< Nyimbo ya Solomoni 6 >

1 Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti? Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti kuti timufunefune pamodzi ndi iwe?
Quo abiit dilectus tuus o pulcherrima mulierum? quo declinavit dilectus tuus, et quaeremus eum tecum?
2 Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake, ku timinda ta zokometsera zakudya, akukadyetsa ziweto zake ku minda, ndiponso akuthyola maluwa okongola.
Dilectus meus descendit in hortum suum ad areolam aromatum, ut pascatur in hortis, et lilia colligat.
3 Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga; amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola.
Ego dilecto meo, et dilectus meus mihi, qui pascitur inter lilia.
4 Ndiwe wokongola, bwenzi langa, ngati Tiriza, wokongola kwambiri ngati Yerusalemu, ndiwe woopsa ngati gulu lankhondo lonyamula mbendera.
Pulchra es amica mea, suavis, et decora sicut Ierusalem: terribilis ut castrorum acies ordinata.
5 Usandipenyetsetse; pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
Averte oculos tuos a me, quia ipsi me avolare fecerunt. Capilli tui sicut grex caprarum, quae apparuerunt de Galaad.
6 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zimene zikubwera kuchokera kokazisambitsa, iliyonse ili ndi ana amapasa, palibe imene ili yokha.
Dentes tui sicut grex ovium, quae ascenderunt de lavacro, omnes gemellis foetibus, et sterilis non est in eis.
7 Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutu, masaya ako ali ngati mabandu a makangadza.
Sicut cortex mali punici, sic genae tuae absque occultis tuis.
8 Ngakhale patakhala akazi a mfumu 60, ndi azikazi 80, ndi anamwali osawerengeka;
Sexaginta sunt reginae, et octoginta concubinae, et adolescentularum non est numerus.
9 koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense; mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake, mwana wapamtima wa amene anamubereka. Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala; akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda.
Una est columba mea, perfecta mea, una est matris suae, electa genetrici suae. Viderunt eam filiae, et beatissimam praedicaverunt: reginae et concubinae, et laudaverunt eam.
10 Ndani uyu akuoneka ngati mʼbandakucha, wokongola ngati mwezi, wowala ngati dzuwa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili mʼmanja?
Quae est ista, quae progreditur quasi aurora consurgens, pulchra ut luna, electa ut sol, terribilis ut castrorum acies ordinata?
11 Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa, kukaona ngati mpesa waphukira kapena ngati makangadza ali ndi maluwa.
Descendi in hortum nucum, ut viderem poma convallium, et inspicerem si floruisset vinea, et germinassent mala punica.
12 Ndisanazindikire kanthu, ndinakhala ngati ndikulota kuti ndili mʼgaleta pambali pa mfumu yanga.
Nescivi: anima mea conturbavit me propter quadrigas Aminadab.
13 Bwerera, bwerera iwe namwali wa ku Sulami; bwerera, bwerera kuti ife tidzakupenyetsetse iwe! Mwamuna Chifukwa chiyani mukufuna kudzapenyetsetsa ine mwana wamkazi wa ku Sulami, pamene ndikuvina pakati pa magulu awiri?
Revertere, revertere Sunamitis: revertere revertere, ut intueamur te. Quid videbis in Sunamite, nisi choros castrorum?

< Nyimbo ya Solomoni 6 >