< Nyimbo ya Solomoni 4 >
1 Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga! Ndithudi, ndiwe wokongola! Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
2 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene, zochokera kozisambitsa kumene. Iliyonse ili ndi ana amapasa; palibe imene ili yokha.
3 Milomo yako ili ngati mbota yofiira; pakamwa pako ndi pokongola kwambiri. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza.
4 Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndi yosalala; pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000, zishango zonsezo za anthu ankhondo.
5 Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala, ngati ana amapasa a nswala amene akudya pakati pa maluwa okongola.
6 Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, ndidzapita ku phiri la mure ndi ku chitunda cha lubani.
7 Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga; palibe chilema pa iwe.
8 Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga, tiye tichoke ku Lebanoni, utsikepo pa msonga ya Amana, kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni, kuchoka ku mapanga a mikango ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa.
9 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima, iwe wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.
10 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa! Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo, ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse!
11 Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi; pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi. Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
12 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa; ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa.
13 Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza; muli zipatso zokoma kwambiri, muli hena ndi nadi,
14 nadi ndi safiro, kalamusi ndi sinamoni, komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino. Mulinso mure ndi aloe ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri.
15 Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda, chitsime cha madzi oyenda, mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni.
16 Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera! Uzira pa munda wanga, kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse. Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.