< Nyimbo ya Solomoni 2 >
1 Ine ndine duwa la ku Saroni, duwa lokongola la ku zigwa.
2 Monga duwa lokongola pakati pa minga ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana.
3 Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata. Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako, ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga.
4 Iye wanditengera ku nyumba yaphwando, ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi.
5 Undidyetse keke ya mphesa zowuma, unditsitsimutse ndi ma apulosi, pakuti chikondi chandifowoketsa.
6 Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere, ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
7 Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho.
8 Tamverani bwenzi langa! Taonani! Uyu akubwera apayu, akulumphalumpha pa mapiri, akujowajowa pa zitunda.
9 Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala. Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira mʼmazenera, akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10 Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine, “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11 Ona, nyengo yozizira yatha; mvula yatha ndipo yapitiratu.
12 Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi; nthawi yoyimba yafika, kulira kwa njiwa kukumveka mʼdziko lathu.
13 Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira; mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga tiye tizipita.”
14 Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe, mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri, onetsa nkhope yako, nʼtamvako liwu lako; pakuti liwu lako ndi lokoma, ndipo nkhope yako ndi yokongola.
15 Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa, minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa.
16 Bwenzi langa ndi wangadi ndipo ine ndine wake; amadyetsa gulu lake la ziweto pakati pa maluwa okongola.
17 Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, unyamuke bwenzi langa, ndipo ukhale ngati gwape kapena ngati mwana wa mbawala pakati pa mapiri azigwembezigwembe.