< Aroma 15 >

1 Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha.
Ὀφείλομεν δὲ ἡμεῖς οἱ δυνατοὶ τὰ ἀσθενήματα τῶν ἀδυνάτων βαστάζειν, καὶ μὴ ἑαυτοῖς ἀρέσκειν.
2 Aliyense wa ife akondweretse mnzake pomuchitira zabwino zomulimbikitsa.
ἕκαστος ἡμῶν τῷ πλησίον ἀρεσκέτω εἰς τὸ ἀγαθὸν πρὸς οἰκοδομήν·
3 Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretsa yekha koma, monga kwalembedwa kuti, “Chipongwe cha anthu okunyozani chinagwera Ine.”
καὶ γὰρ ὁ Χριστὸς οὐχ ἑαυτῷ ἤρεσεν, ἀλλὰ καθὼς γέγραπται, οἱ ὀνειδισμοὶ τῶν ὀνειδιζόντων σε ἐπέπεσον ἐπ᾽ ἐμέ.
4 Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.
ὅσα γὰρ προεγράφη, εἰς τὴν ἡμετέραν διδασκαλίαν προεγράφη, ἵνα διὰ τῆς ὑπομονῆς καὶ τῆς παρακλήσεως τῶν γραφῶν τὴν ἐλπίδα ἔχωμεν.
5 Mulungu amene amapereka kupirira ndi chilimbikitso akupatseni maganizo amodzi pakati panu monga inu mukutsatira Khristu Yesu,
ὁ δὲ Θεὸς τῆς ὑπομονῆς καὶ τῆς παρακλήσεως δῴη ὑμῖν τὸ αὐτὸ φρονεῖν ἐν ἀλλήλοις κατὰ Χριστὸν Ἰησοῦν,
6 kotero kuti ndi mtima umodzi ndi movomerezana mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
ἵνα ὁμοθυμαδὸν ἐν ἑνὶ στόματι δοξάζητε τὸν Θεὸν καὶ πατέρα τοῦ Κυρίου ἡμῶν Ἰησοῦ Χριστοῦ.
7 Tsopano landiranani wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, ndi cholinga choti Mulungu alemekezeke.
διὸ προσλαμβάνεσθε ἀλλήλους, καθὼς καὶ ὁ Χριστὸς προσελάβετο ὑμᾶς εἰς δόξαν Θεοῦ.
8 Chifukwa kunena zoona, Khristu wasanduka mtumiki wa Ayuda, kuonetsa kuti Mulungu ndi wokhulupirika pa malonjezo amene anachita kwa makolo awo
Λέγω δὲ Χριστὸν Ἰησοῦν διάκονον γεγενῆσθαι περιτομῆς ὑπὲρ ἀληθείας Θεοῦ, εἰς τὸ βεβαιῶσαι τὰς ἐπαγγελίας τῶν πατέρων,
9 kuti a mitundu ina atamande Mulungu chifukwa cha chifundo chake. Monga kwalembedwa kuti, “Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa a mitundu; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
τὰ δὲ ἔθνη ὑπὲρ ἐλέους δοξάσαι τὸν Θεόν, καθὼς γέγραπται· διὰ τοῦτο ἐξομολογήσομαί σοι ἐν ἔθνεσι, Κύριε, καὶ τῷ ὀνόματί σου ψαλῶ.
10 Akutinso, “Kondwerani inu anthu a mitundu ina pamodzi ndi anthu ake.”
καὶ πάλιν λέγει· εὐφράνθητε ἔθνη μετὰ τοῦ λαοῦ αὐτοῦ.
11 Ndipo akutinso, “Tamandani Ambuye, inu nonse a mitundu ina, ndi kuyimba zotamanda Iye, inu anthu onse.”
καὶ πάλιν· αἰνεῖτε τὸν Κύριον πάντα τὰ ἔθνη, καὶ ἐπαινέσατε αὐτὸν πάντες οἱ λαοί.
12 Ndiponso Yesaya akuti, “Muzu wa Yese udzaphuka, wina amene adzauka kulamulira anthu a mitundu ina; mwa Iye mudzakhala chiyembekezo cha a mitundu ina.”
καὶ πάλιν Ἡσαΐας λέγει· ἔσται ἡ ῥίζα τοῦ Ἰεσσαί, καὶ ὁ ἀνιστάμενος ἄρχειν ἐθνῶν· ἐπ᾽ αὐτῷ ἔθνη ἐλπιοῦσιν.
13 Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.
Ὁ δὲ Θεὸς τῆς ἐλπίδος πληρώσαι ὑμᾶς πάσης χαρᾶς καὶ εἰρήνης ἐν τῷ πιστεύειν, εἰς τὸ περισσεύειν ὑμᾶς ἐν τῇ ἐλπίδι ἐν δυνάμει Πνεύματος Ἁγίου.
14 Abale anga, ine mwini ndikutsimikiza kuti inuyo ndinu abwino, odzaza ndi chidziwitso ndi okhoza kulangizana wina ndi mnzake.
Πέπεισμαι δέ, ἀδελφοί μου, καὶ αὐτὸς ἐγὼ περὶ ὑμῶν, ὅτι καὶ αὐτοὶ μεστοί ἐστε ἀγαθωσύνης, πεπληρωμένοι πάσης γνώσεως, δυνάμενοι καὶ ἀλλήλους νουθετεῖν.
15 Ine ndakulemberani inu molimba mtima pa fundo zina, kukhala ngati kukukumbutsaninso za zimenezo, chifukwa cha chisomo chimene Mulungu anandipatsa ine
τολμηρότερον δὲ ἔγραψα ὑμῖν, ἀδελφοί, ἀπὸ μέρους, ὡς ἐπαναμιμνήσκων ὑμᾶς, διὰ τὴν χάριν τὴν δοθεῖσάν μοι ὑπὸ τοῦ Θεοῦ
16 kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.
εἰς τὸ εἶναί με λειτουργὸν Ἰησοῦ Χριστοῦ εἰς τὰ ἔθνη, ἱερουργοῦντα τὸ εὐαγγέλιον τοῦ Θεοῦ, ἵνα γένηται ἡ προσφορὰ τῶν ἐθνῶν εὐπρόσδεκτος, ἡγιασμένη ἐν Πνεύματι Ἁγίῳ.
17 Choncho, ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu potumikira Mulungu wanga.
ἔχω οὖν καύχησιν ἐν Χριστῷ Ἰησοῦ τὰ πρὸς τὸν Θεόν·
18 Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita
οὐ γὰρ τολμήσω λαλεῖν τι ὧν οὐ κατειργάσατο Χριστὸς δι᾽ ἐμοῦ εἰς ὑπακοὴν ἐθνῶν λόγῳ καὶ ἔργῳ,
19 mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu.
ἐν δυνάμει σημείων καὶ τεράτων, ἐν δυνάμει Πνεύματος Θεοῦ, ὥστε με ἀπὸ Ἱερουσαλὴμ καὶ κύκλῳ μέχρι τοῦ Ἰλλυρικοῦ πεπληρωκέναι τὸ εὐαγγέλιον τοῦ Χριστοῦ,
20 Chakhala chilakolako changa nthawi zonse kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kumene Khristu sadziwika, kuti ine ndisamange pa maziko a wina wake.
οὕτω δὲ φιλοτιμούμενον εὐαγγελίζεσθαι οὐχ ὅπου ὠνομάσθη Χριστός, ἵνα μὴ ἐπ᾽ ἀλλότριον θεμέλιον οἰκοδομῶ,
21 Koma monga kwalembedwa kuti, “Iwo amene sanawuzidwe za Iye adzaona, ndi iwo amene sanamve adzazindikira.”
ἀλλὰ καθὼς γέγραπται, οἷς οὐκ ἀνηγγέλη περὶ αὐτοῦ ὄψονται, καὶ οἳ οὐκ ἀκηκόασι συνήσουσι.
22 Ichi nʼchifukwa chake ine ndakhala ndikuletsedwa kawirikawiri kubwera kwa inu.
Διὸ καὶ ἐνεκοπτόμην τὰ πολλὰ τοῦ ἐλθεῖν πρὸς ὑμᾶς·
23 Koma tsopano popeza kulibenso malo anga woti ndigwire ntchito mʼmadera awa, ndakhala ndikufuna kukuonani kwa zaka zambiri.
νυνὶ δὲ μηκέτι τόπον ἔχων ἐν τοῖς κλίμασι τούτοις, ἐπιποθίαν δὲ ἔχων τοῦ ἐλθεῖν πρὸς ὑμᾶς ἀπὸ πολλῶν ἐτῶν,
24 Ine ndikukonza kuti nditero pamene ndipita ku Spaniya. Ine ndikuyembekeza kudzakuchezerani pamene ndikudutsa ndi kuti inu mudzathandize popitiriza ulendo wanga, nditasangalala ndi kukhala nanu kwa kanthawi.
ὡς ἐὰν πορεύωμαι εἰς τὴν Σπανίαν, ἐλεύσομαι πρὸς ὑμᾶς· ἐλπίζω γὰρ διαπορευόμενος θεάσασθαι ὑμᾶς καὶ ὑφ᾽ ὑμῶν προπεμφθῆναι ἐκεῖ, ἐὰν ὑμῶν πρῶτον ἀπὸ μέρους ἐμπλησθῶ.
25 Koma tsopano, ine ndili pa ulendo wopita ku Yerusalemu potumikira oyera mtima akumeneko.
νυνὶ δὲ πορεύομαι εἰς Ἱερουσαλὴμ διακονῶν τοῖς ἁγίοις.
26 Pakuti kunakomera a ku Makedoniya ndi a ku Akaya kupereka thandizo kwa osauka pakati pa oyera mtima mu Yerusalemu.
εὐδόκησαν γὰρ Μακεδονία καὶ Ἀχαΐα κοινωνίαν τινὰ ποιήσασθαι εἰς τοὺς πτωχοὺς τῶν ἁγίων τῶν ἐν Ἱερουσαλήμ.
27 Iwo chinawakomera kuchita ichi, ndipo ndithu anali ndi ngongole kwa iwo. Pakuti ngati a mitundu ina anagawana ndi Ayuda madalitso auzimu, iwo ali ndi ngongole kwa Ayuda kuti agawane nawo madalitso awo a ku thupi.
εὐδόκησαν γὰρ καὶ ὀφειλέται αὐτῶν εἰσιν· εἰ γὰρ τοῖς πνευματικοῖς αὐτῶν ἐκοινώνησαν τὰ ἔθνη, ὀφείλουσι καὶ ἐν τοῖς σαρκικοῖς λειτουργῆσαι αὐτοῖς.
28 Tsono ine nditamaliza ntchito iyi ndi kutsimikiza kuti alandira chipatsochi, ndidzadzera kwanuko kudzakuchezerani pa ulendo wanga popita ku Spaniya.
τοῦτο οὖν ἐπιτελέσας, καὶ σφραγισάμενος αὐτοῖς τὸν καρπὸν τοῦτον, ἀπελεύσομαι δι᾽ ὑμῶν εἰς τὴν Σπανίαν.
29 Ine ndikudziwa kuti pamene ndidzabwera kwa inu, ndidzafika ndili wodzaza ndi madalitso a Khristu.
οἶδα δὲ ὅτι ἐρχόμενος πρὸς ὑμᾶς ἐν πληρώματι εὐλογίας τοῦ εὐαγγελίου τοῦ Χριστοῦ ἐλεύσομαι.
30 Abale, ine ndikukupemphani, mwa Ambuye athu Yesu Khristu ndi mwachikondi cha Mzimu, kuti mukhale nane pa kulimbika kwanga pondipempherera kwa Mulungu.
Παρακαλῶ δὲ ὑμᾶς, ἀδελφοί, διὰ τοῦ Κυρίου ἡμῶν Ἰησοῦ Χριστοῦ καὶ διὰ τῆς ἀγάπης τοῦ Πνεύματος, συναγωνίσασθαί μοι ἐν ταῖς προσευχαῖς ὑπὲρ ἐμοῦ πρὸς τὸν Θεόν,
31 Pempherani kuti ine ndilanditsidwe kwa osakhulupirira a ku Yudeya ndi kuti utumiki wanga mu Yerusalemu ukhale ovomerezeka ndi oyera mtima.
ἵνα ῥυσθῶ ἀπὸ τῶν ἀπειθούντων ἐν τῇ Ἰουδαίᾳ καὶ ἵνα ἡ διακονία μου ἡ εἰς Ἱερουσαλὴμ εὐπρόσδεκτος γένηται τοῖς ἁγίοις,
32 Kuti mwachifuniro cha Mulungu ndibwere kwa inu ndi chimwemwe kuti ndidzapumule pamodzi ndi inu.
ἵνα ἐν χαρᾷ ἔλθω πρὸς ὑμᾶς διὰ θελήματος Θεοῦ καὶ συναναπαύσωμαι ὑμῖν.
33 Mulungu wamtendere akhale ndi inu nonse. Ameni.
ὁ δὲ Θεὸς τῆς εἰρήνης μετὰ πάντων ὑμῶν· ἀμήν.

< Aroma 15 >