< Aroma 16 >
1 Ine ndikupereka kwa inu mlongo wathu Febe, mtumiki wa mpingo wa ku Kenkreya.
2 Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.
3 Perekani moni kwa Prisila ndi Akura, atumiki anzanga mwa Khristu Yesu.
4 Iwo anapereka miyoyo yawo chifukwa cha ine. Osati ine ndekha komanso mipingo yonse ya a mitundu ina ikuyamika.
5 Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo. Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.
6 Perekani moni kwa Mariya, amene wakhala akukugwirirani ntchito kwambiri.
7 Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.
8 Perekani moni kwa Ampliato, amene ine ndimamukonda mwa Ambuye.
9 Perekani moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu mwa Khristu ndi wokondedwa wanga Staku.
10 Perekani moni kwa Apele, woyesedwa ndi wovomerezeka mwa Khristu. Perekani moni kwa a mʼbanja la Aristobulo.
11 Perekani moni kwa Herodiona, mʼbale wanga. Perekani moni kwa a mʼbanja la Narkiso amene ali mwa Ambuye.
12 Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika. Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.
13 Perekani moni kwa Rufo, wosankhidwa mwa Ambuye, ndi amayi ake, amene akhala amayi anganso.
14 Perekani moni kwa Asunkrito, Felego, Herima, Patroba, Herima ndi abale amene ali nawo pamodzi.
15 Perekani moni kwa Filologo, Yuliya, Neriya ndi mlongo wake, ndi Olumpa ndi oyera mtima onse amene ali nawo pamodzi.
16 Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona. Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.
17 Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo.
18 Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa.
19 Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.
20 Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu. Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.
21 Timoteyo, mtumiki mnzanga, akupereka moni. Nawonso, Lusio, Yasoni ndi Sosipatro, abale anga akutero.
22 Ine Tertio, amene ndalemba kalatayi, ndi kupereka moni mwa Ambuye.
23 Gayo, amene chifukwa cha chisamaliro chake, ine ndi mpingo wonse kuno tikusangalala, akupereka moni. Erasto, amene ndi msungichuma wa mzinda wonse ndiponso mʼbale wathu Kwato, akupereka moni.
24 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.
25 Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, (aiōnios )
26 koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye, (aiōnios )
27 kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni. (aiōn )