< Tito 3 >
1 Uwakumbutse anthu kuti azigonjera oweruza ndi olamulira, aziwamvera ndi kukhala okonzeka kuchita chilichonse chabwino.
υπομιμνησκε αυτουσ αρχαισ και εξουσιαισ υποτασσεσθαι πειθαρχειν προσ παν εργον αγαθον ετοιμουσ ειναι
2 Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
μηδενα βλασφημειν αμαχουσ ειναι επιεικεισ πασαν ενδεικνυμενουσ πραοτητα προσ παντασ ανθρωπουσ
3 Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake.
ημεν γαρ ποτε και ημεισ ανοητοι απειθεισ πλανωμενοι δουλευοντεσ επιθυμιαισ και ηδοναισ ποικιλαισ εν κακια και φθονω διαγοντεσ στυγητοι μισουντεσ αλληλουσ
4 Koma kukoma mtima ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chitaonekera,
οτε δε η χρηστοτησ και η φιλανθρωπια επεφανη του σωτηροσ ημων θεου
5 Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera
ουκ εξ εργων των εν δικαιοσυνη ων εποιησαμεν ημεισ αλλα κατα τον αυτου ελεον εσωσεν ημασ δια λουτρου παλιγγενεσιασ και ανακαινωσεωσ πνευματοσ αγιου
6 amene anatipatsa mowolowamanja kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu,
ου εξεχεεν εφ ημασ πλουσιωσ δια ιησου χριστου του σωτηροσ ημων
7 kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (aiōnios )
ινα δικαιωθεντεσ τη εκεινου χαριτι κληρονομοι γενωμεθα κατ ελπιδα ζωησ αιωνιου (aiōnios )
8 Mawuwa ndi okhulupirika ndipo ine ndikufuna kuti iwe utsindike zinthu izi, kuti amene akhulupirira Mulungu adzipereke kuchita ntchito zabwino. Zinthu izi ndi zabwino kwambiri ndi zopindulitsa kwa aliyense.
πιστοσ ο λογοσ και περι τουτων βουλομαι σε διαβεβαιουσθαι ινα φροντιζωσιν καλων εργων προιστασθαι οι πεπιστευκοτεσ θεω ταυτα εστιν τα καλα και ωφελιμα τοισ ανθρωποισ
9 Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kuwerengawerenga mndandanda wa mibado ya makolo, mikangano ndi mitsutso pa za Malamulo, chifukwa zimenezi ndi zosapindulitsa ndi zopanda pake.
μωρασ δε ζητησεισ και γενεαλογιασ και ερεισ και μαχασ νομικασ περιιστασο εισιν γαρ ανωφελεισ και ματαιοι
10 Munthu woyambitsa mipatuko umuchenjeze koyamba, ndiponso umuchenjeze kachiwiri. Kenaka umupewe.
αιρετικον ανθρωπον μετα μιαν και δευτεραν νουθεσιαν παραιτου
11 Iwe udziwe kuti munthu wotero ngosokoneza ndi wochimwa, ndipo akudzitsutsa yekha.
ειδωσ οτι εξεστραπται ο τοιουτοσ και αμαρτανει ων αυτοκατακριτοσ
12 Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira.
οταν πεμψω αρτεμαν προσ σε η τυχικον σπουδασον ελθειν προσ με εισ νικοπολιν εκει γαρ κεκρικα παραχειμασαι
13 Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu.
ζηναν τον νομικον και απολλω σπουδαιωσ προπεμψον ινα μηδεν αυτοισ λειπη
14 Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.
μανθανετωσαν δε και οι ημετεροι καλων εργων προιστασθαι εισ τασ αναγκαιασ χρειασ ινα μη ωσιν ακαρποι
15 Onse amene ali ndi ine akupereka moni. Upereke moni kwa amene amatikonda ife mʼchikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.
ασπαζονται σε οι μετ εμου παντεσ ασπασαι τουσ φιλουντασ ημασ εν πιστει η χαρισ μετα παντων υμων αμην