiku lalikulu la Yehova layandikira, layandikira ndipo lifika msanga. Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa, ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri.
Juxta est dies Domini magnus: juxta est, et velox nimis. Vox diei Domini amara: tribulabitur ibi fortis.
15 Tsiku limenelo lidzakhala la ukali, tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni, tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko, tsiku la mdima ndi lachisoni, tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.
Dies iræ dies illa, dies tribulationis et angustiæ, dies calamitatis et miseriæ, dies tenebrarum et caliginis, dies nebulæ et turbinis,
16 Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo, tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwa ndi nsanja za pa ngodya.
dies tubæ et clangoris super civitates munitas, et super angulos excelsos.
17 Ndidzabweretsa msautso pa anthu ndipo adzayenda ngati anthu osaona, chifukwa achimwira Yehova, magazi awo adzamwazika ngati fumbi ndi mnofu wawo ngati ndowe.
Et tribulabo homines, et ambulabunt ut cæci, quia Domino peccaverunt; et effundetur sanguis eorum sicut humus, et corpora eorum sicut stercora.
18 Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Dziko lonse lapansi lidzanyeka mʼmoto wa nsanje yake chifukwa adzakantha modzidzimutsa onse okhala pa dziko lapansi.
Sed et argentum eorum et aurum eorum non poterit liberare eos in die iræ Domini: in igne zeli ejus devorabitur omnis terra, quia consummationem cum festinatione faciet cunctis habitantibus terram.

< Zefaniya 1 >