< Aroma 1 >
1 Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu
Павло, раб Ісуса Христа, покликаний апо́стол, вибраний для звіща́ння Єва́нгелії Божої,
2 umene analonjeza kale mʼMalemba Oyera kudzera mwa aneneri ake.
яку Він перед тим приобіцяв через Своїх пророків у святих Писа́ннях,
3 Uthengawu ndi wonena za Mwana wake amene mwa umunthu wake anali wochokera mwa Davide.
про Сина Свого, що тілом був із насіння Давидового,
4 Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu,
і об'явився Сином Божим у силі, за Ду́хом святости, через воскресіння з мертвих, про Ісуса Христа, Господа нашого,
5 ife tinalandira chisomo chokhala atumwi oyitana anthu a mitundu yonse kuti amukhulupirire ndi kumumvera mwachikhulupiriro kuti dzina lake lilemekezedwe.
що через Нього прийняли ми благода́ть і апо́стольство на по́слух віри через Ім'я́ Його між усіма́ народами,
6 Inunso muli mʼgulu la Amitundu oyitanidwawo kukhala ake a Yesu Khristu.
між якими й ви, покликані Ісуса Христа, —
7 Ndikulembera kwa onse okhala ku Roma amene Mulungu amakukondani nakuyitanani kuti mukhale oyera mtima. Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
усім, хто знаходиться в Римі, улю́бленим Божим, покликаним святим, — благода́ть вам та мир від Бога, Отця нашого, і Господа Ісуса Христа!
8 Poyamba, ndikuthokoza Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akukamba za chikhulupiriro chanu.
Отже, насамперед дякую Богові моєму через Ісуса Христа за всіх вас, що віра ваша звіщається по всьому світові.
9 Mulungu amene ndimamutumikira ndi mtima wanga onse polalikira Uthenga Wabwino wa Mwana wake, ndi mboni yanga kuti ndimakupemphererani nthawi zonse.
Бо свідок мені Бог, Якому служу́ духом своїм у звіща́нні Єва́нгелії Його Сина, що я безпереста́нно згадую про вас,
10 Mʼmapemphero anga, nthawi zonse, ndimapemphera kuti ngati nʼkotheka mwachifuniro cha Mulungu, njira inditsekukire kuti ndibwere kwanuko.
і в моли́твах своїх за́вжди молюся, щоб воля Божа щасливо попрова́дила мене коли прийти до вас.
11 Ine ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugawireni mphatso zina zauzimu kuti zikulimbikitseni
Бо прагну вас бачити, щоб подати вам якого дара духовного для змі́цнення вас,
12 ndiponso kuti tonsefe tilimbikitsane mʼchikhulupiriro wina ndi mnzake.
цебто потішитись ра́зом між вами спі́льною вірою — і вашою, і моєю.
13 Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa kuti nthawi zambiri ndakhala ndikufuna zobwera kwanuko, koma mpaka pano pali zolepheretsa, ndi cholinga choti ndidzapezeko zipatso pakati panupo monga momwe ndakhala ndikuchitira pakati pa a mitundu ina.
Не хочу ж, щоб ви не знали, браття, що багато разів мав я за́мір прийти до вас, але мені перешко́джувано аж досі, щоб мати який плід і в вас, як і в інших наро́дів.
14 Ine ndi wokakamizidwa ndi udindo wotumikira Agriki pamodzi ndi omwe si Agriki, kwa anzeru ndi kwa opusa omwe.
А ге́лленам і чужоземцям, розумним і немудрим — я боржни́к.
15 Pa chifukwa chimenechi, ine ndikufunitsitsa kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso amene muli ku Roma.
Отже, щодо мене, я готовий і вам, хто знаходиться в Римі, звіщати Єва́нгелію.
16 Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene.
Бо я не соромлюсь Єва́нгелії, бож вона — сила Божа на спасі́ння кожному, хто вірує, перше ж юдеєві, а потім ге́лленові.
17 Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
Праведність бо Божа з'являється в ній з віри в віру, як написано: „А праведний житиме вірою“.
18 Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa.
Бо гнів Божий з'являється з неба на всяку безбожність і неправду людей, що правду гаму́ють неправдою,
19 Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo.
тому, що те, що можна знати про Бога, явне для них, бо їм Бог об'явив.
20 Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula. (aïdios )
Бо Його невиди́ме від створення світу, власне Його вічна сила й Божество, ду́манням про твори стає види́ме. Так що нема їм виправдання, (aïdios )
21 Ngakhale iwo anadziwa Mulungu, sanamulemekeze ngati Mulungu kapena kumuthokoza, koma maganizo awo anasanduka wopanda pake ndipo mʼmitima yawo yopusa munadzaza mdima.
бо, пізнавши Бога, не прославляли Його, як Бога, і не дякували, але знікчемні́ли своїми думка́ми, і запа́морочилось нерозумне їхнє серце.
22 Ngakhale ankadzitama kuti ndi anzeru, anasanduka opusa.
Називаючи себе мудрими, вони потумані́ли,
23 Iwo anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu wosafa ndi mafano opangidwa ndi manja wooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame, ndi nyama kapena zokwawa.
і славу нетлінного Бога змінили на подобу образа тлінної люди́ни, і птахів, і чотириногих, і га́дів.
24 Nʼchifukwa chake Mulungu anawasiya kuti azingochita zilakolako zochititsa manyazi zauchimo zomwe mitima yawo inkafuna. Zotsatira zake anachita za chiwerewere wina ndi mnzake kunyazitsa matupi awo.
Тому́ то й видав їх Бог у пожадливостях їхніх сердець на нечи́стість, щоб вони самі знеславляли тіла свої.
25 Iwo anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza ndipo anapembedza ndi kutumikira zinthu zolengedwa mʼmalo mwa Mlengi amene ali woyenera kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni. (aiōn )
Вони Божу правду замінили на неправду, і честь віддавали, і служили створінню більш, як Творце́ві, що благослове́нний навіки, амі́нь. (aiōn )
26 Chifukwa cha ichi, Mulungu anawasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe anasiya machitidwe achibadwidwe pa za ukwati, namachita machitidwe ena otsutsana ndi chibadwa chawo.
Через це Бог їх видав на пожадливість гане́бну, — бо їхні жінки замінили природне єдна́ння на протиприродне.
27 Chimodzimodzinso amuna analeka machitidwe a ukwati ndi akazi nʼkumakhumbana amuna okhaokha. Amuna ankachita zochitisa manyazizi ndi amuna anzawo, ndipo analandira chilango choyenera molingana ndi zochita zawo zachitayikozo.
Так само й чоловіки, позоставивши природне єдна́ння з жіночою статтю, розпали́лися своєю пожадливістю один до о́дного, і чоловіки з чоловіками сором чинили. І вони прийняли́ в собі відплату, відповідну їхньому блу́дові.
28 Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo.
А що вони не вважали за потрібне мати Бога в пізна́нні, видав їх Бог на розум переве́рнений, — щоб чинили непристойне.
29 Iwo ndi odzazidwa ndi mtundu uliwonse wa makhalidwe oyipa, zonyansa, umbombo ndi dumbo. Iwo ndi odzazidwa ndi kaduka, kupha, mikangano, chinyengo ndi udani. Iwowo ndi amiseche,
Вони повні всякої неправедности, лукавства, заже́рливости, зло́би, повні заздрости, убивства, суперечки, омани, лихих звича́їв,
30 osinjirira, odana ndi Mulungu, achipongwe, odzitama ndi odzitukumula. Iwo amapeza njira zochitira zoyipa. Samvera makolo awo,
обмовники, наклепники, богонена́видники, напасники́, чваньки, пишні, винахідники зла, неслухня́ні батькам,
31 alibe nzeru, chikhulupiriro, sakhudzidwa mu mtima ndipo ndi ankhanza.
нерозумні, зрадники, нелюбовні, немилости́ві.
32 Ngakhale kuti amadziwa chiweruzo cholungama cha Mulungu chakuti amene amachita zinthu zotere amayenera imfa, iwo sangopitiriza chabe zimenezi, koma amavomerezanso amene amazichita zimenezi.
Вони знають при́суд Божий, що ті, хто чинить таке, ва́рті смерти, а проте не тільки самі чинять, але й хвалять тих, хто робить таке.