< Zekariya 7 >

1 Pa chaka chachinayi cha Mfumu Dariyo, pa tsiku lachinayi la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi Zekariya.
Katika mwaka wa nne wa utawala wa Mfalme Dario, neno la Bwana lilimjia Zekaria siku ya nne ya mwezi wa tisa, mwezi wa Kisleu.
2 Anthu a ku Beteli anali atatuma Sarezeri ndi Regemu-Meleki pamodzi ndi anthu awo, kuti akapemphe chifundo kwa Yehova
Watu wa Betheli walikuwa wamemtuma Shareza na Regem-Meleki pamoja na watu wao, kumsihi Bwana
3 pokafunsa kwa ansembe a ku Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse ndi aneneri kuti, “Kodi ine ndizilira ndi kusala zakudya pa mwezi wachisanu, monga mmene ndakhala ndikuchitira pa zaka zambiri?”
kwa kuwauliza makuhani wa nyumba ya Bwana Mwenye Nguvu Zote na manabii, “Je, imempasa kuomboleza na kufunga katika mwezi wa tano, kama ambavyo nimekuwa nikifanya kwa miaka mingi?”
4 Pamenepo Yehova Wamphamvuzonse anayankhula nane kuti,
Kisha neno la Bwana Mwenye Nguvu Zote likanijia kusema:
5 “Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine?
“Waulize watu wote wa nchi na makuhani, ‘Je, mlipofunga na kuomboleza katika mwezi wa tano na wa saba kwa miaka sabini iliyopita, mlifunga kweli kwa ajili yangu?
6 Ndipo pamene munkadya ndi kumwa, kodi simunkachita zimenezi podzisangalatsa nokha?
Na mlipokuwa mkila na kunywa, je, hamkuwa mnasherehekea kwa ajili ya nafsi zenu?
7 Kodi awa si mawu amene Yehova ankanena kudzera mwa aneneri oyamba aja pamene Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira anali pa mtendere ndi pa ulemerero, ndi pamene Negevi ndi ku madera akumadzulo a mʼmbali mwa phiri munali anthu?’”
Je, haya sio maneno ya Bwana aliyosema kupitia manabii waliotangulia, wakati Yerusalemu pamoja na miji inayoizunguka ilipokuwa katika hali ya utulivu na ya mafanikio, wakati Negebu na Shefala zikiwa zimekaliwa na watu?’”
8 Ndipo Yehova anayankhulanso ndi Zekariya kuti,
Neno la Bwana likamjia tena Zekaria:
9 “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni.
“Hivi ndivyo asemavyo Bwana Mwenye Nguvu Zote: ‘Fanyeni hukumu za haki, onyesheni rehema na huruma ninyi kwa ninyi.
10 Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’
Msimwonee mjane wala yatima, mgeni wala maskini. Msiwaziane mabaya mioyoni mwenu ninyi kwa ninyi.’
11 “Koma makolo anu anakana kumvera uthenga umenewu; anawumitsa mtima nandifulatira, natseka makutu awo kuti asamve.
“Lakini wakakataa kusikiliza, wakanipa kisogo kwa ukaidi na kuziba masikio yao.
12 Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri.
Wakaifanya mioyo yao migumu kama jiwe gumu na hawakuisikiliza sheria au maneno ambayo Bwana Mwenye Nguvu Zote aliyatuma kwa njia ya Roho wake kupitia manabii waliotangulia. Kwa hiyo Bwana Mwenye Nguvu Zote alikasirika sana.
13 “‘Pamene ndinawayitana, iwo sanamvere; choncho pamene iwo anandiyitana, Ine sindinamverenso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“‘Wakati nilipoita, hawakusikiliza, kwa hiyo walipoita, sikusikiliza,’ asema Bwana Mwenye Nguvu Zote.
14 ‘Ndinawamwaza ndi kamvuluvulu pakati pa mitundu yonse ya anthu, kumene anali alendo. Dziko lawo linatsala litasakazidwa kwambiri kotero kuti palibe amene amabwera kapena kupitamo. Umu ndi mmene anasandutsira dziko labwino kukhala chipululu.’”
‘Niliwatawanya kwa upepo wa kisulisuli miongoni mwa mataifa yote, mahali ambapo walikuwa wageni. Nchi ikaachwa ukiwa nyuma yao kiasi kwamba hakuna aliyeweza kuingia au kutoka. Hivi ndivyo walivyoifanya ile nchi iliyokuwa imependeza kuwa ukiwa.’”

< Zekariya 7 >