< Zekariya 8 >

1 Awa ndi mawu amene Yehova Wamphamvuzonse ananena.
The word of Yahweh of Armies came to me.
2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikuchitira nsanje yayikulu Ziyoni. Mtima wanga ukupweteka chifukwa cha nsanje pa iyeyo.”
Yahweh of Armies says: “I am jealous for Zion with great jealousy, and I am jealous for her with great wrath.”
3 Yehova akuti, “Ndidzabwerera ku Ziyoni ndi kukakhala ku Yerusalemu. Pamenepo Yerusalemu adzatchedwa Mzinda wa Choonadi ndipo phiri la Yehova Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Lopatulika.”
Yahweh says: “I have returned to Zion, and will dwell in the middle of Jerusalem. Jerusalem shall be called ‘The City of Truth;’ and the mountain of Yahweh of Armies, ‘The Holy Mountain.’”
4 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Abambo ndi amayi okalamba adzakhalanso mʼmisewu ya mu Yerusalemu, aliyense ali ndi ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha kuchuluka kwa masiku ake.
Yahweh of Armies says: “Old men and old women will again dwell in the streets of Jerusalem, every man with his staff in his hand because of their old age.
5 Ndipo misewu ya mu mzindamo idzadzaza ndi anyamata ndi atsikana akusewera.”
The streets of the city will be full of boys and girls playing in its streets.”
6 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Yahweh of Armies says: “If it is marvelous in the eyes of the remnant of this people in those days, should it also be marvelous in my eyes?” says Yahweh of Armies.
7 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani ndidzapulumutsa anthu anga kuchokera ku mayiko a kummawa ndi kumadzulo.
Yahweh of Armies says: “Behold, I will save my people from the east country and from the west country.
8 Ndidzawabweretsa kuti adzakhale mu Yerusalemu; adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, wokhulupirika ndi wolungama pakati pawo.”
I will bring them, and they will dwell within Jerusalem. They will be my people, and I will be their God, in truth and in righteousness.”
9 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Inu amene tsopano mukumva mawu awa amene akuyankhula aneneri amene analipo pamene ankayika maziko a nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, ‘limbani mtima kuti mumange Nyumba ya Yehova.’
Yahweh of Armies says: “Let your hands be strong, you who hear in these days these words from the mouth of the prophets who were in the day that the foundation of the house of Yahweh of Armies was laid, even the temple, that it might be built.
10 Mpaka nthawi imeneyi panalibe munthu wolandira malipiro pa ntchito kapena ndalama zolipirira nyama zogwira ntchito. Panalibe munthu amene ankadzigwirira ntchito mwamtendere chifukwa choopa adani ake, pakuti Ine ndinkawayambanitsa.
For before those days there was no wages for man nor any wages for an animal, neither was there any peace to him who went out or came in, because of the adversary. For I set all men everyone against his neighbor.
11 Koma tsopano sindidzachitira otsala mwa anthu awa zomwe ndinachita kale,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
But now I will not be to the remnant of this people as in the former days,” says Yahweh of Armies.
12 “Pakuti mbewu zidzamera bwino, mpesa udzabala zipatso zake, nthaka idzatulutsa zomera zake, ndi thambo lidzagwetsa mame. Ndidzapereka zonse kukhala cholowa cha otsala mwa anthu awa.
“For the seed of peace and the vine will yield its fruit, and the ground will give its increase, and the heavens will give their dew. I will cause the remnant of this people to inherit all these things.
13 Monga mwakhala muli chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu ina ya anthu, inu Yuda ndi Israeli, choncho ndidzakupulumutsani, ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha, koma limbani mtima.”
It shall come to pass that, as you were a curse among the nations, house of Judah and house of Israel, so I will save you, and you shall be a blessing. Don’t be afraid. Let your hands be strong.”
14 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Monga ndinatsimikiza mtima kubweretsa choyipa pa inu, komanso osakuchitirani chisoni pamene makolo anu anandikwiyitsa,” akutero Yehova,
For Yahweh of Armies says: “As I thought to do evil to you when your fathers provoked me to wrath,” says Yahweh of Armies, “and I didn’t repent,
15 “Choncho tsopano ndatsimikiza mtima kuchitiranso zabwino Yerusalemu ndi Yuda. Musachite mantha.
so again I have thought in these days to do good to Jerusalem and to the house of Judah. Don’t be afraid.
16 Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu;
These are the things that you shall do: speak every man the truth with his neighbor. Execute the judgment of truth and peace in your gates,
17 musamachitire mnzanu chiwembu, musamakonde kulumbira zonama. Zonsezi Ine ndimadana nazo,” akutero Yehova.
and let none of you devise evil in your hearts against his neighbor, and love no false oath; for all these are things that I hate,” says Yahweh.
18 Yehova Wamphamvuzonse anayankhulanso nane.
The word of Yahweh of Armies came to me.
19 Ndipo ananena kuti, “Kusala zakudya kwa pa mwezi wachinayi, chisanu, chisanu ndi chiwiri ndi wakhumi, kudzakhala nthawi yachimwemwe, ya chisangalalo ndi nthawi ya madyerero chikondwerero kwa Yuda. Nʼchifukwa chake muzikonda choonadi ndi mtendere.”
Yahweh of Armies says: “The fasts of the fourth, fifth, seventh, and tenth months shall be for the house of Judah joy, gladness, and cheerful feasts. Therefore love truth and peace.”
20 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a mitundu yambiri ndi anthu okhala mʼmizinda yambiri adzabwerabe,
Yahweh of Armies says: “Many peoples and the inhabitants of many cities will yet come.
21 ndipo nzika za mzinda wina zidzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe madalitso kwa Yehova ndi kukapembedza Yehova Wamphamvuzonse. Inenso ndikupita kumeneko.’
The inhabitants of one will go to another, saying, ‘Let’s go speedily to entreat the favor of Yahweh, and to seek Yahweh of Armies. I will go also.’
22 Anthu ambiri ndiponso a ku mayiko amphamvu adzabwera ku Yerusalemu kudzapembedza Yehova Wamphamvuzonse ndi kudzapempha madalitso.”
Yes, many peoples and strong nations will come to seek Yahweh of Armies in Jerusalem and to entreat the favor of Yahweh.”
23 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’”
Yahweh of Armies says: “In those days, ten men out of all the languages of the nations will take hold of the skirt of him who is a Jew, saying, ‘We will go with you, for we have heard that God is with you.’”

< Zekariya 8 >