< Zefaniya 2 >

1 Sonkhanani pamodzi, sonkhanani pamodzi, inu mtundu wochititsa manyazi,
התקוששו וקושו--הגוי לא נכסף
2 isanafike nthawi yachiweruzo, nthawi yanu isanawuluke ngati mungu, usanakufikeni mkwiyo woopsa wa Yehova, tsiku la ukali wa Yehova lisanafike pa inu.
בטרם לדת חק כמץ עבר יום בטרם לא יבוא עליכם חרון אף יהוה--בטרם לא יבוא עליכם יום אף יהוה
3 Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko, inu amene mumachita zimene amakulamulani. Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa; mwina mudzatetezedwa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.
בקשו את יהוה כל ענוי הארץ אשר משפטו פעלו בקשו צדק בקשו ענוה--אולי תסתרו ביום אף יהוה
4 Gaza adzasiyidwa ndipo Asikeloni adzasanduka bwinja. Nthawi yamasana Asidodi adzakhala wopanda anthu ndipo Ekroni adzazulidwa.
כי עזה עזובה תהיה ואשקלון לשממה אשדוד בצהרים יגרשוה ועקרון תעקר
5 Tsoka inu okhala mʼmbali mwa nyanja, inu mtundu wa Akereti; mawu a Yehova akutsutsa iwe Kanaani, dziko la Afilisti. “Ndidzakuwononga ndipo palibe amene adzatsale.”
הוי ישבי חבל הים--גוי כרתים דבר יהוה עליכם כנען ארץ פלשתים והאבדתיך מאין יושב
6 Dziko la mʼmbali mwa nyanja, kumene kumakhala Akereti, lidzakhala malo a abusa ndi la makola a nkhosa.
והיתה חבל הים נות כרת רעים--וגדרות צאן
7 Malowa adzakhala a anthu otsala a nyumba ya Yuda; adzapezako msipu. Nthawi ya madzulo adzagona mʼnyumba za Asikeloni. Yehova Mulungu wawo adzawasamalira; adzabwezeretsa mtendere wawo.
והיה חבל לשארית בית יהודה--עליהם ירעון בבתי אשקלון בערב ירבצון--כי יפקדם יהוה אלהיהם ושב שבותם (שביתם)
8 “Ndamva kunyoza kwa Mowabu ndi chipongwe cha Amoni, amene ananyoza anthu anga ndi kuopseza kuti alanda dziko lawo.
שמעתי חרפת מואב וגדפי בני עמון--אשר חרפו את עמי ויגדילו על גבולם
9 Choncho, pali Ine Wamoyo,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, “Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu, Amoni adzasanduka ngati Gomora; malo a zomeramera ndi maenje a mchere, dziko la bwinja mpaka muyaya. Anthu anga otsala adzawafunkha; opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.”
לכן חי אני נאם יהוה צבאות אלהי ישראל כי מואב כסדם תהיה ובני עמון כעמרה ממשק חרול ומכרה מלח ושממה עד עולם שארית עמי יבזום ויתר גוי ינחלום
10 Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo, chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.
זאת להם תחת גאונם כי חרפו ויגדלו על עם יהוה צבאות
11 Yehova adzawachititsa mantha kwambiri pamene adzawononga milungu yonse ya mʼdzikomo. Ndipo mitundu ya anthu pa dziko lonse idzamulambira, uliwonse ku dziko la kwawo.
נורא יהוה עליהם כי רזה את כל אלהי הארץ וישתחוו לו איש ממקומו כל איי הגוים
12 “Inunso anthu a ku Kusi, mudzaphedwa ndi lupanga.”
גם אתם כושים חללי חרבי המה
13 Yehova adzatambasulira dzanja lake kumpoto ndi kuwononga Asiriya, kusiya Ninive atawonongekeratu ndi owuma ngati chipululu.
ויט ידו על צפון ויאבד את אשור וישם את נינוה לשממה ציה כמדבר
14 Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko, pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse. Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanungu adzakhala pa nsanamira zake. Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera, mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha, nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera.
ורבצו בתוכה עדרים כל חיתו גוי--גם קאת גם קפד בכפתריה ילינו קול ישורר בחלון חרב בסף כי ארזה ערה
15 Umenewu ndiye mzinda wosasamala umene kale unali wotetezedwa. Unkanena kuti mu mtima mwake, “Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.” Taonani lero wasanduka bwinja, kokhala nyama zakutchire! Onse owudutsa akuwunyoza ndi kupukusa mitu yawo.
זאת העיר העליזה היושבת לבטח האמרה בלבבה אני ואפסי עוד איך היתה לשמה מרבץ לחיה--כל עובר עליה ישרק יניע ידו

< Zefaniya 2 >