< Zekariya 9 >

1 Mawu a Yehova odzudzula dziko la Hadiraki ndi mzinda wa Damasiko pakuti maso a anthu ndiponso mafuko onse a Israeli ali pa Yehova—
מַשָּׂ֤א דְבַר־יְהוָה֙ בְּאֶ֣רֶץ חַדְרָ֔ךְ וְדַמֶּ֖שֶׂק מְנֻחָת֑וֹ כִּ֤י לַֽיהוָה֙ עֵ֣ין אָדָ֔ם וְכֹ֖ל שִׁבְטֵ֥י יִשְׂרָאֵֽל׃
2 ndiponso mzinda wa Hamati, umene ukuchita malire ndi dzikoli, komanso pa Turo ndi Sidoni, ngakhale kuti iwo ndi anzeru kwambiri.
וְגַם־חֲמָ֖ת תִּגְבָּל־בָּ֑הּ צֹ֣ר וְצִיד֔וֹן כִּ֥י חָֽכְמָ֖ה מְאֹֽד׃
3 Ndipo Turo anadzimangira linga; wadziwunjikira siliva ngati fumbi, ndi golide ngati zinyalala za mʼmisewu.
וַתִּ֥בֶן צֹ֛ר מָצ֖וֹר לָ֑הּ וַתִּצְבָּר־כֶּ֙סֶף֙ כֶּֽעָפָ֔ר וְחָר֖וּץ כְּטִ֥יט חוּצֽוֹת׃
4 Taonani Ambuye adzamulanda chuma chakecho ndi kuwononga mphamvu zake mʼnyanja, ndipo adzapserera ndi moto.
הִנֵּ֤ה אֲדֹנָי֙ יֽוֹרִשֶׁ֔נָּה וְהִכָּ֥ה בַיָּ֖ם חֵילָ֑הּ וְהִ֖יא בָּאֵ֥שׁ תֵּאָכֵֽל׃
5 Mzinda wa Asikeloni udzaona zimenezi, nʼkuchita mantha; Gaza adzanjenjemera ndi ululu, chimodzimodzinso Ekroni, chifukwa chiyembekezo chake chidzatheratu. Mfumu ya ku Gaza idzaphedwa ndipo Asikeloni adzakhala opanda anthu.
תֵּרֶ֨א אַשְׁקְל֜וֹן וְתִירָ֗א וְעַזָּה֙ וְתָחִ֣יל מְאֹ֔ד וְעֶקְר֖וֹן כִּֽי־הֹבִ֣ישׁ מֶבָּטָ֑הּ וְאָ֤בַד מֶ֙לֶךְ֙ מֵֽעַזָּ֔ה וְאַשְׁקְל֖וֹן לֹ֥א תֵשֵֽׁב׃
6 Mu Asidodi mudzakhala mlendo, ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisti.
וְיָשַׁ֥ב מַמְזֵ֖ר בְּאַשְׁדּ֑וֹד וְהִכְרַתִּ֖י גְּא֥וֹן פְּלִשְׁתִּֽים׃
7 Ndidzachotsa nyama ya magazi mʼkamwa mwawo, chakudya choletsedwa mʼmano mwawo. Amene atsala adzakhala anthu a Mulungu wathu, adzasanduka atsogoleri mu Yuda, ndipo Ekroni adzakhala ngati Ayebusi.
וַהֲסִרֹתִ֨י דָמָ֜יו מִפִּ֗יו וְשִׁקֻּצָיו֙ מִבֵּ֣ין שִׁנָּ֔יו וְנִשְׁאַ֥ר גַּם־ה֖וּא לֵֽאלֹהֵ֑ינוּ וְהָיָה֙ כְּאַלֻּ֣ף בִּֽיהוּדָ֔ה וְעֶקְר֖וֹן כִּיבוּסִֽי׃
8 Koma Ine ndidzalondera Nyumba yanga ndi kuyiteteza kwa ankhondo osakaza. Palibenso mdani amene adzagonjetse anthu anga, pakuti tsopano ndikuwayangʼanira.
וְחָנִ֨יתִי לְבֵיתִ֤י מִצָּבָה֙ מֵעֹבֵ֣ר וּמִשָּׁ֔ב וְלֹֽא־יַעֲבֹ֧ר עֲלֵיהֶ֛ם ע֖וֹד נֹגֵ֑שׂ כִּ֥י עַתָּ֖ה רָאִ֥יתִי בְעֵינָֽי׃ ס
9 Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni! Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu! Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yolungama ndi yogonjetsa adani, yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu, pa mwana wamphongo wa bulu.
גִּילִ֨י מְאֹ֜ד בַּת־צִיּ֗וֹן הָרִ֙יעִי֙ בַּ֣ת יְרוּשָׁלִַ֔ם הִנֵּ֤ה מַלְכֵּךְ֙ יָ֣בוֹא לָ֔ךְ צַדִּ֥יק וְנוֹשָׁ֖ע ה֑וּא עָנִי֙ וְרֹכֵ֣ב עַל־חֲמ֔וֹר וְעַל־עַ֖יִר בֶּן־אֲתֹנֽוֹת׃
10 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efereimu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu, ndipo uta wankhondo udzathyoka. Mfumuyo idzabweretsa mtendere pakati pa mitundu ya anthu. Ulamuliro wake udzayambira ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndipo kuchokera ku Mtsinje (Yufurate) mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
וְהִכְרַתִּי־רֶ֣כֶב מֵאֶפְרַ֗יִם וְסוּס֙ מִיר֣וּשָׁלִַ֔ם וְנִכְרְתָה֙ קֶ֣שֶׁת מִלְחָמָ֔ה וְדִבֶּ֥ר שָׁל֖וֹם לַגּוֹיִ֑ם וּמָשְׁלוֹ֙ מִיָּ֣ם עַד־יָ֔ם וּמִנָּהָ֖ר עַד־אַפְסֵי־אָֽרֶץ׃
11 Tsono kunena za iwe, chifukwa cha magazi a pangano lako ndi Ine, ndidzamasula amʼndende ako, ndidzawatulutsa mʼdzenje lopanda madzi.
גַּם־אַ֣תְּ בְּדַם־בְּרִיתֵ֗ךְ שִׁלַּ֤חְתִּי אֲסִירַ֙יִךְ֙ מִבּ֔וֹר אֵ֥ין מַ֖יִם בּֽוֹ׃
12 Bwererani ku malo anu otetezedwa, inu amʼndende achiyembekezo; ngakhale tsopano ndikulengeza kuti ndidzakubwezerani zabwino mowirikiza.
שׁ֚וּבוּ לְבִצָּר֔וֹן אֲסִירֵ֖י הַתִּקְוָ֑ה גַּם־הַיּ֕וֹם מַגִּ֥יד מִשְׁנֶ֖ה אָשִׁ֥יב לָֽךְ׃
13 Ndidzakoka Yuda monga ndimakokera uta wanga, ndipo Efereimu ndiye muvi wake. Ndidzadzutsa ana ako iwe Ziyoni, kulimbana ndi ana ako iwe Grisi, ndipo ndidzakusandutsa iwe lupanga la munthu wankhondo.
כִּֽי־דָרַ֨כְתִּי לִ֜י יְהוּדָ֗ה קֶ֚שֶׁת מִלֵּ֣אתִי אֶפְרַ֔יִם וְעוֹרַרְתִּ֤י בָנַ֙יִךְ֙ צִיּ֔וֹן עַל־בָּנַ֖יִךְ יָוָ֑ן וְשַׂמְתִּ֖יךְ כְּחֶ֥רֶב גִּבּֽוֹר׃
14 Pamenepo Yehova adzaonekera kwa anthu ake; mivi yake idzangʼanima ngati chingʼaningʼani. Ambuye Yehova adzaliza lipenga; ndipo adzayenda mu mkuntho wochokera kummwera,
וַֽיהוָה֙ עֲלֵיהֶ֣ם יֵֽרָאֶ֔ה וְיָצָ֥א כַבָּרָ֖ק חִצּ֑וֹ וַֽאדֹנָ֤י יְהֹוִה֙ בַּשּׁוֹפָ֣ר יִתְקָ֔ע וְהָלַ֖ךְ בְּסַעֲר֥וֹת תֵּימָֽן׃
15 ndipo Yehova Wamphamvuzonse adzawateteza. Iwo adzawononga ndipo adzagonjetsa ndi miyala ya legeni. Adzamwa magazi ndi kubangula ngati amwa vinyo; magazi adzayenderera ngati a mʼmbale yowazira magazi pa ngodya za guwa lansembe.
יְהוָ֣ה צְבָאוֹת֮ יָגֵ֣ן עֲלֵיהֶם֒ וְאָכְל֗וּ וְכָֽבְשׁוּ֙ אַבְנֵי־קֶ֔לַע וְשָׁת֥וּ הָמ֖וּ כְּמוֹ־יָ֑יִן וּמָֽלְאוּ֙ כַּמִּזְרָ֔ק כְּזָוִיּ֖וֹת מִזְבֵּֽחַ׃
16 Tsiku limenelo Yehova Mulungu wawo adzawapulumutsa pakuti anthu ake ali ngati nkhosa. Adzanyezimira mʼdziko lake ngati miyala yokongola pa chipewa chaufumu.
וְֽהוֹשִׁיעָ֞ם יְהוָ֧ה אֱלֹהֵיהֶ֛ם בַּיּ֥וֹם הַה֖וּא כְּצֹ֣אן עַמּ֑וֹ כִּ֚י אַבְנֵי־נֵ֔זֶר מִֽתְנוֹסְס֖וֹת עַל־אַדְמָתֽוֹ ׃
17 Taonani chikoka ndi kukongola kwawo! Tirigu adzasangalatsa anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.
כִּ֥י מַה־טּוּב֖וֹ וּמַה־יָפְי֑וֹ דָּגָן֙ בַּֽחוּרִ֔ים וְתִיר֖וֹשׁ יְנוֹבֵ֥ב בְּתֻלֽוֹת׃

< Zekariya 9 >