< Zekariya 1 >
1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti:
Au huitième mois de la deuxième année de Darius, la parole de l'Éternel fut adressée au prophète Zacharie, fils de Bérékia, fils d'Iddo, en ces termes:
2 “Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu.
L'Éternel a été très mécontent de vos pères.
3 Choncho awuze anthuwa kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Bwererani kwa Ine,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
C'est pourquoi tu leur diras: L'Éternel des armées dit: « Revenez à moi, dit l'Éternel des armées, et je reviendrai à vous », dit l'Éternel des armées.
4 Musakhale ngati makolo anu, amene aneneri akale anawalalikira kuti: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Tsopano lekani njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu oyipawo.’ Koma iwo sanamvere kapena kulabadira za Ine, akutero Yehova.
Ne soyez pas comme vos pères, à qui les anciens prophètes ont annoncé, en disant: L'Éternel des armées dit: « Revenez maintenant de vos mauvaises voies et de vos mauvaises actions »; mais ils n'ont pas écouté et ne m'ont pas écouté, dit l'Éternel.
5 Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya?
Vos pères, où sont-ils? Et les prophètes, vivent-ils éternellement?
6 Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu? “Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’”
Mais mes paroles et mes décrets, que j'ai prescrits à mes serviteurs les prophètes, n'ont-ils pas atteint vos pères? Ils se repentirent et dirent: « Ce que Yahvé des armées avait décidé de nous faire, selon nos voies et nos pratiques, il l'a fait avec nous ».
7 Tsiku la 24 la mwezi wa 11, mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido.
Le vingt-quatrième jour du onzième mois, qui est le mois de Shebat, la deuxième année de Darius, la parole de Yahvé fut adressée au prophète Zacharie, fils de Béréchia, fils d'Iddo, en ces termes:
8 Nthawi ya usiku ndinaona masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Iye anayima pakati pa mitengo ya mchisu mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali akavalo ofiira, akhofi ndi oyera.
« J'ai eu une vision pendant la nuit: voici un homme monté sur un cheval roux, qui se tenait parmi les myrtes qui étaient dans un ravin; et derrière lui, il y avait des chevaux roux, bruns et blancs.
9 Ine ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi ndi chiyani?” Mngelo amene amayankhula nane anayankha kuti, “Ndidzakuonetsa kuti zimenezi ndi chiyani.”
Je demandai alors: « Mon seigneur, qu'est-ce que c'est? » L'ange qui m'a parlé m'a dit: « Je vais te montrer ce que c'est. »
10 Pamenepo munthu amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu anafotokoza kuti, “Amenewa ndiwo amene Yehova wawatuma kuti ayendere dziko lonse lapansi.”
L'homme qui se tenait parmi les myrtes répondit: « Ce sont ceux que Yahvé a envoyés pour aller et venir sur la terre. »
11 Ndipo okwera pa akavalo enawo anafotokoza kwa mngelo wa Yehova, amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu kuti, “Ife tayendera dziko lonse lapansi ndipo tapeza kuti dziko lonselo lili pa bata ndi mtendere.”
Ils firent leur rapport à l'ange de Yahvé qui se tenait parmi les myrtes, et dirent: « Nous avons parcouru la terre de long en large, et voici que toute la terre est en repos et en paix. »
12 Tsono mngelo wa Yehova anati, “Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?”
L'ange de Yahvé répondit: « Yahvé des armées, jusqu'à quand n'auras-tu pas pitié de Jérusalem et des villes de Juda, contre lesquelles tu t'es indigné pendant soixante-dix ans? »
13 Choncho Yehova anayankhula mawu abwino ndi achitonthozo kwa mngelo amene ankayankhula nane.
Yahvé répondit à l'ange qui me parlait par des paroles aimables et réconfortantes.
14 Pamenepo mngelo amene ankayankhula nane anati, “Lengeza mawu awa: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndikuchitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni,
L'ange qui m'a parlé m'a dit: « Proclame, en disant: « L'Éternel des armées dit: « Je suis jaloux de Jérusalem et de Sion, d'une grande jalousie.
15 koma ndakwiya kwambiri ndi anthu a mitundu ina amene akuganiza kuti ali pa mtendere. Ndinakwiyira anthu anga pangʼono pokha, koma iwo anawonjeza kuzunza anthu angawo.’
Je suis très irrité contre les nations qui sont à l'aise; car je n'étais qu'un peu mécontent, mais elles ont ajouté à la calamité. »
16 “Choncho, Yehova akuti, ‘Ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo, nyumba yanga adzayimanganso kumeneko. Ndipo adzatenganso chingwe choyezera kuti amange Yerusalemu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
C'est pourquoi Yahvé dit: « Je suis revenu à Jérusalem avec miséricorde. Ma maison y sera bâtie, dit Yahvé des armées, et une ligne sera tendue sur Jérusalem. »"
17 “Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’”
« Proclamez encore, en disant: « Yahvé des armées dit: « Mes villes regorgeront de nouveau de prospérité, et Yahvé consolera de nouveau Sion, et choisira de nouveau Jérusalem »".
18 Kenaka ndinayangʼananso, ndipo patsogolo panga panali nyanga zinayi.
Je levai les yeux et je vis, et voici, il y avait quatre cornes.
19 Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi ndi chiyani?” Iye anandiyankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu.”
Je demandai à l'ange qui parlait avec moi: « Qu'est-ce que c'est? » Il me répondit: « Ce sont les cornes qui ont dispersé Juda, Israël et Jérusalem. »
20 Kenaka Yehova anandionetsa amisiri azitsulo anayi.
Yahvé me montra quatre artisans.
21 Ndinafunsa kuti, “Amisiri a zitsulowa akudzachita chiyani?” Iye anayankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda kotero kuti panalibe wina amene akanalimbana nazo, koma amisiri a zitsulowa abwera kudzaziopseza ndi kugwetsa nyanga zimenezi za mitundu ya anthu amene analimbana ndi dziko la Yuda ndi kubalalitsa anthu ake.”
Et j'ai demandé: « Que viennent-ils faire? » Il dit: « Ce sont les cornes qui ont dispersé Juda, de sorte que personne n'a levé la tête; mais celles-ci sont venues pour les terrifier, pour abattre les cornes des nations qui ont levé leur corne contre le pays de Juda pour le disperser. »