< Zekariya 11 >
1 Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni, kuti moto unyeketse mikungudza yako!
Otvori vrata, Libanone, nek' ti oganj sažeže cedrove!
2 Lira mwachisoni, iwe mtengo wa payini, pakuti mkungudza wagwa; mtengo wamphamvu wawonongeka! Lirani mwachisoni, inu mitengo ya thundu ya Basani; nkhalango yowirira yadulidwa!
Kukaj, čempresu, jer pade cedar, jer su mogućnici upropašteni! Kukajte, hrastovi bašanski, jer posječena je šuma najgušća.
3 Imvani kulira mwachisoni kwa abusa; msipu wawo wobiriwira wawonongeka! Imvani kubangula kwa mikango; nkhalango yowirira ya ku Yorodani yawonongeka!
Čuj jauk pastira, opustošen je sjaj njihov! Čuj riku lavića, opustošen je ponos jordanski!
4 Yehova Mulungu wanga akuti, “Dyetsa nkhosa zimene zikukaphedwa.
Ovako mi reče Jahve:
5 Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo.
“Pasi ovce klanice! Kupci ih njihovi kolju nekažnjeno, a koji ih prodaju, govore: 'Blagoslovljen bio Jahve, obogatio sam se!' i pastiri ih njihovi ne štede.
6 Pakuti Ine sindidzamveranso chisoni anthu okhala mʼdziko,” akutero Yehova. “Ndidzapereka munthu aliyense mʼmanja mwa mnansi wake ndi mwa mfumu yake. Iwo adzazunza dziko, ndipo Ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.”
Ni ja više neću štedjeti žitelja zemlje - riječ je Jahve nad Vojskama - nego: predajem, evo, svakoga u ruke njegova bližnjega i u ruke kralja njegova; i oni će pustošiti zemlju, a ja neću izbavljati iz ruku njihovih.”
7 Choncho ine ndinadyetsa nkhosa zokaphedwa, makamaka nkhosa zoponderezedwa. Pamenepo ndinatenga ndodo ziwiri ndipo yoyamba ndinayitcha Kukoma mtima ndipo yachiwiri ndinayitcha Umodzi ndipo ndinadyetsa nkhosazo.
Stadoh pasti ovce klanice za trgovce ovcama te uzeh dva štapa: jedan nazvah Naklonost, drugi Sveza. Tako sam pasao stado.
8 Pa mwezi umodzi ndinachotsa abusa atatu. Abusawo anadana nane, ndipo ndinatopa nawo.
I u jednom mjesecu odbacih tri pastira. Ali mi i ovce dojadiše, omrznuh im.
9 Ndinawuza gulu la nkhosalo kuti, “Sindidzakhalanso mʼbusa wanu. Imene ikufa, ife, ndipo imene ikuwonongeka, iwonongeke, zimene zatsala zizidyana.”
Tad rekoh: “Neću vas više pasti! Koja mora uginuti, nek' ugine! Koja mora nestati, nek' nestane! A koje ostanu, neka jedna drugoj meso prožderu!”
10 Kenaka ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Kukoma mtima ndi kuyithyola, kuphwanya pangano limene ndinachita ndi mitundu yonse ya anthu.
Tad uzeh svoj štap Naklonost i slomih ga da raskinem Savez svoj što ga bijah sklopio sa svim narodima.
11 Linaphwanyidwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zosautsidwa zimene zimandiyangʼanitsitsa zinadziwa kuti anali mawu a Yehova.
I on se raskinu onog dana, i trgovci ovcama koji su to gledali doznaše da je to bila riječ Jahvina.
12 Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
Rekoh im tad: “Ako vam je to dobro, dajte mi plaću; ako nije, nemojte.” Oni mi odmjeriše plaću: trideset srebrnika.
13 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.
A Jahve mi reče: “Baci u riznicu tu lijepu cijenu kojom su me procijenili!” Ja uzeh trideset srebrnika i bacih u riznicu u Domu Jahvinu.
14 Kenaka ndinathyola ndodo yanga yachiwiri yotchedwa Umodzi, kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israeli.
Onda slomih i svoj drugi štap, Svezu - da raskinem bratstvo između Jude i Izraela.
15 Pamenepo Yehova anayankhula nane kuti, “Tenganso zida za mʼbusa wopusa.
I reče mi Jahve: “Uzmi još opremu bezumna pastira,
16 Pakuti ndidzawutsa mʼbusa mʼdzikomo amene sadzasamalira zotayika, kapena kufunafuna zazingʼono, kapena zovulala, kapena kudyetsa nkhosa zabwino, koma iye adzadya nyama ya nkhosa zonenepa, nʼkumakukuta ndi ziboda zomwe.
jer, evo, podići ću jednoga bezumnog pastira u ovoj zemlji: za izgubljene on se neće brinuti, zalutale neće tražiti, ranjene neće vidati, iscrpljene neće nositi, nego će jesti meso od pretilih i papke im otkidati.
17 “Tsoka kwa mʼbusa wopandapake, amene amasiya nkhosa! Lupanga limukanthe pa mkono wake ndi pa diso lake lakumanja! Mkono wake ufote kotheratu, diso lake lamanja lisaonenso.”
Teško pastiru opakom koji stado ostavlja! Neka mu mač stigne ruku i desno oko! Nek' mu desnica sasvim usahne, oko desno sasvim potamni!”