< Rute 1 >

1 Mu nthawi imene oweruza ankalamulira Israeli, munali njala mʼdziko, ndipo munthu wina wa ku Betelehemu mʼdziko la Yuda anapita pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna awiri, kukakhala ku Mowabu kwa nthawi yochepa.
ויהי בימי שפט השפטים ויהי רעב בארץ וילך איש מבית לחם יהודה לגור בשדי מואב--הוא ואשתו ושני בניו
2 Dzina la munthuyo linali Elimeleki, dzina la mkazi wake linali Naomi, ndipo mayina a ana awo aamuna anali Maaloni ndi Kiliyoni. Iwo anali Aefurati ochokera ku Betelehemu ku Yuda. Ndipo anapita kukakhala ku Mowabu.
ושם האיש אלימלך ושם אשתו נעמי ושם שני בניו מחלון וכליון אפרתים--מבית לחם יהודה ויבאו שדי מואב ויהיו שם
3 Kenaka Elimeleki, mwamuna wake wa Naomi anamwalira ndipo Naomiyo anatsala ndi ana ake aamuna awiri aja.
וימת אלימלך איש נעמי ותשאר היא ושני בניה
4 Iwo anakwatira akazi a Chimowabu; wina dzina lake Oripa ndi wina Rute. Atakhala kumeneko pafupifupi zaka khumi,
וישאו להם נשים מאביות--שם האחת ערפה ושם השנית רות וישבו שם כעשר שנים
5 Maloni ndi Kiliyoni anamwaliranso kotero kuti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja ndi mwamuna wake.
וימתו גם שניהם מחלון וכליון ותשאר האשה משני ילדיה ומאישה
6 Naomi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kubwerera kwawo kuchokera ku Mowabu popeza anali atamva ali ku Mowabuko kuti Yehova anakomera mtima anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.
ותקם היא וכלתיה ותשב משדי מואב כי שמעה בשדה מואב--כי פקד יהוה את עמו לתת להם לחם
7 Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja anachoka kumene ankakhala ndi kuyamba ulendo obwerera kwawo ku Yuda.
ותצא מן המקום אשר היתה שמה ושתי כלותיה עמה ותלכנה בדרך לשוב אל ארץ יהודה
8 Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, “Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe.
ותאמר נעמי לשתי כלתיה לכנה שבנה אשה לבית אמה יעשה (יעש) יהוה עמכם חסד כאשר עשיתם עם המתים ועמדי
9 “Yehova akuthandizeni kuti aliyense wa inu apeze pokhala pabwino komanso mwamuna.” Kenaka anawapsompsona koma awiriwo analira mokweza.
יתן יהוה לכם ומצאן מנוחה אשה בית אישה ותשק להן ותשאנה קולן ותבכינה
10 Ndipo anati kwa Naomi, “Ife tipita nawo kwa anthu akwanu.”
ותאמרנה לה כי אתך נשוב לעמך
11 Koma Naomi anati, “Bwererani kwanu ana anga. Chifukwa chiyani mukufuna kupita ndi ine? Kodi ine ndingaberekenso ana ena kuti akhale amuna anu?
ותאמר נעמי שבנה בנתי למה תלכנה עמי העוד לי בנים במעי והיו לכם לאנשים
12 Bwererani kwanu ana anga muzipita kwanu. Ine ndakalamba kwambiri kotero kuti sindingakwatiwenso. Ngakhale ndikananena kuti ndili nacho chikhulupiriro, ngakhale ndikanakhala ndi mwamuna usiku uno, ndipo nʼkubala ana aamuna,
שבנה בנתי לכן כי זקנתי מהיות לאיש כי אמרתי יש לי תקוה--גם הייתי הלילה לאיש וגם ילדתי בנים
13 kodi inu mukanadikira kuti akule? Kodi mukanakhalabe osakwatiwa kudikira iwowo? Ayi ana anga. Zimenezi zikundiwawa kwambiri kuposa inu, chifukwa ndi ineyo amene Yehova wafuna kuti ndizunzike.”
הלהן תשברנה עד אשר יגדלו הלהן תעגנה לבלתי היות לאיש אל בנתי כי מר לי מאד מכם--כי יצאה בי יד יהוה
14 Atamva zimenezi analiranso kwambiri, ndipo Oripa anapsompsona apongozi ake nawatsanzika, koma Rute anakakamirabe.
ותשנה קולן ותבכינה עוד ותשק ערפה לחמותה ורות דבקה בה
15 Naomi anati “Taona, mʼbale wako wabwerera kwawo kwa anthu ake ndi kwa milungu yake. Bwerera nawenso umulondole mʼbale wako.”
ותאמר הנה שבה יבמתך אל עמה ואל אלהיה שובי אחרי יבמתך
16 Koma Rute anayankha kuti, “Musandikakamize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndibwerere osakutsatani. Kumene inu mupite ine ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.
ותאמר רות אל תפגעי בי לעזבך לשוב מאחריך כי אל אשר תלכי אלך ובאשר תליני אלין--עמך עמי ואלהיך אלהי
17 Kumene mukafere inenso ndidzafera komweko ndipo komweko ndikayikidwa mʼmanda. Yehova andichite choyipa chingakule motani, ngati china chingatirekanitse ife kupatula imfa.”
באשר תמותי אמות ושם אקבר כה יעשה יהוה לי וכה יוסיף--כי המות יפריד ביני ובינך
18 Naomi atazindikira kuti Rute watsimikiza kupita naye, analeka kumukakamiza.
ותרא כי מתאמצת היא ללכת אתה ותחדל לדבר אליה
19 Choncho amayi awiriwo anapitiriza ulendo wawo mpaka anakafika ku Betelehemu. Pamene ankafika mu Betelehemu, anthu onse a mʼmudzimo anatekeseka chifukwa cha iwowo ndipo amayi ambiri ankanena kuti, “Kodi uyu nʼkukhala Naomi?”
ותלכנה שתיהם עד בואנה בית לחם ויהי כבואנה בית לחם ותהם כל העיר עליהן ותאמרנה הזאת נעמי
20 Iye anawawuza kuti, “Musanditchenso Naomi. Muzinditchula ine kuti Mara, chifukwa Wamphamvuzonse wandizunza kwambiri.
ותאמר אליהן אל תקראנה לי נעמי קראן לי מרא כי המר שדי לי מאד
21 Ine ndinapita wolemera, koma Yehova wabwera nane wopanda kanthu. Nanga munditchulirenji Naomi pamene Yehova wandisautsa. Wamphamvuzonse uja wandigwetsera mavuto owawa.”
אני מלאה הלכתי וריקם השיבני יהוה למה תקראנה לי נעמי ויהוה ענה בי ושדי הרע לי
22 Naomi anabwerera kuchoka ku dziko la Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake. Ndipo anafika ku Betelehemu nthawi yoyamba kukolola barele.
ותשב נעמי ורות המואביה כלתה עמה השבה משדי מואב והמה באו בית לחם בתחלת קציר שערים

< Rute 1 >