< Nyimbo ya Solomoni 1 >

1 Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse.
שיר השירים אשר לשלמה
2 Undipsompsone ndi milomo yako chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo.
ישקני מנשיקות פיהו כי טובים דדיך מיין
3 Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino; dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa. Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda!
לריח שמניך טובים שמן תורק שמך על כן עלמות אהבוך
4 Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire! Mfumu indilowetse mʼchipinda chake. Abwenzi Ife timasangalala ndi kukondwera nawe, tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo. Mkazi Amachita bwinotu potamanda iwe!
משכני אחריך נרוצה הביאני המלך חדריו נגילה ונשמחה בך--נזכירה דדיך מיין מישרים אהבוך
5 Ndine wakuda, komatu ndine wokongola, inu akazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda ngati tenti ya ku Kedara, ngati makatani a tenti ya Solomoni.
שחורה אני ונאוה בנות ירושלם כאהלי קדר כיריעות שלמה
6 Musandiyangʼane monyoza chifukwa ndine wakuda, ndine wakuda chifukwa cha dzuwa. Alongo anga anandikwiyira ndipo anandigwiritsa ntchito mʼminda ya mpesa; munda wangawanga sindinawusamalire.
אל תראוני שאני שחרחרת ששזפתני השמש בני אמי נחרו בי שמני נטרה את הכרמים--כרמי שלי לא נטרתי
7 Ndiwuze iwe, amene ndimakukonda, kumene umadyetsa ziweto zako ndi kumene umagoneka nkhosa zako nthawi yamasana. Ndikhalirenji ngati mkazi wachiwerewere pambali pa ziweto za abwenzi ako?
הגידה לי שאהבה נפשי איכה תרעה איכה תרביץ בצהרים שלמה אהיה כעטיה על עדרי חבריך
8 Ngati sukudziwa iwe wokongola kwambiri kuposa akazi ena, ngati sukudziwa, tsatira makwalala a nkhosa ndipo udyetse ana ambuzi pambali pa matenti a abusa.
אם לא תדעי לך היפה בנשים צאי לך בעקבי הצאן ורעי את גדיתיך על משכנות הרעים
9 Iwe bwenzi langa, uli ngati kavalo wamkazi ku magaleta a Farao.
לססתי ברכבי פרעה דמיתיך רעיתי
10 Masaya ako ndi okongola ndi ndolo zamʼmakutuzo, khosi lako likukongola ndi mikanda yamiyala yamtengowapatali.
נאוו לחייך בתרים צוארך בחרוזים
11 Tidzakupangira ndolo zagolide zokongoletsedwa ndi mikanda yasiliva.
תורי זהב נעשה לך עם נקדות הכסף
12 Pamene mfumu inali pa malo ake odyera, mafuta anga onunkhira anamveka fungo lake.
עד שהמלך במסבו נרדי נתן ריחו
13 Wokondedwa wanga ali ngati kathumba ka mure kwa ine, kamene kamakhala pakati pa mawere angawa.
צרור המר דודי לי בין שדי ילין
14 Wokondedwa wanga ali ngati mpukutu wa maluwa ofiira, ochokera ku minda ya mpesa ya ku Eni-Gedi.
אשכל הכפר דודי לי בכרמי עין גדי
15 Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe chiphadzuwa, maso ako ali ngati nkhunda.
הנך יפה רעיתי הנך יפה עיניך יונים
16 Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri! Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira.
הנך יפה דודי אף נעים אף ערשנו רעננה
17 Mitanda ya nyumba yathu ndi ya mkungudza, phaso lake ndi la mtengo wa payini.
קרות בתינו ארזים רחיטנו (רהיטנו) ברותים

< Nyimbo ya Solomoni 1 >