< Aroma 9 >

1 Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni.
αληθειαν λεγω εν χριστω ου ψευδομαι συμμαρτυρουσης μοι της συνειδησεως μου εν πνευματι αγιω
2 Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga.
οτι λυπη μοι εστιν μεγαλη και αδιαλειπτος οδυνη τη καρδια μου
3 Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga,
ευχομην γαρ αυτος εγω αναθεμα ειναι απο του χριστου υπερ των αδελφων μου των συγγενων μου κατα σαρκα
4 anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake.
οιτινες εισιν ισραηλιται ων η υιοθεσια και η δοξα και αι διαθηκαι και η νομοθεσια και η λατρεια και αι επαγγελιαι
5 Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni. (aiōn g165)
ων οι πατερες και εξ ων ο χριστος το κατα σαρκα ο ων επι παντων θεος ευλογητος εις τους αιωνας αμην (aiōn g165)
6 Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli.
ουχ οιον δε οτι εκπεπτωκεν ο λογος του θεου ου γαρ παντες οι εξ ισραηλ ουτοι ισραηλ
7 Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.
ουδ οτι εισιν σπερμα αβρααμ παντες τεκνα αλλ εν ισαακ κληθησεται σοι σπερμα
8 Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu.
τουτ εστιν ου τα τεκνα της σαρκος ταυτα τεκνα του θεου αλλα τα τεκνα της επαγγελιας λογιζεται εις σπερμα
9 Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
επαγγελιας γαρ ο λογος ουτος κατα τον καιρον τουτον ελευσομαι και εσται τη σαρρα υιος
10 Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake.
ου μονον δε αλλα και ρεβεκκα εξ ενος κοιτην εχουσα ισαακ του πατρος ημων
11 Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire,
μηπω γαρ γεννηθεντων μηδε πραξαντων τι αγαθον η κακον ινα η κατ εκλογην προθεσις του θεου μενη ουκ εξ εργων αλλ εκ του καλουντος
12 osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.”
ερρηθη αυτη οτι ο μειζων δουλευσει τω ελασσονι
13 Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”
καθως γεγραπται τον ιακωβ ηγαπησα τον δε ησαυ εμισησα
14 Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe!
τι ουν ερουμεν μη αδικια παρα τω θεω μη γενοιτο
15 Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti, “Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo, ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”
τω γαρ μωυση λεγει ελεησω ον αν ελεω και οικτειρησω ον αν οικτειρω
16 Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu.
αρα ουν ου του θελοντος ουδε του τρεχοντος αλλα του ελεουντος θεου
17 Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.”
λεγει γαρ η γραφη τω φαραω οτι εις αυτο τουτο εξηγειρα σε οπως ενδειξωμαι εν σοι την δυναμιν μου και οπως διαγγελη το ονομα μου εν παση τη γη
18 Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.
αρα ουν ον θελει ελεει ον δε θελει σκληρυνει
19 Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?”
ερεις ουν μοι τι ετι μεμφεται τω γαρ βουληματι αυτου τις ανθεστηκεν
20 Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’”
μενουνγε ω ανθρωπε συ τις ει ο ανταποκρινομενος τω θεω μη ερει το πλασμα τω πλασαντι τι με εποιησας ουτως
21 Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?
η ουκ εχει εξουσιαν ο κεραμευς του πηλου εκ του αυτου φυραματος ποιησαι ο μεν εις τιμην σκευος ο δε εις ατιμιαν
22 Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko.
ει δε θελων ο θεος ενδειξασθαι την οργην και γνωρισαι το δυνατον αυτου ηνεγκεν εν πολλη μακροθυμια σκευη οργης κατηρτισμενα εις απωλειαν
23 Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake
και ινα γνωριση τον πλουτον της δοξης αυτου επι σκευη ελεους α προητοιμασεν εις δοξαν
24 ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina.
ους και εκαλεσεν ημας ου μονον εξ ιουδαιων αλλα και εξ εθνων
25 Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”
ως και εν τω ωσηε λεγει καλεσω τον ου λαον μου λαον μου και την ουκ ηγαπημενην ηγαπημενην
26 ndipo, “Pamalo omwewo pamene ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’”
και εσται εν τω τοπω ου ερρηθη αυτοις ου λαος μου υμεις εκει κληθησονται υιοι θεου ζωντος
27 Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti, “Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiye adzapulumuke.
ησαιας δε κραζει υπερ του ισραηλ εαν η ο αριθμος των υιων ισραηλ ως η αμμος της θαλασσης το καταλειμμα σωθησεται
28 Pakuti Ambuye adzagamula milandu ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”
λογον γαρ συντελων και συντεμνων εν δικαιοσυνη οτι λογον συντετμημενον ποιησει κυριος επι της γης
29 Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti, “Ngati Yehova Wamphamvuzonse akanapanda kutisiyira zidzukulu, ife tikanawonongeka ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”
και καθως προειρηκεν ησαιας ει μη κυριος σαβαωθ εγκατελιπεν ημιν σπερμα ως σοδομα αν εγενηθημεν και ως γομορρα αν ωμοιωθημεν
30 Kodi nanga tidzati chiyani? Tidzati a mitundu ina amene sanafune chilungamo analandira chilungamo chachikhulupiriro
τι ουν ερουμεν οτι εθνη τα μη διωκοντα δικαιοσυνην κατελαβεν δικαιοσυνην δικαιοσυνην δε την εκ πιστεως
31 koma Aisraeli, amene anafuna chilungamo cha lamulo sanachilandire.
ισραηλ δε διωκων νομον δικαιοσυνης εις νομον δικαιοσυνης ουκ εφθασεν
32 Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.”
δια τι οτι ουκ εκ πιστεως αλλ ως εξ εργων νομου προσεκοψαν γαρ τω λιθω του προσκομματος
33 Monga momwe kwalembedwa kuti, “Taonani, Ine ndikuyika mwala mu Ziyoni wopunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Koma amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”
καθως γεγραπται ιδου τιθημι εν σιων λιθον προσκομματος και πετραν σκανδαλου και πας ο πιστευων επ αυτω ου καταισχυνθησεται

< Aroma 9 >