< Tito 2 >

1 Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona.
But say the things which fit sound doctrine,
2 Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.
that older men should be sober-minded, worthy of respect, self-controlled, sound in faith, in love, and in patience:
3 Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino.
and that older women likewise be reverent in behavior, not slanderers nor enslaved to much wine, teachers of that which is good;
4 Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo.
that they may train the young women to love their husbands, to love their children,
5 Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.
to be self-controlled, pure, working at home, kind, and being subject to their own husbands, so that God's word may not be discredited.
6 Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa.
Likewise, exhort the younger men to be self-controlled;
7 Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako.
in all things showing yourself an example of good works. In your teaching show integrity, seriousness,
8 Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.
and a sound message that cannot be condemned; that he who opposes you may be ashamed, having no evil thing to say about us.
9 Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo
Exhort servants to be in subjection to their own masters, and to be well-pleasing in all things; not contradicting;
10 kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu.
not stealing, but showing all good fidelity; that they may adorn the doctrine of God, our Savior, in all things.
11 Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse.
For the grace of God has appeared, bringing salvation to all people,
12 Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, (aiōn g165)
instructing us to say "No" to ungodliness and worldly desires, and to live soberly, righteously, and godly in this present age; (aiōn g165)
13 pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu,
looking for the blessed hope and appearing of the glory of our great God and Savior, Jesus Christ;
14 amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
who gave himself for us, that he might redeem us from all iniquity, and purify for himself a people for his own possession, zealous for good works.
15 Tsono zimenezi ndi zinthu zomwe uyenera kuphunzitsa. Uziwalimbikitsa anthu ndi kuwatsutsa komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ayi.
Say these things and exhort and reprove with all authority. Let no one despise you.

< Tito 2 >