< Nyimbo ya Solomoni 7 >

1 Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola mu nsapato wavalazo! Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali, ntchito ya manja ya mmisiri waluso.
Quam pulchri sunt gressus tui in calceamentis, filia principis! Iuncturae femorum tuorum, sicut monilia, quae fabricata sunt manu artificis.
2 Mchombo wako uli ngati chikho chowumbika bwino chimene nthawi zonse ndi chodzaza ndi vinyo. Chiwuno chako ndi choningʼa ngati mtolo wa tirigu utazunguliridwa ndi maluwa okongola.
Umbilicus tuus crater tornatilis, numquam indigens poculis. Venter tuus sicut acervus tritici, vallatus liliis.
3 Mawere ako akuoneka ngati ana awiri a mbawala, ngati mphoyo zamapasa.
Duo ubera tua, sicut duo hinnuli gemelli capreae.
4 Khosi lako lili see! ngati nsanja ya mnyanga wa njovu. Maso ako ali ngati mayiwe a ku Hesiboni, amene ali pafupi ndi chipata cha Bati Rabimu. Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni, yoyangʼana ku Damasiko.
Collum tuum sicut turris eburnea. Oculi tui sicut piscinae in Hesebon, quae sunt in porta filiae multitudinis. Nasus tuus sicut turris Libani, quae respicit contra Damascum.
5 Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli. Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu; mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola.
Caput tuum ut Carmelus: et comae capitis tui, sicut purpura regis vincta canalibus.
6 Ndiwe wokongola kwambiri ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwa, namwali wokondweretsawe!
Quam pulchra es, et quam decora charissima, in deliciis!
7 Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa, ndipo mawere ako ali ngati phava la zipatso.
Statura tua assimilata est palmae, et ubera tua botris.
8 Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa; ndidzathyola zipatso zake.” Mawere ako ali ngati maphava a mphesa, fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi,
Dixi: Ascendam in palmam, et apprehendam fructus eius: et erunt ubera tua sicut botri vineae: et odor oris tui sicut malorum.
9 ndipo pakamwa pako pali ngati vinyo wokoma kwambiri. Mkazi Tsono vinyo ameneyu amuthirire wachikondi wanga, ayenderere bwino pa milomo yake ndi mano ake.
Guttur tuum sicut vinum optimum, dignum dilecto meo ad potandum, labiisque et dentibus illius ad ruminandum.
10 Wokondedwayo ine ndine wake, ndipo chilakolako chake chili pa ine.
Ego dilecto meo, et ad me conversio eius.
11 Bwera wachikondi wanga, tiye tipite ku madera a ku midzi, tikagone ku midzi.
Veni dilecte mi, egrediamur in agrum, commoremur in villis.
12 Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa, tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira, ngati maluwa ake ayamba kuoneka, komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa. Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa.
Mane surgamus ad vineas, videamus si floruit vinea, si flores fructus parturiunt, si floruerunt mala punica: ibi dabo tibi ubera mea.
13 Mitengo ya mankhwala a chisulo ikupereka fungo lake labwino, ndipo pa khomo pathu pali zipatso zonse zokoma, zatsopano ndi zakale zomwe, zimene ndakusungira wokondedwa wanga.
Mandragorae dederunt odorem. In portis nostris omnia poma: nova et vetera, dilecte mi, servavi tibi.

< Nyimbo ya Solomoni 7 >