< Aroma 6 >

1 Nanga tinene chiyani? Kodi tipitirire kuchimwa kuti chisomo chichulukebe?
Quid ergo dicemus? permanebimus in peccato ut gratia abundet?
2 Ayi. Mʼnjira iliyonse! Popeza tinafa ku tchimo, nanga tidzapitirira bwanji kukhalabe mʼmenemo?
Absit. Qui enim mortui sumus peccato, quomodo adhuc vivemus in illo?
3 Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake?
an ignoratis quia quicumque baptizati sumus in Christo Jesu, in morte ipsius baptizati sumus?
4 Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
Consepulti enim sumus cum illo per baptismum in mortem: ut quomodo Christus surrexit a mortuis per gloriam Patris, ita et nos in novitate vitæ ambulemus.
5 Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake.
Si enim complantati facti sumus similitudini mortis ejus: simul et resurrectionis erimus.
6 Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo
Hoc scientes, quia vetus homo noster simul crucifixus est, ut destruatur corpus peccati, et ultra non serviamus peccato.
7 chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo.
Qui enim mortuus est, justificatus est a peccato.
8 Koma ngati tinafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye.
Si autem mortui sumus cum Christo, credimus quia simul etiam vivemus cum Christo,
9 Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye.
scientes quod Christus resurgens ex mortuis jam non moritur: mors illi ultra non dominabitur.
10 Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.
Quod enim mortuus est peccato, mortuus est semel: quod autem vivit, vivit Deo.
11 Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
Ita et vos existimate vos mortuos quidem esse peccato, viventes autem Deo, in Christo Jesu Domino nostro.
12 Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa.
Non ergo regnet peccatum in vestro mortali corpore ut obediatis concupiscentiis ejus.
13 Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.
Sed neque exhibeatis membra vestra arma iniquitatis peccato: sed exhibete vos Deo, tamquam ex mortuis viventes: et membra vestra arma justitiæ Deo.
14 Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.
Peccatum enim vobis non dominabitur: non enim sub lege estis, sed sub gratia.
15 Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi!
Quid ergo? peccabimus, quoniam non sumus sub lege, sed sub gratia? Absit.
16 Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake.
Nescitis quoniam cui exhibetis vos servos ad obediendum, servi estis ejus, cui obeditis, sive peccati ad mortem, sive obeditionis ad justitiam?
17 Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira.
Gratias autem Deo quod fuistis servi peccati, obedistis autem ex corde in eam formam doctrinæ, in quam traditi estis.
18 Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.
Liberati autem a peccato, servi facti estis justitiæ.
19 Ine ndikufanizira zinthu za tsiku ndi tsiku chifukwa chikhalidwe chanu nʼchofowoka. Monga momwe munkapereka ziwalo za matupi kukhala akapolo a zonyansa ndi makhalidwe oyipa, zimene zimanka zichulukirabe, choncho tsopano dziperekeni ziwalozo kuti zikhale akapolo achilungamo ndi a kuyera mtima.
Humanum dico, propter infirmitatem carnis vestræ: sicut enim exhibuistis membra vestra servire immunditiæ, et iniquitati ad iniquitatem, ita nunc exhibete membra vestra servire justitiæ in sanctificationem.
20 Pomwe munali akapolo atchimo, simunkalabadira za chilungamo.
Cum enim servi essetis peccati, liberi fuistis justitiæ.
21 Kodi munapeza phindu lanji pochita zinthu zimenezi, zomwe tsopano mukuchita nazo manyazi? Zinthu zimenezo zotsatira zake ndi imfa!
Quem ergo fructum habuistis tunc in illis, in quibus nunc erubescitis? nam finis illorum mors est.
22 Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha. (aiōnios g166)
Nunc vero liberati a peccato, servi autem facti Deo, habetis fructum vestrum in sanctificationem, finem vero vitam æternam. (aiōnios g166)
23 Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu. (aiōnios g166)
Stipendia enim peccati, mors. Gratia autem Dei, vita æterna, in Christo Jesu Domino nostro. (aiōnios g166)

< Aroma 6 >