< Zekariya 3 >
1 Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye.
2 Yehova anawuza Satana kuti, “Yehova akukudzudzula iwe Satana! Yehova amene wasankha Yerusalemu akukudzudzula! Kodi munthu uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”
3 Tsono Yoswa anali atavala zovala zalitsiro pa nthawi imene anayima pamaso pa mngelo.
4 Mngelo uja anawuza anzake amene anali naye kuti, “Muvuleni zovala zake zalitsirizo.” Kenaka anawuza Yoswa kuti, “Taona, ndachotsa tchimo lako, ndipo ndikuveka zovala zokongola.”
5 Ndipo ine ndinati, “Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake.” Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali.
6 Mngelo wa Yehova analimbikitsa Yoswa kuti,
7 “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa.
8 “‘Mvera tsono, iwe Yoswa mkulu wa ansembe, pamodzi ndi anzako amene wakhala nawowa, amene ndi chizindikiro cha zinthu zimene zikubwera: Ine ndidzabweretsa mtumiki wanga, wotchedwa Nthambi.
9 Taona, mwala wokongola umene ndayika patsogolo pa Yoswa! Pa mwala umenewu pali maso asanu ndi awiri, ndipo Ine ndidzalembapo mawu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndipo ndidzachotsa tchimo la dziko lino tsiku limodzi.
10 “‘Tsiku limenelo aliyense adzayitana mnzake kuti akhale pansi pa mtengo wamphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”